16/06/2026
*MAWU ACHITSITSIMUTSO*
๐ฑ:+2717779344
Wasap group ya: https://chat.whatsapp.com/EMlVuEpJOjyIRBzi7OkrOJ
*MUTU: TIYANG'ANEBE CHITSOGOLO*
Chifuniro cha Mulungu pa ife ndichoti tipite chitsogolo ndinso kusintha m'moyo. Sikufuna Kwake kuti ana Ake atitimire kapena kubwelera m'mbuyo m'moyo. Ndizosadabwitsa kuona mau Ake akunena kuti:
Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, Kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe. Miyambo 4:18
Umenewo ukhala umboni wanu kuyambira lero, mu dzina la mphamvu la Yesu! Mudzawalabe ndikupita chitsogolo m'magawo onse a moyo wanu, mu dzina la mphamvu la Yesu!
Ndichifukwa chake ndikukulimbikitsani kuti muyang'ane chitsogolo nthawi zonse. Musalore kulephera kapena zokhumudwitsa zam'mbuyo kuti zikukokereni pansi. Dzulo lapita ndipo chimene muli nacho inu pano ndi Lero, Kotero, ligwiritseni tchito lero lanu mwaphindu. Musalore zokhumudwitsa zam'mbuyo ziononge chimene muli pakanali pano. Mulungu akunena kuti:
Musakumbukire zidapitazo, ngakhale kulingalira zinthu zakale. Taonani, ine ndidzachita chinthu chatsopano; tsopano chidzaoneka; kodi simudzachidziwa? Ndidzakonzadi njira m'chipululu, ndi mitsinje m'zidalala. Yesaya 43:18-19
Wokondedwa, chifukwa choti muli moyo kuwerenga phunziloli, ndi umboni wokwanira woti danga likadalipo. Aliko masiku abwino kutsogolo kwanu, Kotero, yang'anani chitsogolo. Mulungu ali nanu kukakusungani, kukugwirani dzanja ndi kukumenyerani nkhondo. Mukwaniritsa mu dzina la mphamvu la Yesu!
*Pemphero Lanu Lero*
Lero ndikulandira chisomo, mphamvu ndi nyonga zoyang'ana chitsogolo mwa chikhulupiriro ndi kulimbika mtima, kusatengera nyengo zondizungulira, mu dzina la mphamvu la Yesu!
MUKHALE NDI TSIKU LODALITSIKA ๐