Ikraa Muslim Youth Dawah Group

Ikraa Muslim Youth Dawah Group Indeed the only true religion in the sight of Allah is Islam; those who had received the Books differed only after the knowledge came to them,...

Indeed the only true religion in the sight of Allah is Islam; those who had received the Books differed only after the knowledge came to them, due to their hearts’ envy; and whoever disbelieves in the signs of Allah, then Allah is Swift At Taking Account.
[A/I`mran 3:19]

04/04/2020

Asalam alayikum

29/03/2020

KODI CHISILAMU CHIDAYAMBA BWANJI?
Chisilamu sadayambitse Muhammad pbuh
[
Mwawerenga apa👆🏽👆🏽 chisilamu ndichipembedzo cha Noah. Abraham.moses mpaka Yesu
Chisilamu kuthanthauza kugonjera mwa Mulungu.
[ Muhammad pbuh ndi ntumiki wa chisilamu amene adagwira ntchito yaikulu kuchifalitsa molimba ku mitundu yonse. Chifukwa iye adatumizidwa ku anthu omwe sadawafikire atumiki .
[ Nde kwa anthu amenewo chisilamucho kudali kuyamba kuchimva. Chidali chiyambi chawo. Sikuti chisilamucho chidayambira pamenepo ayi. Koma kwa mitundi imeneyo chidali chiyambi
[
Monga kuwauza anthu kuti Mulungu ndi mmodzi . Moses adaphunzitsa kale zimenezo. Deautronomy 6:4
4. Imvani, Israyeli; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi;(Deuteronomo 6:4)
Muzipereka Zakaah chopereka.
21. Ndipo Yesu anamyang'ana, namkonda, nati kwa iye, Cinthu cimodzi cikusowa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo cuma udzakhala naco m'mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.(Marko 10:21).
Kuyang'anira ana amasiye.
27. Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndiwo: z kuceza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'cisautso cao, ndi 1 kudzisungira mwini wosacitidwa mawanga ndi dziko lapansi.(Yakobo 1:27)
Muzisala chakudya. Mwezi wa number 9.
Izo zidaphunzisidwa kalenso👇.
9. Ndipo panali caka cacisanu ca Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mwezi wacisanu ndi cinai, anthu onse a m'Yerusalemu, ndi anthu onse ocokera m'midziya Yuda kudzaku Yerusalemu, analalikira kusala kudya pamaso pa Yehova.(Yeremiya 36:9).
Kupita ku Mecca zidalamulidwa kalenso
6. Gulu la ngamila lidzakukuta, ngamila zazing'ono za Midyani ndi Efa; iwo onsewo adzacokera ku Seba adzabwera nazo golidi ndi zonunkhira; ndipo adzalalikira matamando a Yehova.(Yesaya 60:6)
7. Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebaioti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa pa guwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.(Yesaya 60:7)
Kedara ,Naboaiti.Efa onse atchulidwa kuti azasonkhana ku guwa la nsembeli pamepa👆🏽👆🏽ndi ana A Ishmael. Komwe kudachokera mtumiki muhammad. Pbuh.
13. ndipo maina a ana a Ismayeli, maina ao m'mibadwo yao ndi awa: woyamba wa Ismayeli ndi Nebayoti; ndi Kedara, ndi Abideele, ndi Mibisamu,(Genesis 25:13)
Ndipo Seba ndi Yemeni.
Mwachidule akuti anthu adzakasonkhana ku guwa la nsembe.
Kodi ndikutiko komwe anthu amakasonkhana lero lino kupatula ku Mecca?
2. Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.(Yesaya 2:2)
[
chisilamu nchakale. Ndipo zimene amaphunzitsa muhammad pbuh zidali zomwezo adaphunzitsa aneneri akale.
[
Azimayi kufunda kumutu.
👇👇.
5. Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wobvula mutu, anyoza mutu wace; pakuti kuli cimodzimodzi kumetedwa.(1 Akorinto 11:5)
6. Pakuti ngati mkazi sapfunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kucititsa manyazi, apfunde,(1 Akorinto 11:6).
Munthu akazilotera olo akagona ndi mkazi wake akasambe👇👇👇.
16. Ndipo munthu ali yense akagona uipa, azisamba thupi lace lonse ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.(Levitiko 15:16)
18. Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.(Levitiko 15:18).
Akazi kukhala chete mumzikiti👇👇👇.
34. Akazi akhale cete m'Mipingo. Pakuti vsikuloledwa kwa iwo kulankhula, Koma akhale omvera, mongansocilamulo cmena,(1 Akorinto 14:34).
35. Koma ngati afuna kuphunzirakanthu afunseamuna ao aiwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo.(1 Akorinto 14:35).
11. Mkazi aphunzire akhale wacete m'kumvera konse.(1 Timoteo 2:11)
12. Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale cete.(1 Timoteo 2:12)
[
Nde mukawerenga pamenepa mupeza kuti👆🏽👆🏽mfundo zambiri za chisilamu zomwe muhammad amalalikira . Zidabwera kale iye amangobwereza ku anthu achilendo omwe sankaziwa.
Ndizochepa zomwe muhammad adaphunzitsa zomwe nzachilendo.
Koma zambiri ndi zakale.
Monga.
Kusambitsa ziwalo.ekisodo 40:30-31
Kuyang'ana ku kachisi popemphera. Masalimo 138:2.
2. Ndidzagwadira kuloza ku Kacisi wanu woyera,
Ndi kuyamika dzina lanu,
Cifukwa ca cifundo canu ndi coonadi canu;
Popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.(Masalmo 138:2).
Kugwetsa nkhope pansi.
Mateyu 26:39.
Taonaninso angelo👇.
11. Ndipo angelo onse anaimirira pozinga mpando wacifumu, ndi akulu, ndi zamoyozo zinai; ndipo anagwa nkhope yao pansi ku mpando wacifumu, nalambifa Mulungu,(Cibvumbulutso 7:11).
[
Nde chisilamu ndichipembedzo cha Atumiki onse.
Ndipo adayambitsa chisilamu ndi mulungu mwiniwake.
Ndime yochoka m'qur'aan: Suurat As-Shuura (42:13)
شَرَعَ لَكُم مِّنَ الدِّينِ مَا وَصَّىٰ بِهِ نُوحًا وَالَّذِي أَوْحَيْنَا إِلَيْكَ وَمَا وَصَّيْنَا بِهِ إِبْرَاهِيمَ وَمُوسَىٰ وَعِيسَىٰ ۖ أَنْ أَقِيمُوا الدِّينَ وَلَا تَتَفَرَّقُوا فِيهِ ۚ كَبُرَ عَلَى الْمُشْرِكِينَ مَا تَدْعُوهُمْ إِلَيْهِ ۚ اللَّهُ يَجْتَبِي إِلَيْهِ مَن يَشَاءُ وَيَهْدِي إِلَيْهِ مَن يُنِيبُ ﴿١٣﴾
13. Wakhazikitsa kwa inu chipembedzo Chonga chomwe adam'langiza Nuhi. Ndipo chimene takuvumbulutsira iwe Ndi chimenenso tidavumbulutsira Ibrahim, Musa, ndi Isa kuti: Mulimbike Chipembedzo (potsatira Malamulo) ndikuti musalekane pa Chipembedzo. Koma ndizovuta kwa Opembedza mafano (kuvomera) Zimene ukuwaitanira. Mulungu Amadzisankhira amene wam'funa ndipo Amamuongolera amene Akutembenukira kwa lye.
Via Qur'aanM'chichewa...

16/01/2019
01/01/2019

*📢MSONKHANO!! MSONKHANO!! 📢*

Asalaam Aleikum Warahamatulaah Wabarakatuh

Kwa Nthawi yoyamba Mukuitanidwa Ku Msonkhano wa ukulu omwe ukutchedwa kuti (Chichewa Dawah Conference) omwe uchitike mmwezi uno wa January :

*DATE/TSIKU*
_____________________
Sunday (Lasabata)
27 January 2019

*NTHAWI*
_____________________
Kuyambira 10:00 AM mpakana 3:00 PM

*MALO OPANGILA MSONKHANO*
_____________________
Pamzikiti waukulu mu Town ya Durban
*Grey Street Musjid (Jumah Musjid* )

*OLALIKILA NDI:*
_____________________
1.Sh Saleem Banda (Dbn)
2.Sh Abubakar Mtenje (Dbn)
3.Sh Habeeb Milanzi (Dbn)
4.Sheikh Ismail Mtewa (Dbn)
5.Sh Amani Said (Jhb)
6.Sh Abdul Wahid Qassim (Jhb)
7.Sh Abdul Rasheed (Jhb)
8.Qari Idrisa Rajab (Dbn)

*CHOLINGA CHA MSONKHANOWU*
_____________________
Kulumikizanitsa (kuyanjanitsa) pakati pa amalawi ndi ma south African monga ummah umodzi ndi kuwayandikitsa pafupi ndi Mulungu wawo.

*DZIYANKHULO DZOMWE DZIKAGWIRITSIDWE NTCHITO:*
_____________________
1.English
2.Chichewa
3.Yao

*CHAKUDYA*
_____________________
Chakudya chidzaperekdewa mwa ulere

*CHIPINDA CHA AMAYI/ATSIKANA*
_____________________
Chipinda cha amayi ndi atsikana chidzakhalapo

*Bwerani nonse mwa unyinji !!!*

Mukafuna kudziwa zambiri. Imbani pa manambala a:
*AMENE AKONZA MSOKHANOWU* :
_____________________
1.Sheikh Jaafar Magombo
(0787711019)
2.Sheikh Suwed Stephen
(0748104019)
4.Sheikh Habeeb Thabit
(0843136207)
5.Muazin Ibrahim Fakson
(0717875883)

*MOTHANDIZIDWA NDI*:
▪Imam Development Project.
▪Islamic Propogation Centre International.
▪Muadhin Development Programme.

📢 *ANNOUNCEMENT*  📢 Asalaam Aleikum Warahamatulaah Wabarakatuh*You are invited to the 1st Chichewa Dawah Conference**DAY...
31/12/2018

📢 *ANNOUNCEMENT* 📢

Asalaam Aleikum Warahamatulaah Wabarakatuh

*You are invited to the 1st Chichewa Dawah Conference*

*DAY/DATE:*
Sunday
27 January 2019

*TIME:*
10:00AM to 3:00 PM

*VENUE:*:
Grey Street Jumuah Musjid, Durban

*SPEAKERS:*
1.Sh Saleem Banda (Dbn)
2.Sh Abubakar Mtenje (Dbn)
3.Sh Habeeb Milanzi (Dbn)
4.Sheikh Ismail Mtewa (Dbn)
5.Sh Amani Saidi(Jhb)
6.Sh Abdul Wahid Qassim (Jhb)
7.Sh Abdul Rasheed (Jhb)
8.Qari Idrisa Rajab (Dbn)

*AIM AND OBJECTIVE:*
To foster unity between the Malawian South African community by bringing people closer to their Creator.

*LANGUAGES TO BE USED:*
1.English
2.Chichewa
3.Yao

*LUNCH:*
Lunch will be served

*LADIES FACILITY:*
Ladies Facility will be available.

*Come one, come all !!!*

For further details contact:
*ORGANISERS:*

1.Sheikh Jaafar Magombo
(0787711019)
2.Sheikh Suwed Stephen
(0748104019)
4.Sheikh Habeeb Thabit
(0843136207)
5.Muazin Ibrahim Fakson
(0717875883)

*Powered by:*
▪Imam Development Project.
▪Islamic Propogation Centre International.
▪Muadhin Development Programme.

08/06/2017

Asalam alaykum brothers & sisters. I need anyone who can give us every times every day messages in this page. I need 5 people so comment this message I will come to ur in box, I give u all details for this page to be the owners

Address

Abertina Sizulu And Vonwel
Johannesburg
ISLAM

Telephone

+27624006590

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Ikraa Muslim Youth Dawah Group posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share