Hermanus Grace Of God Living Church GGLC

Hermanus Grace Of God Living Church GGLC The Grace of God Living Church has a defining focus on legalism.

The Grace of God Living Church believes that they are the β€œtrue Church of God that stands apart from this religious Babylon,” meaning all other Christian denominations.

02/04/2026

*TAWAUZAN ADANI ANUWO KT ZOMWE MUKUNENA ZOKHUDZA INEYO SIZITHEKA AKUTERO YEHOVA πŸ™πŸ½πŸ’ͺ🏽πŸ’ͺ🏽*
Yesaya : 7 : 4-74. Ukamuwuze kuti, β€˜Chenjera, khala phee ndipo usaope. Usataye mtima chifukwa cha zitsa ziwiri zomwe zikufuka, chifukwa cha ukali woopsa wa Rezini ndi Siriya, ndiponso wa Peka mwana wa Remaliya.7. Komabe zimene akunena Ambuye Yehova ndi izi: β€œ β€˜Zimenezo sizidzatheka, sizidzachitika konse,
*Hallelujah πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ™ŒπŸ½!!Munauzidwapo inu kt musavutike ai mawa simufika,kmaso iiiii!!! Akt atan akapambana andifuse ndye munthu wake siineyo ai,Apita ku ma interview!? Akabwererako palibe comwe angakapange,Kd inu or anawo angakhale ndi amene aja Hehehede iri πŸ˜‚,Mwava kd ati apeza mamunatu likakhala banja mudzandifuse,!!Iyi imakhala nyengo omwe adan afika polepheretsa ciriconse cako ndipo bas iweyo kukhala pa zero,Indeee azibale anga akt or Naye Ahazi inafika nthaw iyi,omwe Yerusalemu anazunguliridwa kt athiridwe nkhondo,Kma Yesaya ndkut pa nthaw iyi atapangidwa kukhala m'neneri ndipo akutumidwa kupita kukakumana ndi Ahazi,ndkukamuuza zomwe Yehova akunena zokhudza adan ake,Abale anga tisadere nkhawa ai,tisaope ai,tisagwedezeke ai,auzen anebawo kt Mulungu akt zomwe mukuganizazo zokhudza ine sizitheka ai ndipo Yesaya 54:16,17,Kmaso Eksodo 14:14,Eksodo 15:3,Wauza ine lero ndipo adani anga sandipambana ai πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ’ͺ🏽πŸ’ͺ🏽πŸ’ͺ🏽πŸ’ͺ🏽*

02/04/2026

*TIYENI TIGWIRITSITSENI CABWINONO-CO OR ENA ANENE ZOIPA ZA ICO πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ™ŒπŸ½*
Romans : 14 : 16-17.Musalole kuti chimene muchiyesa chabwino achinene ngati choyipa.17. Pakuti Ufumu wa Mulungu si nkhani yakudya ndi kumwa, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.
*Hallelujah πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ™ŒπŸ½!!Tiripo ena masiku ano tinasiya kupemphera cifukwa ca maganizo a anthu ena,Ena analipo otiuza kt aaaaa!! Kd inuso ku church kwa daily daily muzikataniko,or Bible limat muzipita daily,Ndipo izi tinazivera ndkusiya kupita ku church daily,Masalimo 122:1,Davide anat anasangalala atati tiye ku nyumba a Atate,Kmaso Davide emweyi pa Masalimo 37:10 Anat cinthu cinodzi comwe ndicikonda ndico kupezeka nyumba a Atate,Tiripo ena amene timakakamizidwa kunena bodza pakt ena akt titero,Mukawerenga Numeri 22:18Nkhan a Baalamu ndi Balaki, Akt Baalamu anati or atandipasa nyumba odzaza ndi golide kmaso silva kma sindingacite ciriconse cacikulu or cacing'ono kuposa comwe Mulungu wanena,Indeee azibale anga tiyen tigwiritsitsen cilungamo nthaw zonse ndipo tikatero or enewa adzasowa mpata oticitira coipa or kutineneza bodza πŸ™ŒπŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½*

02/04/2026

*KD INUYO MISSION ANU NDIOTAN πŸ€·πŸ½β€β™‚οΈπŸ€·πŸ½β€β™‚οΈπŸ€·πŸ½β€β™‚οΈ*
Mateyu 20:28 CCL
[28] Momwenso Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kukhala dipo la anthu ambiri.”
*Hallelujah πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ™ŒπŸ½!!Aliyese akamapanga zinthu amakhala ndi colinga,ndipo amayesetsa kt colinga cakeco citheke,Citsanzo ndiri ku South Africa,colinga canga ndkt ndipeze ndalama a business kmaso ndimange nyumba,ena ali kuno kt adzamwe mowa kmaso kukwatira akaz akuno,ena agule galimoto kt akapangire business, enaso anabwera kudzangoonako south africa,Kd nanga inuyo mission anu a umzimu ndiotan!? Ambiri masiku ano akusangalala akamat Atsogoleri, Abusa,Abishop or atumiki kma or ziri conco iwowo mission ao akungofuna kukwaniritsa lemba la Mateyu 23 Lija,ndipo colinga cao ndkupeza phindu mu mΚΌdzina la Ubusa kapena Atsogoleri, enaso akufuna apeze ulemu ndkulambiridwa momo,Yesu Khristu akt sindinabwere pano kudzatumikiridwa kma kudzatumikira,Pamene inuyo pakt akt ndinu abusa mukufuna kutumikiridwa,Ai,Pa Mateyu 28,Yesu Khristu anakupasan ntchito,ntchito ake ndiyo kukalalikira za uthenga wabwino ndkuwabatiza anthu mu mdzina la Atate,Mwana ndi Mzimu,Kd inuyo mission anu ndiotan!? Indeee tikhale osamala pakt tikacita cibwana paja si onse amene amat Ambuye Ambuye akalowe mu umfumu wakumwamba Mateyu 7:21 πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ™ŒπŸ½*

Address

LANDLERA Street
Hermanus
7200

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Hermanus Grace Of God Living Church GGLC posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Place Of Worship

Send a message to Hermanus Grace Of God Living Church GGLC:

Shortcuts

Share