19/06/2022
*Rhapsody of Realities*
*By Pastor Chris*
*(Chichewa Version)*
*lamulungu 19, June 2022*
*MKWATULO SI NKHANI YABODZA*
Pakuti n'kanthawi kochepa chabe,
Iye amene akubwera adzabwera
ndipo sadzachedwa ayi!
*(Ahebri 10:37 CCL).*
Anthu ena amakhulupirira kuti Mkwatulo
wa Mpingo ndi chinyengo. Potsutsa
zamkwatulozi iwo amanena kuti mawu akuti
“mkwatulo” sapezeka paliponse m’Baibulo, ndipo
ngakhale Yesu sanalankhulepo zokhudza zimenezi.
Inde, pali zinthu zambiri zimene Yesu sanazifotokoze
kwambiri. Mwachitsanzo, ophunzira ake anali Naye
kwa zaka zochepa zimene Iye anatumikira padziko
lapansi, komabe iwo sankadziwa kanthu za kulandira
chipulumutso kwa Amitundu. Ngakhale adawaphunzitsa
zinthu zambiri, iwo sadapeze chilichonse chomwe
chidakawapangitsa kumvetsetsa bwino kuti Amitundu
adzabweretsedwa ku chipulumutso.
https://chat.whatsapp.com/GebTAZOadei6pJNA9apS61
Ndipo Petulo pamene adapita kunyumba ya
Korneliyo, Mkulu wa Kenturiyo wachiroma ophunzira
ena atamva zimenezi, sanasangalale naye. Iye
adawafotokozera zimene adakumana nazo ndi Mzimu
wa Mulungu, ndi zamomwe, mopanda chilolezo
chake (Petroyo), Mzimu Woyera anadza pa Amitundu
pamene iye anali kulankhula nawo. Kenako Yakobo
anatsegula Malemba ndi kupeza pamene aneneri
adanena kuti Amitundu adzapulumuka. Uwu unali
umboni wawo woyamba, kufikira pamene chinsinsi
komanso vumbulutso la thupi la Khristu zinaperekedwa
kwa Mtumwi Paulo.
Ndi momwemonso ndi Mkwatulo. Simungapeze
liwu lakuti “mkwatulo” m’ndime iriyonse chifukwa,
panthawi imene amalemba, Paulo analongosola kuti
mkwatulo ndi chinsinsi: “Taonani, ndikuuzani chinsinsi;
sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika.” (1
Akorinto 15:51) Pa 1 Atesalonika 4:17, Malemba amati,
‘tidzakwatulidwa”. Liwuli muchi Greek ndi “harpazo”
kutanthauza kulanda ndi kuchotsa. Matanthauziridwe
a Chilatini ndi “raptura”, amene m’Chichewa ndi
“mkwatulo”; kotero ndikulakwitsa kuti munthu anene
kuti mulibe mkwatulo m’Baibulo.
Koma musalole kuti wina aliyense akunamizeni,
Mkwatulo uchitika nthawi ina iliyonse posachedwapa.
Wayandikira kuposa kale. Zidzachitika
mofulumira kotero kuti iwo omwe sanakonzekere
ndikuwuyembekezera sadzakhala ndi nthawi
yokonzekera ndipo adzasiyidwa. Musadzakhale
inu osiyidwa. “…Khristunso ataperekedwa nsembe
kamodzi kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera
pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo
amene amlindirira, kufikira chipulumutso” (Ahebri
9:28).
*PEMPHERO*
Wokondedwa Atate, ndikukuthokozani chifukwa cha
mwayi wondiululira zozama zochokera m’Mawu
anu. Zikomo pondidziwitsa ine mwa Mzimu wanu
chenicheni cha Mkwatulo, ndikuti kwayandikira
kwambiri. Ndine odzipereka kukonzekeretsa anthu
ku mkwatulo, pamene ndikuyembekezera mwachidwi
kubweranso kwa Ambuye posachedwa. Amen.
*WERENGANINSO:*
2 Petro 3:3-4 NIV
1 Akorinto 15:51-52;
1 Atesalonika 4:15-18
*Ndondomeko Yowerenga Baibulo Chaka Chimodzi :*
*Ndondomeko Yowerenga Baibulo Zaka Ziwiri :*
Machitidwe 8:9-40 & 2 Mbiri 33-34
2 Akorinto 6:1-10 & Yesaya 5-6
For your loved ones who have *visual challenges*, those who have *difficult reading* and those who just *enjoying listening* to the Rhapsody Message, we now have the Rhapsody in *Audio format*, in the following languages, in our Groups :
*English, Xhosa, Shona, Ndebele, Setswana, Sesotho and Zulu.*
*PEMPHERO LA CHIPULUMUTSO*
Tikukhulupirira kuti mwadalitsika ndi bukuli. Ndipo tikukumemani kuti mumlandire yesu khristu kuti akhale mbuye wa moyo wanu popemphera pemphero ili:
*“Ambuye mulungu, ndi mtima wanga wonse, ndikukhulupilira mwa yesu khristu, mwana wa mulungu wamoyo. Ndikukhulupilira kuti iye adandifera ine ndipo mulungu adamuukitsa kwa akufa. ndikukhulupilira kuti iye ali ndi moyo lero. Ndikuvomereza ndi pakamwa panga kuti yesu khristu ndi ambuye a moyo wanga kuyambira lero. Kudzera mwa iye ndi mwa dzina lake, ndiri ndi moyo wosatha; ndabadwanso mwatsopano. Zikomo ambuye, populumutsa moyo wanga! ndine mwana wa mulungu tsopano. Halleluiah!”*
Mwachita bwino! Ndinu mwana wa mulungu tsopano.
..
*GREAT NEWS*
You can now receive the *Rhapsody of Realities Daily Devotional* messages, in your *mother tongue*, every morning on your phone or device, including *English Rhapsody* and *Teevo*
Currently we have the following *African Languages* available in our Groups (in Alphabetic Order):
*Afrikaans, Chichewa, Ndebele, Nyanja, Sesotho, Setswana, Shona, SiSwati, Xhosa, and Zulu*; and counting!
Also *invite* your friends, family and colleagues, to join the Group. Send them a copy of this Rhapsody, with the *JOIN the Group* Link.
*Click Here – to JOIN Our Groups*
https://chat.whatsapp.com/GebTAZOadei6pJNA9apS61
WhatsApp Group Invite