03/01/2025
Lipoti la momwe utumiki wa chinyamata m'boma la Zomba wayendera mu Chaka Cha 2024.
Utumiki wa chinyamata m'boma la Zomba unakhazikitsa zochitika zikuluzikulu zitatu. Zochitikazi ndi monga izi;
1. Kuthandiza ophunzira mu Sukulu zapulaimale.
2. Maphunziro amasiku atatu.
3. Ulendo waku Cape Maclear.
Chochitika choyamba mu chaka Cha 2024, chinali kuthandiza ophunzira apa Sukulu ya namisunju yomwe ili kwa Jali m'boma la Zomba. Ophunzira opitilira 1000 analandira thandizo monga;
-Makope
- Zolembera
- mipando ( Mabetchi)
- Zodzisamalira atsikana Nthaw ya msambo (sanitary pads).
Utumiki wachinyamata ukuthokoza kwambiri kwa onse omwe anatenga gawo kupeleka thandizo lachuma kapena katundu amene amafunika ku ntchitoyi. Ena mwa anthuwa anali oti samasonkhana mu mpingo wa Khristu koma anadzichepetsa kupeleka thandizo lopita ku ntchito imeneyi.
Chochitika chachiwiri unali msonkhano umene unachitika mu mwezi wa August kuchingale. Msonkhano umenewu unali wamasiku atatu ndipo mutu wake unali " UMODZI UMENE AMBUYE YESU KHRISTU ADAUPEMPHERERA.
Achinyamata oposa 250 kuchokera mmagome oposa 30 ndiwo anabwera ku msonkhanowu.
Chochitika chomaliza unali msonkhano umene unachitika kuyambira pa 29 November ndipo unatha pa 1 December 2024. Msonkhano umenewu unali wamasiku atatu ndipo unachitikira pa Sukulu yapulaimale ya Cape Maclear ku mangochi.
Maphunziro anali apamwamba kwambiri pamene aphunzitsi athu achitsulo kuchokera ku ntaja, komanso a G Phiri kuchokera ku mangochi anaphunzitsa zozama kwambiri pa mutu onena kuti KUYENDA MOYENERA MAITANIDWE ATHU.
Achinyamata pafupipafup 300 ochokera ku Zomba komanso boma lamangochi anali nawo pa msonkhano umenewu. Mwa zina, msonkhanowu unakulitsa ubale pakati pa mipingo yaku mangochi ndi Zomba.
Zochitika zina zinali monga kukwera maboti, kusambira pa nyanja ndi zina. Izi zinapeleka chimwemwe chachikulu kwa achinyamata chifukwa ena kanali koyamba kubwera ku nyanja.
Mmalo mwa achinyamata onse ku Zomba, timafuna tithokoze kwambiri atsogoleri ampingo omwe amadzipeleka kuutumiki wachinyamata popeleka thandizo la ndalama, malangizo komanso ena amapezeka pa msonkhano.
Tithokoze kwambiri makolo amene amapeleka ndalama komanso chilolezo kwa achinyamata. Achinyamata eni ayeneranso kuthokozedwa chifukwa kupanga ganizo lopita ku msonkhano sichinthu chapafupi maka mmoyo uno pamene achinyamata akuyenda munyengo zovuta.
Chaka Cha 2024 Chinali chovuta kwambiri ku dziko la Malawi kumbali ya chuma. Izi zinadza chifukwa anthu sadakolole bwino kamba kamavuto odza chifukwa Cha namondwe. Chuma chikavuta mudziko, mpingo nawo umavutika kukwanitsa ma program amene akhazikitsidwa.
Ngakhale panali zovuta zonsezi, Mulungu wakhala okhulupilika ku utumiki wa chinyamata m'boma la Zomba pamene takwanitsa zochitika ZONSE.
Pamene 2024 wapita, tikuyang'ana chitsogolo kuti 2025 atibweretsera zotani.
Zina mwa zochitika chaka chino, achinyamata ndi atsogoleri ampingo adzakumana ku Chikamveka Church of Christ pa 15 komwe akudzasankha atsogoleri atsopano omwe ayendetse utumiki kwa zaka zomwe zikudzazi. Pa msonkhano umenewu mpamene padzaikidweso ndondomeko ya zochitika za 2025.
Tipemphera kuti Chaka chino Mulungu atipatse chuma choyendetsera zochitika zake. Tipemphera kuti Mulungu apeleke atsogoleri amasomphenya omwe adzapitiliza kuchita pamene komiti yakale yakhala ikuchita ndikubweranso zina zatsopano.