21/11/2018
*PHUNZIRO LA KOTALE M'CHIGAWO CHA AKULU*
*PHUNZIRO: 8*
( *17-23 NOVEMBER*)
*UMODZI M'CHIKHULUPILIRO (UNITY IN FAITH)*
_LASABATA_ _MASANA_
Machitidwe 4:8-12,1:11
Mateyu 25:1-13
Ahebri 9:11,12
Ekisodo 20:8-11
1 Akorinto 15:51-54
*VESI LOLOWEZA*
(Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense ,Pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo lakumwamba,lopatsidwa mwa anthu,limene tiyenera kupulumutsidwa nano *Machitidwe 4:12*).
M'chaka cha *1888* mpingo wa Seventh-day Adventest unadutsa mu mtsutsano waukulu wokhuza kamasulidwe ka mavesi ena ofunikira kwambiri m'Baibulo.
Pamene Abusa ndi akulu a mpingo amatsutsana zokhudza tanthauzo la *Nyanga khumi*, mu ulosi wopezeka pa *Daniel chaputala 7*,komanso tanthauzo la lamulo lomwe likukambidwa pa *Agalatiya 3:24*,ziwalo zambiri mu mpingo sizinazindikire kukula kwa udani,womwe unali pakati pa wina ndi mnzake mpaka kufika poononga chiyanjano chawo, ubwenzi wawo,komanso umodzi wawo ndi cholinga cha utumiki wa mpingo.
*Ellen G White* anadzudzula chochitikachi,ndipo anawalimbikitsa onse omwe amatenga nawo mbali pa zikambiranazi,kuganizira mofatsa zokhuza ubale wawo ndi *Yesu*,komanso mmene chikondi chathu pa *Yesu* chikuyenera kuonesedwa mu khalidwe lathu,makamaka pamene tasiyana maganizo.
*TSIKU LOYAMBA*
*CHIPULUMUTSO MWA YESU (SALVATION IN JESUS)*
Ngakhale ife a *Seventh-day Adventest* tili ndi ziphunzitso zina zofanana ndi mipingo ina ya Chikhristu,komabe zikhulupiliro zathu zonse pamodzi ndi zapaderadera kwambiri, pofotokoza Choonadi cha m'Baibulo zomwe mipingo ina ya Chikhristu siilalikira.
Ziphunzitso zimenezi ndi zomwe zimatipanga ife kukhala mpingo wa Mulungu wotsala,wa kumapeto a nthawi.
*Kodi Petro akuonetsa kuti akumvetsetsa bwanji kufunikira kwa Yesu Khristu mu nzeru ya Chipulumutso? Machitidwe 4:8-12*
Mtumwi Paulo anawauza anthu aku Korinto kuti UTHENGAππ wabwino "ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Khristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa iye yekha" *2 Akorinto 5:19*
*TSIKU LACHIWIRI*
*KUBWERA KWACHIWIRI KWA KHRISTU (SECOND COMING OF CHRIST)*
Atumwi pamodzi ndi Akhristu oyambilira ankatenga Kubweranso kwa Khristu monga "Chiyembekezo chodala" *Tito 2:13*,Ndipo iwo anayembekezera kuti maulosi ndi malonjezano onse a mmalembo adzakwaniritsidwa pakubweranso kwachiwiri.
Akhristu a *Seventh-day Adventest* akadagwiritsabe kulimba chikhulupiliro chimenechi. Kunena zoona (mwatchutchutchu),dzina lathu loti *Adventest* likufotokoza bwino za nkhani imeneyi. Onse omwe akonda Khristu akudikirira tsiku lina mtsogolo, limene adzakhale pa chiyanjano choonana maso ndi maso ndi maso ndi *Yesu*.
Kuyambira tsopano mpaka tsiku limenelo, lonjezo la kubweranso kwachiwiri kwa Khristu likupereka chikoka chotilunzanitsa pamodzi monga anthu a Mulungu.
*Kodi mavesi otsatirawa akutiphunzitsanji zokhuza mabweredwe a Khristu?*
Machitidwe 1:11
Mateyu 24:26,27
Chivumbulutso 1:7
1 Atesalonika 4:13-18
Chivumbulutso 19:11-16.
*TSIKU LACHITATU*
*UTUMIKI WA YESU MKACHISI WA KUMWAMBA (JESUS MINISTRY IN THE HEAVEN SANCTUARY)*
Mulungu anamuuza Mose m'chipangano chakale kuti amange chihema, kapena kachisi kuti akhale ngati "mokhalamo" mwake pano pa dziko lapansi *Ekisodo 25:8*. Kachisi ndi malo omwe anthu a Israeli amaphunzirako nzeru ya chipulumutso,kupyolera mu mautumiki ake osiyanasoyana. Mzaka za mtsogolo, nthawi ya mfumu Solomon, kachisi wonyamula uja anasinthidwa ndi kachisi wamkulu wopangidwa mwa luso *1 Mafumu 5&8*. Makachisi onse awiri, wamng'ono ndi wamkulu anamangidwa mofanizira kachisi wakumwamba, *Ahebri 8:2,Ekisodo 2:59-40*.
Kupyolera mu Baibulo lonse, pali ganizo loti pali kachisi wakumwamba,yemwe ndi kokhalako kwake kwenikweni kwa Mulungu.
*TSIKU LACHINAYI*
*SABATA (THE SABBATH)*
Chiphunzitso China chofunikira kwambiri chomwe Akhristu a *Seventh-day Adventest* amakhulupilira, komanso kuchigwiritsitsa ndi Sabata la tsiku LACHISANU ndi chiwiri. Ichi ndi chiphunzitso cha chipembezo cha mtengo wapatali chimene chimadzetsa umodzi ndi chiyanjano pakati pathu. Ndicho chimene ife tokha chimatitsatira bwino pokhala ndi zosiyana zochepa kwambiri mu chipembezo chonse cha Chikhristu.
Sabata ndi Mphatso yopasidwa kwa munthu Kuchokera kwa Mulungu kuyambira msabata lomwelo la chilengedwe *Genesis :21-3*
*TSIKU LACHISANU*
*IMFA NDI MZUKIRO (DEATH AND RESURRECTION)*
Pa nthawi ya chilengedwe, Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo *Genesis 2:7*. Nkhani iyi ya chilengedwe cha munthu imaonetsa kuti Moyo umachokera kwa Mulungu.Kodi Moyo opanda malekezero uli mkati mwa Moyo umenewu?.
Baibulo limatiuza kuti Mulungu yekha ndi pamene alinawo moyo wosatha.
Moyo wopanda malekezero superekedwa kwa anthu pobadwa ayi *1 Temoteo 6:16*.
Munthu ndi wosiyana ndi Mulungu chifukwa munthu amafa.
*werengani*
Yakobo 4:14
Mlaliki 9:5
Masalimo 146:4
*MATHERO A PHUNZIRO 8*
*Okonzedwa ndi:*
*TEACHING SDA GOSPEL WHATSAPP GROUP (TSGWG)*
*+ _265991390469_*