20/04/2026
Kodi mumatani wina akakuchitilani choipa? Kodi mumakhululuka kapena mumabwezera?
Wokondedwa moyo uno utawachitira ena zabwino zotani, sionse amabweza zabwino. Ena amabweza chipongwe Malo mobweza zabwino. Moyo uno ena amatha kukunyoza ngakhale usanawalakwire kalikonse. Ena amatha kukuipitsira mbiri ngakhale usanawalakwire kalikonse. Ena amatha kukunyoza popanda nkhani yeniyeni. Ma officemu muli kupekelana nkhani kuti wina zake zisokonekele basi.
Kodi zonsezi zikachitika Kodi inu mumatani? Mumabwenzera kapena mumasankha kukhala chete?
Choyamba tikueneka kudziwa kuti moyo uno zotichimwitsa sizizaleka kubwera, Luke 17:1. Kutanthauza kuti titachita zabwino zotani zotikhumudwitsa zidzikhalapobe, koma zikachitika tikueneka kusankha kukhululuka. Monga Yesu Khristu anatikhululukila pa mtanda paja, ifenso tiyeni tikhale nawo mtima womwewo kwa a mangawa athu. Amen
Luka 23:34
*Yesu anati, “Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita.” Ndipo anagawana malaya ake mochita maere.*
Machitidwe a Atumwi 7:59-60.
*Akumugenda miyala, Stefano anapemphera kuti, “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.”*
*Ndipo anagwada pansi nafuwula mwamphamvu kuti, “Ambuye musawawerengere tchimoli.” Atanena mawu amenewa anamwalira.*