27/08/2023
Abusa atsopano amene awadzoza kukhala otumikira mu mpingo wa CCAP Blanytre Synod awalangiza kuti akhale achitsanzo, opilira, okhulupirika ndi kulalikira Uthenga wachipulumutso mu utumiki wawo.
"Ndikupemphani kuti mumulole Mulungu akonze milomo yanu kenako muyankhule kuti Ambuye ndili pano nditumeni, adatero M'busa a William Gondwe omwenso ndi mlembi wamkulu wa sinodi ya Livingstonia.
Mu ulaliki wawo umene udatsamira pamutu wakuti ndili pano Ambuye mtumeni (Yesaya 6:8-13, Mateyu 20:25-28) M'busa Tembo adawalangiza abusawa kuti avomereze kukatumikira kulikonse ndinso kwa anthu a magulu onse kuphatikizapo ovutika.
Malangizowa awapereka pa 27 August 2023 kumwambo wa mapemphero ku St Michael and Angels mu mzinda wa Blanytre. Iyi ndi mbali imodzi ya msonkhano waukulu wa Sinodi-yi wachinambala 34.
Poyankhulanso kumwambowu M'busa Khamisa amene akuyembekezera kukhala wamkulu oyang'anira moyo wa uzimu mu Sinodi ya Livingstonia adalangiza adindowa kuti apite akatumikira Yesu Khristu mokhulupirika osati chifukwa cha zokoma ndi zoyanja.
Adapitiriza kuwalangiza kuti akonde mabanja awo ndinso akapange ubale wabwino ndi anthu onse, akakhulupirika pankhani zachuma ndi kupanga zinthu poyera kumalo amene akatumikire.
"Kapeweni zinthu zitatu izi: kufuna maudindo mwachangu, azimayi ofuna kuchita zibwenzi ndi abusa komanso chikondi cha pa ndalama. Osaiwala anthu andale" adatero M'busa Khamisa.
Abusa okwana khumi ndi awiri (12) ndiwo awapatula pa mwambowu umene adautsogolera ndi M'busa Edna Navaya amene ndi Wamkulu Woyang'anira moyo wa uzimu mu sinodi-yi.
Malingana ndi Mlembi wamkulu wa Sinodi ya Blantyre, M'busa Dr Billy Gama izi zikubweretsa chiwerengero cha abusa mu sinodi-yi kufika pa 254 tsopano.
(by Edward Abraham)