19/03/2026
Ine theka lamoyo wanga ndidakulira kuchikristu, kuchisilamu ndidalowa ndili zaka 18, komabe funso ili ndiyankha.
Fasting kuchislamu imayenda motere:
- You fast mutsiku (during the day, not night)
- A day in islam starts at sunset, (tsiku limayamba ndi pomwe dzuwa lalowa). Dzuwa likangolowa ndekuti layambika tsiku pamenepo, lidzatha dzuwa likadzatuluka nkulowa.
- koma kusala kudya kumayamba pomwe zizindikiro zakucha kwa tsiku zayamba kuwoneka, apano tikukamba za dzuwa (tsiku as Day, excluding night).
Kuno kwathu, especially ku Zomba tsiku likumayamba around 4:30a.m madera ena. Ndekuti Fasting imakhala from that time kufikira pomwe zizindikiro zakuda kwatsiku zayamba kuoneka, kuno kwathu munyengo ino it's around 6pm. Apa dzuwa limakhala kuti tatsimikiza kuti lalowa ndithu, makamaka munyengo inoyo.
- Izi it means Fasting ya asilamu imachitika kwambiri chigawo cha tsiku (DAY), osati usiku (night) ayi. Mmenemo ndi mmene chisilamu chilili, chilichonse chimayenda ndi lamulo lake ndithu, ndipo zili mmalemba ake achisilamu.
- Munthu kukhala osadya dzuwa litalowa, usiku wonse mpaka tsiku linalo kumati ukusala kudya, limenelo ndi tchimo, it means ukutsatira zina osati zachisilamu ayi. Fasting yachisilamu imakhala ndi break time, nthawi yake ndiyomwe dzuwa lalowayo ndithu. Kuyamba kwatsiku lina kumeneko.
- Kwa Mulungu wathu (ALLAH), Fasting sanayipange kukhala chilango kwa ife akapolo ake ayi, ndi chifukwa adatifewetsera nkutipatsa malamulo ofewa oterewa. Tidye dzuwa likalowa, tisadye dzuwa likakhala layamba kuonetsa zizindikiro zotuluka, mpakananso pomwe lalowa, basitu.
- Komano ambiri azipembezo zina amaona ngati asilamu amangosintha nthawi yodyera, kusiya masana, nkumadya usiku poona kuti asilamu pena amadzuka ndikumadya 3a.m, or 4a.m, tsiku litasala pang'ono kuyamba.
Eheeee, apa ndipomwe anthu simumapamvetsa ayi.
TAMVERANI
- chisilamu sichidabwere kudzakhala chipsinjo kwa anthu ayi. Potero chidaloleza kuti munthu utha kudya mugawo lausiku kufikira isadakwane nthawi ya pemphero lakummawa mumalimva lija.
Cholinga chakudya nthawi imeneyi sikupedza mkhuto ayi, chifukwa zikunenedwa kwa ife kuti olo utangodzuka ndikumwa madzi pang'ono, olo tende kanthanga kamodzi kokha, ndizokwanira ndithu.
Izi ndipotengera ndi malamulo achisilamu, chisilamucho nde chimenecho. Komatu ukakhala kuti siudadye nthawi imeneyi ndekuti wachimwatu ayi, sichomcho. Everything is guided ndi malamulo ndithu.
Kuposera apo, nthawi imene timadya ija timakhala ambiri tadzuka kale around mma 2a.m or 3a.m every day kuyimika mapemphero athu kwa Mulungu, kupempha chifundo ndi chisoni chake.
Mapemphero amenewa timawatchula kuti Tahajd, omwe ali osakakamizika, koma ndiofunika kwambiri koti asilamu ambiri mu mwezi wa Ramadan amapemphera coz ndi mapemphero amene Mulungu wathu, ALLAH adatipangs assure kuti mugawo la usiku, pomwe ena akugona, ifeyo tikayima ndikupemphera, ndithu iye adzatiyankha, ndiyetu timatengera mwayi pamenepa kupemphanso zomwe moyo wathu umafuna kuti Mulungu atatichitira. It works ndithu.
Koma dziko silimayika emphasis pamapemphero athu awusikuwo, kapena aja akummawa aja, koma instead dziko limatipanga criticize pokudya munthawi imeneyi before dawn. Zomwe zili zodabwitsa kwambiri kuti osatipanga criticize pamapempherowo bwanji? Chifukwa every act we do zimatsamira kumeneko.
Ndatha ine wanu Tikos