15/03/2026
M'mawa wabwino kwa nonse oyera mtima! MAWU A MULUNGU MU CHICHEWA CHALERO.( 2016)
Luka 7 vs 14.
Kenaka anapita nakakhudza chithatha cha maliro, ndipo amene anachinyamulawo anayima. Iye anati," Mnyamata ndikukuwuza kuti dzuka!"
Amene tikuweranga mu mawu athu a lerowa ndi mawu a Ambuye athu Yesu amene anadzutsa mnyamata wakufa.( Luka 7:15)
Ma lofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri zinamva mawu a Mulungu ndipo zinadzichulukitsa ndipo anthu ambiri anadya ndi kukhuta.( Marko 6:38-44)
Nsomba mu nyanja zinamva ndithu kuti Ambuye Yesu akunena kuti zipite ku dzanja lamanja la bwato la ophunzira ake a Yesu kuti akazigwire ndipo zinachitikadi.( Yohane 21:4-6)
Izi ndi mphamvu zimene mawu a Mulungu ali nazo, ndipo ife tinawuzidwa kuti titatenga mawu a Mulungu ndi kuwasunga mkati mwathu, ndiye kuti chilichonse chimene tingafune kuti chichitike chidzatheka.( Yohane 15:7)
Pajatu zimene zimatuluka m'kamwa mwa munthu ndi zimene zinasungidwa mkati mwa munthuyo.( Mateyu 12:34-35)
Kutereku mawu amene anatuluka pakamwa pa Elisa ndi kupanga kuti madzi a mu mtsinje wa Yorodani amuchititse Namani anali mawu a Mulungu.( 2 Mafumu 5:9-10,14)
Petro anangoyankhula mawu a Mulungu kwa munthu olumala amene ankakhala pa chipata chokongola ndipo pompo anachira.( Machitidwe 3:1-8)
Inuyo muli ndi mawu anji kapena kuti a ndani mkati mwanu oti akhonza kusintha zinthu? Tamasungani mawu a Mulungu mkati mwanu ndipo mudzakhala ndi ulamuliro wa kusintha zinthu zimene mukufuna kuti zisinthe.
Ambuye Mulungu akudalitseni kwambiri, mukhale ndi tsiku lopambana zedi!