Islamic strength's

Islamic strength's Qur'an recitation, Hadith lessons,Teachings from scholars, Fiqih and Islamic advice

07/09/2026

People will always criticize you!
Don't please them rather please your Lord(Allah).
You can never be a good person spiritually without being criticized Kuti ndinu olephera, a time waster,iwowa Kodi akapulumuka? akufuna awoneke ngati ndani? amadzinva ungelo.
Accept to be a failure in their world, be a super star, ,clever and brave by spending your time in pleasing allah.

06/09/2026

ALLAH ADALITSE ALIYENSE AMENE WALIYAMBA TSIKU NDI SWALAH YA FAJIR AMEEN

27/07/2026

UMMU SULYIM رضي الله عنها
Kodi mudanvapo za nkhani yakeyi??
Islamic strength's
Aakhir zamaan TV

NKHANI YA SWAHAABIYAH UMMU SULYIM (SWAHABAH WACHIKAZI).Dzina lake ndi Sulyim mwana wa Milhaana Allah asangalare nawo och...
22/07/2026

NKHANI YA SWAHAABIYAH UMMU SULYIM (SWAHABAH WACHIKAZI).

Dzina lake ndi Sulyim mwana wa Milhaana Allah asangalare nawo ochokera ku mtundu uja wama An'swaar aku Madinah. Ndipo ndimayi ake aswahabah odziwika bwino Hazrat Anasi Bin Malick, Allah asangalare naye yemwe adagwila ntchito kwazaka zochuluka kutumikira mtumiki wathu Muahammad madalitse a Allah akhale pa iye.

BANJA LAKE ASADALOWE CHISILAMU

Ummu Sulyim adakwatira ndi Mzibambo otchedwa Malick Bin Nadwar, ndipo awiri onse adali ma kufaar (okanira mwa Allah). Banja lawo adabelekerana mwana otchedwa Anasi. Pambuyo poti chislamu chafika ku Madina iyeyu adalowa chislamu ndikuyamba kumamuphunzitsa Anasi umoyo wachislamu, zomwe zidapangitsa kuti mamuna wake Malick akwiye ndikusamukira ku Syria komwe adakakhala mpaka kumwalilira konko.uku kudali kusiyana kwa banja pakati pa Ummu sulyim ndi Malick bin Nadhwar.

KUKWATIRA KWAKE NDI ABU- TALHAH

Pambuyo poti wathawidwa ndi mamuna awo Ummu Sulyim kamba kolowa chislamu, kudabwera mamuna okafunsira banja yemwe ndi Abu Talhah yemwe adalinso Kaafir. Ndipo atafunsira banja adamuyankha kunena kuti; Ohh Abu Talhah mamuna ngati inuyo sioti mungakanidwe banja ayi!! Komano vuto ndiloti iweyo ndi kaafir ndipo ine ndi msilamu. Pachifukwa chimenechi ngati ungalowe chisilamu basi ine ndidzakupanga kulowa chisilamu kwako kukhala Mahar yoti undikwatilire. Pambuyo pake zidapezeka kuti Abu Talhah adalowa chislam ndipo Mahar yake idali kulowa chislam ko yomwe adapezera banja ndi Ummu Sulyim Allah asangalale naye.

Adalankhula swahabah olemekeza Al Bunaaniyyu kunena kuti; Ndithudi sitidanvepo mahar yopambana ife mu umoyo wathu kuponsa Mahar yomwe adapatsidwa Ummu Sulyim ndi Abu Talhah.

Talingalirani kulora kusiyana ndi mamuna wake chifukwa chakumuopa Allah ndikusankha kupanga chifuniro chake chomwe ndi chislamu? Talingalirani kusafuna kalikonse kuchokera muchuma kuti apatsidwe ngati chiwongo kupatula kusankha kuutenga ngt mwayi oti apeze thawaabu kuchokera kwa Allah pakulowa chislamu kwa mamuna wake!

Ndi angati mwa ife omwe tikadatha kupanga chisankho ngati chomwe adapanga Ummu sulyim Allah asangalare naye?

Kodi mudanvapo nkhani ya swahabiyaah (a woman companion) wotchedwa ummu sulyim?get ready don't miss out as we will be dr...
17/07/2026

Kodi mudanvapo nkhani ya swahabiyaah (a woman companion) wotchedwa ummu sulyim?
get ready don't miss out as we will be dropping soon
Islamic strength's

Shaytwaan amadzera mwa azikazi akafuna kukokera mamuna ku uchimo choncho tiyeni tipewe kukhala ndi azizathu omwe tingath...
06/07/2026

Shaytwaan amadzera mwa azikazi akafuna kukokera mamuna ku uchimo choncho tiyeni tipewe kukhala ndi azizathu omwe tingathe kuwakwatira
Islamic strength's

26/05/2026

A Lesson from Hazrat Ibrahim Aalayih salaam

20/05/2026

CHIFUKWA CHIYANI TIMAPHA NYAMA YOPEREKA NSEMBE

Kodi bambo angakwanitse bwanji kukweza mpeni pa mwana wake yekha? Yankho lili pa cholinga cha Eid al-Adha ndi tanthauzo lenileni la kupereka nsembe.

Nkhani ya Mneneri Ibrahim عليه السلام ndi mwana wake Ismail عليه السلام si mbiri chabe. Ndi maziko a Qurban ndi phunziro la kudzipereka lomwe mibadwo yonse iyenera kukumbukira.

Mayeso Omwe Anayamba ndi Maloto

Ibrahim عليه السلام anadalitsidwa ndi mwana, Ismail, atapemphera kwa zaka zambiri. Koma Allah amayesa omwe Iye amawakonda kwambiri.

Usiku wina, Ibrahim analota kuti akupha mwana wake. Kwa mneneri, maloto ndi vumbulutso lochokera kwa Allah.

قَالَ يَا بُنَيَّ إِنِّي أَرَىٰ فِي الْمَنَامِ أَنِّي أَذْبَحُكَ فَانظُرْ مَاذَا تَرَىٰ
_“O mwana wanga, ndalota kuti ndikuzinge monga nsembe yopereka kwa Mulungu, iwe ukuganiza bwanji.”_ [Surah As-Saaffat 37:102]

Ibrahim sanabisire lamuloli. Anauza mwana wake momasuka ndi kufunsa maganizo ake.

Yankho la Ismail: Pamwamba pa Kudzipereka

Ismail anali wokhwima mokwanira kumvetsetsa kulemera kwa lamuloli. Yankho lake linakhala chitsanzo chosatha cha chikhulupiriro.

قَالَ يَا أَبَتِ افْعَلْ مَا تُؤْمَرُ ۖ سَتَجِدُنِي إِن شَاءَ اللَّهُ مِنَ الصَّابِرِينَ
_“O bambo anga, chitan zomwe mwalamulidwa, ngati Allah afuna, mudzandipeza mgulu la anthu opilira”_ [Surah As-Saaffat 37:102]

Onse awiri bambo ndi mwana anadzipereka kwathunthu. Ibrahim anagoneka Ismail chafupi ndi pansi kuti akwaniritse lamulo popanda kukayika.

فَلَمَّا أَسْلَمَا وَتَلَّهُ لِلْجَبِينِ
_“Ndipo pamene onse awiri anadzipereka, ndipo anamugoneka pachifuwa.”_ [Surah As-Saaffat 37:103]

Pa nthawi imeneyo ya kudzipereka kwathunthu, Allah analowererapo.

Kusintha kwa Chifuniro cha Allah

Allah sakanafuna kuti Ismail aphedwe. Mayeso anali okhudza kufuna ndi kumvera. Pomwe izi zinatsimikizika, Allah anasinthanitsa Ismail ndi nkhosa yaikulu.

وَفَدَيْنَاهُ بِذِبْحٍ عَظِيمٍ
_“Ndipo tinamuwombola ndi nsembe yaikulu.”_ [Surah As-Saaffat 37:107]

Check more in comment section

19/05/2026

Taswali koma Fajir yalero?or chidwi chathu chili pakukangana nkhani ya tsiku la Aarafah basi😢
Allah atichitire chisoni

15/05/2026

JUMMUA MUBARAK
MAY ALLAH ACCEPT OUR DUAS Islamic strength's

Address

Durban

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Islamic strength's posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share