18/12/2022
YOHANE (JOHN) 3 VS 16
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anatuma mwana wake obadwa yekha kuti yense wakukhulipilira our asataike, koma akhale nawo moyo osatha
🔹🔹🔹🔹🔹🔹🔹🔹🔹🔹🔹🔹🔹🔹🔹
Kodi okondedwa mukamakhala mimadziwa kuti Mulungu amakukondani? Nanga kodi mumadziwa kuti Yesu anafa chifukwa cha inu? Nanga mumakhulupilira kuti Yesu ndiye mpulumutsi wamoyo wanu?
Malemba akuti; ine ndine Njira ndi choonadi ndi moyo palibe munthu adza kwa Agate Loma mwa one ndekha.
Zachidziwikire kuti sitingakapeze moyo osatha ngati sitiyenda naye Yesu
Muloleni Yesu kuti akhale mbuye ndi mpulumutsi wa moyo wanu, mukatero mukhilupilire kuti anafa kamba ka inu, ndipo anadzuka ataikidwa mmanda kotero imfa sinakhalenso ndi mphamvu pa iye, ndiye ngati mukhulupilira iye simudzafai ndipo mudzakhala ndi moyo mpaka muyaya.
Chikhulupiliro ndiye gwero la moyo wosatha, tamkhulupilirani ndikuyamba kuyenda naye muon ngati sakucgitirani zazikulu pamoyo wanu. Tamuyesani muone zomwe amapanga.
Yesu ndiye yankho la chilichonse cha moyo wanu, bwerani chifupi ndi iye mukatero mudzapeza mtendere pa moyo wanu wa mtsiku ndi tsiku.
Mukhale ndi tsiku lopambana pamene mukupanga chisankho choyenda ndi Yesu. AMEN