GRACE of GOD living Church

GRACE of GOD living  Church Receive updates of how the radical love of Jesus is changing peoples lives and setting them on fire with the Holy Spirit ! Also see info on future events.

20/06/2026

Machitidwe : 8 : 14-16. Atumwi a ku Yerusalemu atamva kuti anthu a ku Samariya analandira Mawu a Mulungu, anatumiza Petro ndi Yohane.15. Atafika anawapempherera kuti alandire Mzimu Woyera,16. chifukwa Mzimu Woyera anali asanafike pa wina aliyense wa iwo; anali atangobatizidwa mΚΌdzina la Ambuye Yesu.
*Hallelujah πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ™ŒπŸ½!!Pamene tikudya nkhomaliro athu masana ano,tiganizire za mau awa,Indee munabatizidwa,Ubatizo omizidwa ndthu,Kma kd munalandira Mzimu Oyera!? Cifukwa mwina ndkutheka kumadzitcha obatizidwa kma mulibe Mzimu Oyera,Pamenepo pakufunika kuzamapo πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™πŸ½πŸ™ŒπŸ½πŸ™ŒπŸ½*

08/05/2026
MUTU 12 KUTHA KWA   BANJA Tiyeni tione mwa zina zomwe zimachitika ngati banja latha. Nthawi zambiri banja limakathera ku...
28/01/2026

MUTU 12
KUTHA KWA BANJA

Tiyeni tione mwa zina zomwe zimachitika ngati banja latha. Nthawi zambiri banja limakathera kukhoti, mwamuna kapena mkazi akakasuma.
Yesaya 41:10
Usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Ngati wachotsedwa ku banja opanda chifukwa chokwanira Yehova amakhala nawe nthawi zonse.
Mukasankha kuti banja lithe, mungalandidwe mwana, nyumba kapena kulipira ndalama. Mungayesetse kudandaulira woweruza koma mwina iye sangasinthe chigamulo. Mapeto ake woweruzayo, yemwe mwina simukudziwana naye n’komwe, angakuuzeni masiku amene muyenera kukaona mwana wanu pa mwezi, ndiponso ndalama zimene muyenera kumamupatsa. Zimene woweruzayu angakulamuleni kuchita zingakhale zosiyana kwambiri ndi zimene inuyo mukanachita panokha.
1 Akorinto 1:10
Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'chiweruziro chomwecho.
Nthawi zambiri kuthetsa banja kumangoyambitsa mavuto ena. Chilichonse chimasintha, kungoyambira kokhala komanso ndalama, ndipo nthawi zambiri kusintha kwake kumakhala kopweteka. Komanso kutha kwa banja kumawakhudza kwambiri ana.

Mateyu 19:9
Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.
Ena amathetsa banja ati chifukwa mkazi sakubereka kapena mwamunsa koma tizindikire mawu ochokera ku Genesis 25:21, Ndipo Isaki anampembedzera mkazi wake kwa Yehova popeza anali wouma: ndipo Yehova analola kupembedza kwake, ndipo Rebeka mkazi wake anatenga pakati.

Address

Salima

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when GRACE of GOD living Church posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share