06/09/2026
MAU A MULUNGU A LERO OWERENGEDWA PA 06 SEPTEMBER 2026 - LAMULUNGU - MAWU A M'BUKHU LA MNENERI EZEKIEL 33:7-9
“Tsono iwe mwana wa munthu, ndakuika kuti ukhale mlonda wa Aisraele. Ukamva mau anga, uŵachenjeze. Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Munthu woipa iwe, udzafa,’ iwe nupanda kumchenjeza kuti aleke makhalidwe oipa, kuti akhalebe ndi moyo, munthuyo adzafadi ali wochimwa, koma iweyo ndidzakuzenga mlandu chifukwa cha imfa yake. Koma munthu woipa ukamchenjeza kuti asiye njira zake zoipa, iye nkupitiriza makhalidwe ake oipawo, adzafa ali wochimwa, koma iweyo udzapulumutsa moyo wako.
Mau a Ambuye
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 95:1-2,6-7abc,7d-9
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu
Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye,
thanthwe lotipulumutsa.
Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze,
tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu
Bwerani, timpembedze ndi kumlambira.
Tiyeni tigwade pamaso pa Chauta Mlengi wathu.
Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ife
ndife anthu a pa busa lake,
ndife nkhosa zodyera m'manja mwake.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu
Lero mukadamverako mau ake!
Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja,
monganso tsiku lija ku Masa m'chipululu muja,
pamene makolo anu adandiputa mondiyesa ngakhale anali ataona ntchito zanga.
MAU ACHIWIRI A M'KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA 13:8-10
Musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena. Pajatu malamulo amene amati, “Usachite chigololo, usaphe, usabe, usasirire”, ndiponso malamulo ena onse, amaundidwa mkota m'lamulo ili lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.” Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Mau a Ambuye
Aleluya (1 Akor 5:19)
Ndiye kuti mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, osaŵaŵerengera machimo ao. Ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiŵalalike.
Aleluya
UTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYU WOYERA 18:15-20
“Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo. Koma akapanda kukumvera, utengerepo wina mmodzi kapena ena aŵiri, kuti mau onse akatsimikizike ndi mboni ziŵiri kapena zitatu. Akapanda kuŵamvera iwowo, ukauze Mpingo. Ndipo akapanda kumveranso ndi Mpingo womwe, umuyese munthu wakunja kapena wokhometsa msonkho. “Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mudzamanga pansi pano, chidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo chilichonse chimene mudzamasula pansi pano, chidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe. “Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani. Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”
Uthenga wa Ambuye