Pastor Chisomo Khomera

Pastor Chisomo Khomera Revelation 14:7
Fear God and give him groly for the hour of his judgement is come...

Sabata Lopambana
18/04/2026

Sabata Lopambana

04/07/2024

NTHAWI

Mbalame ikakhala ndi moyo imadya nyerere. Mbalame ikafa, nyerere zimadya mbalameyo. Nthawi ndi zochitika zimatha kusintha nthawi iliyonse.

Osachepetsa kapena kunyoza munthu aliyense m'moyo. Ukhoza kukhala wamphamvu lero, koma kumbukira, Nthawi ndi yamphamvu kuposa inu.

Mtengo umodzi umapanga ndodo za machesi mamiliyoni koma machesi amodzi okha ndi omwe amafunikira kuwotcha mitengo mamiliyoni.

Khalani wabwino ndipo chitani zabwino.

Tsiku labwino

06/02/2024

PHUNZIRO LA SABATA SUKULU KOTALE M'CHIGAWO CHA AKURU.

PHUNZIRO: 6

Mutu: NDIDZAUKA

Lasabata Masana

Phunziro Lathu Mlungu Uno Tiwerenga Kuchokera mu:
Masalimo 18:3-18, Masalimo 4l:13, Deuteronomo 15:7-11, Masalimo 82,
Masalimo 96:6-10, Masalimo 99:1-4, Aroma 8:34. 8:34.

Vesi Loloweza: "Chifiukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, Ndiuka tsopano, ati Yehova; Ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo " (Masalimo 12:5).

Mbadwo wathuwu si wokhawo momwe choipa, chosalungama ndi kuponderezana zakhala zikuchitika mochuluka kwambiri. Nawonso olemba Masalimo anakhala mu nyengo zangati zomnwezi. Ndipo
chidzudzulo chimene Mulungu akuchita pofuna kudzudzura ziwawa ndi kuponderezana zomwe zikuchitika m'dziko lapansi lathuli komanso chidzudzulo cha olemba masalimowo eni.

Inde, Yehova ndi woleza mtima ndipo Iye amagwira mkwiyo Wake mu
chilekerero Chake chachikulu, osafuna wina awonongeke,koma kuti onse afike ku kulapa ( 2 Petro 3:9-15). Komabe,ngakhale nthawi yoikika ya kulowelerapo kwa chiweruziro cha Mulungu ikubwera ndithu (Masalimo 96:13,Masalimo 98:9). Ife tikungoyenera kukhulupira Yehova ndi malonkezo Ake,kufikira nthawi yomwe tsikulo lidzafika.

Mlengi yekha, amene mpando Wake wachifumu wakhazikitsidwa pa chilungamo (Masalimo 89:14, Masalimo 97:2), ndipo chiweruziro Chake ndi chachikulu ndi yemwe angapereke mtendere ndi chipambano ku dziko lino lapansi. Magawo awiri a chiweruziro cha Mulungu akuphatikizira chiombolo cha oponderezedwa komanso kuonongedwa kwa oipa (Masalimo 7:6-17).

Izitu ndi zimene ife talonjezedwa,ndipo ndithudi tsiku lina zimenezi zidzachitika, koma iyi idzakhala nthawi yoikika ya Mulungu,osati yathu ayi,ndipo imeneyi ndi mfundo imene olemba Masalimoyu akutsindika kwambiri.

TSIKU LOYAMBA

WANKHONDO WAMPHAMVU

Werengani Masalimo 18:3-18, Masalimo 76:3-9, 12; ndi Masalimo
144:5-7. Kodi Yehova wafotokozedwa motani mmavesi amenewa? nanga zifanizo zimenezi zikuti chiyani za mmene Mulungu alili wokonzeka kuombola anthu Ake?

Nyimbozi zikuyamika Yehova chifukwa cha mphamvu Zake zodabwitsa zomwe ndi zoposa mphamvu za chopa zimene zikuopseza anthu Ake. Masalimo anaonetsera Mulungu mu ulemelero Wake monga Wankhondo chilkupezeka mmalo ambiri m'buku la Masalimo ndipo chagwiritsidwa ntchito kutsindika za kufunikira ndi kutsimikizika kwa yankho la Malungu loyankha anthu Ake amene
akulira chifukwa cha mavuto awo.

"Ndipo anagunda m'mwamba Yehova. Ndipo Wam'mwambamwamba anamvetsa liwu lake; Matalala ndi makala amoto. Ndipo anatuma mivi yake nawabalalitsa;Inde mphezi yaunyinji nawamwaza. Ndipo zikuoneka zoyendamo madzi,Nafukuka madziko a dziko lapansi,mwa kidzudzula kwanu, Yehova mwa Mpumo wa mpweya wa mphuno mwanu" (Masalimo 18:13-15).

Kutsimikizika ndi kukula Kwa ntchito ya Mulungu kukuyenera kuchosa
chikaiko china chilichonse chokaikira za chitsamaliro ndi chifundo chake chachikulu pa odzunzidwa kapena chokaikira za mphamvu yake yogonjetsa choipa. Ifetu tikungoyenera kudikira iye kuti achite motero.

Ndipo pamapeto pake , ngakhale pamene anthu a Mulungu monga Davide anali kumenya nkhondo,chiombolo sichinachitidwe ndi mphamvu ya munthu. Mu nkhondo zake zomenyana ndi adani a anthu a Mulungu,mfumu Davide analemekeza Mulungu kuti iye yekha ndi amene anachita zipambano zonse.

Ndithudi chikadatha kukhala chinthu chofewa kwa Davide kudzitamandira pa zomwe zinachitika pa zipambano ndi zigonjetso zakezo, chikhalirecho iye sanaganize motero ayi. Davide ankadziwa bwino lomwe gwero la mphamvu zake.

Ngakhale Davide akunena kuti Yehova akuphunzitsa manja Ake nkhondo (Masalimo 18:34) mu nkhondo zake zonsezo, palibe pena paliponse m'masalimo pamene iye akudzitamandira chifukwa Cha luntha lake lodziwa kumenya nkhondo. M'malo mwake Davide akutama Yehova monga amene akumumenyera iye nkhondo ndi kukuombola (Masalimo 18:47-48).

M'Masalimo, mfumu Davide amene watchulidwa monga wankhondo wamkulu, akugwira ntchito yake monga katswiri odziwa kuimba nyimbo mwanthetemya komanso amene akulemekeza Yehova monga mombolo ndi wakusunga wa anthu Ake yekhayo (Masalimo 114:10-15). Kulemekeza Mulungu ndi kupemphera ndi zomwe zili gwero la mphamvu za Davide,zinthu zimene zinali zamphamvu kuposa chida china chilichonse cha nkhondo. Mulungu yekha ndi amene ayenera kukhulupilidwa ndi kulambiridwa ndi anthu onse.

*Posatengera kuti muli ndi mphatso,maluso ndi zipambano zanji mmoyo mwanu,Kodi ndi chifukwa chiyani kuli koyenera kuti nthawi zonse inu muzikumbukira gawo la zonsezi? Nanga pamene inu mwaiwala gwero la mphamvu zanu,pakakhala choopsa chanji?*

TSIKU LACHIWIRI

CHILUNGAMO KWA OPONDEREZEDWA

Werengani Masalimo 9:18, Masalimo 12:5, Masalimo 40:17,Masalimo 41:1-3, Masalimo 113:7, Masalimo 146:6-10. Kodi ndi uthenga wanji
umene uli m'mavesi amenewa, womwe ukubwera ngakhalenso kwa ife lino??

Mulungu akuonetsera chitsamaliro chapadera komanso nkhawa yake pa momwe adindo ambiri akulepherelera kuchita chilungamo pa magulu osiyanasiyana a anthu osowa chitetezo,monga osauka,aumphawi,oponderezedwa, opanda bambo,akazi amasiye ,amuna amasiye ndi alendo. Masalimo akufotokoza bwino mfundo imeneyi,monganso chilamulo ndi aneneri (Eksodo 22:21-27,Yesaya 3:13-15).

Masalimo ambiri amagwiritsa ntchito mawu oti "osauka ndi aumphawi" ndipo amapewa kuwatchula oponderezedwa pogwiritsa ntchito mawu ozolowereka ku fuko ndi chipembedzo cha Chiyuda. Izi zachitika pofuna kusindika kuti chitsamaliro Cha Mulungu ndi chopita Kwa anthu onse apadziko lapansi.

Mawu oti "osauka ndi aumphawi" sakungonena za umphawi wakusowa
chuma wokha, koma akuoneranso za umphawi wakusowa chitetezo ndi thandizo. Mawuwa akunena za chifundo Cha Mulungu,ndipo kupereka ganizo lakuti munthu wosaukayo ali yekha yekha komanso alibe thandizo lina lililonse ndipo thandizo lake lokhalo ndi Mulungu yekha basi.

Chithunzithunzi cha "osauka ndi aumphawi" chikukambanso za kukhulupirika, kuona mtima, ndikukonda Mulungu povomereza kuti ife timadalira pa Iye yekha basi ndi kukana khalidwe lina lililonse losonyeza kudzidalira ndi kuzitamandira tokha.

Ndithudi,panopa kusamalira osauka (Masalime 41:1-3) kuli chisonyezo cha kukhulupiriku kwa anthu pamaso pa Mulungu. Zoipa zimene anthu osowa chitetezo anali kuchitiridwa zinali zoipa Kwambiri maka mu chikhalidwe Cha Baibulo nthawi ya (Deuteronomy 15:7-11). Masalimo akulimbikitsa anthu okhulupilira kukweza mawu awo podzudzula mchitidwe uliwonse wankhanza ndi wopondereza osauka.

Masalimo akutsindikanso za kupanda pake koika chikhulupiriro chathu pa zinthu zokutha,kuzitenga ngati izo ndi gwero podalirika la nzeru ndi chitetezo chathu. Anthu a Mulungu akuyenera kukana yesero loika chikhulupiliro chonse Cha chipulumutso chawo mwa atsogoleri awo komanso mu nzeru za anthu,maka pamene zinthu zimenezi zili zosemphana ndi njira za Mulungu.

Mu chisomo chake Ambuye wathu Yesu Khristu anamvetsetsa mavuto amene osauka amakumana nawo,pokhala osauka Iye mwini ,kuti m'kusauka Kwake ambiri akhale olemera (2 Akorinto 8:9). Kulemera Kwa Khristu kukuphatikizira kumasulidwa kwathu ku kuponderezedwa kulikonse kobwera kamba ka uchimo,ndipo Iye akutilonjeza moyo wosatha mu ufumu wa Mulungu (Chivumbulutso 21:4).

Yesu Khristu akukwaniritsa malonjezo amene akupezeka m'masalimo okamba za Woweruza wa Mulungu,amene adzaweruze aliyense wochita nkhanza anthu osauka komanso aliyense wonyalanyaza udindo wosamalira aumphawi (Mateyu 25:31-46).

*Kodi ndi kangati ife timaganizira za "osauka ndi aumphawi" amene ali pakati pathu,nanga ndi kangatinso ife timawasamalira anthu oterewa??*

TSIKU LACHITATU

KODI MUDZAWERUZA MOPANDA CHILUNGAMO KUFIKIRA LITI?

Yehova wapatsa atsogoien a lsrayeli mphamvu zosunga ndi kulimbikitsa chilungamo mu ISrayeli (Masalimo 72:1-7, 12-14). Mafumua Israyeli ankayenera kugwiritsa ntchito mphamvu zawo motsatira chifuniro cha Mulungu. Cholinga chachikulu cha atsogoleriwo chinayenera kukhala kuonetsetsa ku mdzikomo muli mtendere ndi chilungamo komanso kuti osauka akusamaliridwa,ndipo pokhapo ndi pamene dzikolo ndi anthu ake onse akadapedza chipambano .

Ufumuwo ukukhala Wamphamvu chifukwa Cha kukhulupilika Kwa atsogoleri ndi anthu Ake pamaso pa Mulungu,osati chifukwa za mphamvu zawo za umunthu.

*Werengani Masalimo 82. Kodi chinkachitika ndi chiyani atsogoleriwo akakhotetsa chilungamo ndi kupondereza anthu amene iwo anapatsidwa kuti awateteze???*

Mu Masalimo 82. Mulungu akulengeza zilango zake pa oweruza a ISrayeli omwe anali opanda chilungamo, "Milungu" (Masalimo 87:1,6) yomwe yatchulidwayi,modziwikiratu singakhale milungu yachikunja kapena angelo, chifukwatu magulu awiriwa sanapatsidwe udindo opereka chilango Kwa anthu a Mulungu,chotero iwo sakanalangidwa chifukwa cholephera kukwaniritsa udindo umenewu.

Malamulo amene alembedwa mu Masalimo 82:2-4 akubwereza Malamulo omwe ali m'mabuku asanu oyambilira a Baibulo olembedwa ndi Mose momwe atsogoleri a ISrayeli atchulidwa monga 'milungu' (Deuteronomo 1:16-18,16:18-20, Yohane 10:33-35), Mulungu akufunsa "ana a anthu" ngati akuweruza mwa chilungamo ndipo chilungamo chao chilengezedwa chifukwa iwo apezeka opanda chilungamo. Atsogoleri apunthwa mu mdima koma sakudziwa (Masalimo 82:5), chifukwa iwo asiya chilamulo cha Mulungu chomwe chili kuunika (Masalimo 119:105).

Malembo akulimbikitsa motsindika ganizo lakuti Yehova ali Mulungu yekhayo. Mulungu amalamulira dziko lapansi kupyolera mwa atsogoleri a anthu amene asankhidwa ndi Iye kukhaka akazembe Ake (Aroma 13:1), Chikhalirecho,kodi ndi kangati mu mbiri za dziko ngakhalenso panopa akazembe amenewa,akhala akugwiritsa ntchito udindo wawo molakwika.

Masalimo 82 monyogodola akuika poyera mpatuko wa atsogoleri ena amene amadzikweza pamwamba pa anthu awo,podziyetsa iwo eni 'milungu'. Ngakhale Mulungu amapereka ulamuliro ndi mwayi Kwa atsogoleri a ISrayeli,wotchedwa "ana a Mwambamwamba" komano womuimikira Iye monga akazembe Ake, Iye anadzudzulabe atsogoleri oipawa .

Mulungu akukumbutsa atsogoleriwo kuti ali chimodzi modzi anthu ena onse,ndipo akuyenera kumvera Malamulo otsogolera anthu ku khalidwe,mmene zilili ndi anthu ena onse, chifukwa palibe munthu amene ali opambana woposa malamulo a Mulungu (Masalimo 82:6-8).

Mulungu adzaweruza dziko lonse lapansi; nawonso anthu a Mulungu adzayankha milandu yawo kwa Mulungu. Magulu onse awiri, atsogoleriwo ndi anthu awo,onse akuyenera kutsanza chitsanzo cha Woweruza wa Umulungu ndi kuika chiyembekezo chawo chonde mwa Iye.

Kodi inu muli ndi ulamuliro wanji pa ena? Nanga mukugwiritsa ntchito ulamuliro wanuwo molungama ndi m***a mtima motani?

Inutu mukuyenera kumvera zimene zanenedwazi.

TSIKU LACHINAYI

TSANULANI MKWIYO WANU

Werengani Masalimo 58:6-8;Masalimo 69:22-28;Masalimo 83:9-17;Masalimo 137:7-9, Masalimo 94:12. Kodi Masalimo amenewa akutipatsa malingaliro anji?Nanga m'Masalimo amenewa ndi ndani amene watchulidwa kuti ndi mkhalapakati wa chiweruziro ??

Masalimo ena akupempha Mulungu kubwezera chilango pa anthu ndi mafuko amene akufuna kuononga, kapena amene aononga kale,Alembi a Masalimo kapena ngakhale anthu awo.

Masalimo akhoza kuoneka ndi kumveka ngati ndi ovuta kuwamvetsetsa kamba ka mawu ake achindunji amene akuoneka ngati ali osemphana ndi mfundo ya Baibulo yotilangiza kukonda adani athu (Mateyu 5:44).

Komabe, mkwiyo wa mlembi wa Masalimoyu wodana ndi nkhanza kapena kuponderezana uli mkwiyo wothandiza ndi wabwino. Zikutanthauza kuti olemba Masaimowa anali osamala kwambiri pa mfundo zokhudza chabwino ndi choipa kuposa mmene ena ambiri ankakhalira. Iwo anali okhuzika
chifukwa zoipa zomwe zinali kuchitidwa m'dziko lapansi osati zochitidwa kwa iwo kokha koma ngakhalenso zimene zimachitidwa Kwa anthu ena.

Komabe, palibe pamene wolemba Masalimoyu mwini wanena kuti abwezera choipacho yekha. Koma mmalo mwake iye akusiya nkhani yobwezerayo m'manja
mwa Mulungu mwini Wake. Masalimowa akukumbutsa anthu za matemberero a
pangano la Mulungu (Denteronomo 27:916), ndipo olemba Masalimowa akupempha Mulungu kuti lye achitepo kanthu posatira lonjezo Lake.

Masalimo ali malangizo olembedwa mu ulosi onena za chiweruziro Cha
Mulungu chimene chilinkudza; iwo sanangokhala mapemphero a wolemba Masalimo kokha. Salimo 137 likuonetsera kulengezedwa kwa chiweruziro cha
Mulungu pa Baibulo, monganso mmene zaonetseredwa kupyolera mwa aneneri.

Chionongêko chimene anthu a Baibulo anachita pa mafuko ena chidzabwerera pa iwo eni. Masalimo akupereka malangizo a umulungu oti ochita choipa sadzakhala osalangidwa mpaka kale.

Kubwezera kwa Mulungu kumachitika mwa chilungamo ndi mwa chisomo. Ana a Mulungu akupemphedwa kupempherera iwo amene akuwachitira nkhanza ndi
khumbo lalikulu loti anthu oterowo atembenuke (Masalimo 83:18,Yeremiya 29:7).

Komabe, pamene alembi a Masalimo akufuna kuti Masalimowa agwirizane
Ndi ndondomeko ya chikondi cha pa adani, ife tikuyenera kusamala kuti tisachepese zochitika zoipa ndi zowawa zimene zafotokozedwa m'Masalimo amenewa.

Mulungu akuvomereza za kutsautsidwa Kwa ana Ake ndipo lye akuwatsimikizira kuti 'imfa' ya okondedwa Ake nja mtengo wake pamaso pa Yehova" (Masalimo 116:15).

Chiweruzo cha Mulungu chimkakamiza anthu Ake kukweza mawu awo podzudzula choipa ndi kufuna kuti ufumu Wake udze m'chidzalo chake chonse. Masalimo akulankhula kwa anthu amene akuvutika ,kuwadziwitsa kuti Mulungu akudziwa za kuvutika kwawo ndi kuti tsiku lina chilungamo chidzafika ndithu.

*Kodi ndi ndani amene nthawi zina sakhala ndi maganizo kapena malingaliro ofuna kubwezera Kwa anthu amene anamuchitira choipa kapena amene anachitira okondedwa ake chinthu choipa Kwambiri? Kodi Masalimo amenewa angakuthandizeni bwanji kuchosa malingaliro otero??*

TSIKU LACHISANU

CHIWERUZO CHA YEHOVA NDI KACHISI

Werengani Masalimo 96:6-10; Masalimo 99:1-4; ndi Masalimo 132:7-9,13-18. Kodi chiweruzo cha Mulungu chikuchitikira kuti, nanga yankholi lili ndi zotsatira zanji pa ife? Kodi kachisi amatithandiza bwanji kumvetsetsa momwe Mulungu adzachitire ndi choipa?

Chiweruziro cha Yehova chili cholumikizana Kwambiri ndi kachisi. Kachisi ndi kumalo komwe wolemba Masalimo anayamba kumvetsetsa bwino za vuto la choipa (Masalimo 73:17 20). Kachisi anakazikitsidwa monga malo a chiweruziro cha Mulungu monga mmene zaonetseredwa ndi chiweruziro cha
Urimu (Numeri 27:21) komanso chapachifuwa cha chiweruziro cha mkulu wa ansembe (Eksodo 28:5, 28-30). Chotsatira chake, Masalimo ambiri akutionetsera Mulungu Ali pa mpando Wake wa chifumu m'kachisi, ali wokonzeka Kuweruza dziko lapansi chifukwa cha tchimo ndi choipa chake.

Nayonso nzeru ya chipulunutso inaonetseredwa kuchokera ku kachisi. Poyamba, anthu achikunja ankalimvetsa tchimo monga banga looneka ndi maso lomwe linkayenera kuchotsedwa pogwiritsa ntchito njira za matsenga Mosiyana
ndi zimenezi, Baibulo limati tchimo ndiko kuchita khalidwe lolakwika la lamulo la Mulungu.

Chiyero cha Mulungu chimatanthauza kuti lye ndi Mulungu wokonda chilungamo ndi kuongoka mtima. Momwemonso anthu Ake akuyenera kutsata
chilungamo Chake ndi kukhala a mtima woongoka, konanso ampembedze lye
m'chiyero Chake. Anthuwo angathe kupembedza Mulungu mchiyero pokha pokha ngati iwo atasunga chilamulo Chake, chomwe chili chitsanzo cha chiyero Chakecho.

Choteroo monga zaonetseredwa ndi mpando wa chifundo wa Mulungu komanso "nsembe za chilungamo," kachisi ndi kumalo kumene machimo
amakhululukidwa ndi komwenso chilungamo chimabwezeretsedwa (Deuteronomo 33:19, Masalimo 4:5:).

Chikhalirecho, "Mulungu wakuwakhululukira" akubwera chilango pa ntchito zoipa za anthu osalapa (Masalimo 99:8). Zotsatira zoonekeratu zoonetsera kachisi monga malo a chiweruziro cha Mulungu zikuoneka mu kutchulidwe Kwa nthawi ndi nthawi kwa chiyero cha Mulungu komanso m'malamulo otilangiza kukhala moyo wa chilungamo, wogwiriza ndi mfundo za Mulungu zomwe zili m'pangano Lake.

Chotsatira Cha chiweruziro Cha Yehova chochokera m'ziyoni chili moyo wabwino wa olungama ndi kugonjetsedwa Kwa ochimwa (Masalimo 132:13-18). Kachisi akulimbikitsa chiyembekezo chotsangalatsa cha kubwera Kwa Yehova monga Woweruza Maka pa Tsiku la Chitetezero.

Momwemonso Masalimo akutitsimikizira kuti Woweruza wa Umulungu wotchedwa Yesu Khristu afika posachedwa m'kachisi wa kumwamba (Masalimo 96:13,98:9, chivumbulutso 11:15-19).

*Werengani Aroma 8:34. Kodi vesi limeneli likutisonyeza bwanji zoti zimene Khristu akuchita m'Kachisi wa kumwamba ndi nkhani yokomeraa anthu Ake*

TSIKU LACHISANU NDI CHIMODZI

KUPITIRIZA PHUNZIRO:

Werengani Ellen G. White, "The Beatitudes," masanmba 6-13, 29-35. M'bukhu la Thoughts From the Mount of blessing.

Masalimo ali mfundo zodzula anthu amene salabadira pamene ena akuchitidwa chosalungama; mfundo zimene zimaletsa anthu kuyanjana ndi choipa. Masalimo salimbikitsa ndi khumbo lofuna kubwezera choipa koma ndi olombikitsidwa ndi changu chofuna kulemekeza dzina la Mulungu.

Pa chifukwachi,ndi
koyenera kuti olungama akondwere pamene akuona kubwezera
kwa Mulungu pa choipa, chifukwa kudzera mu njira imeneyi ndi momwe dzina la
Mulungu ndi chilungamo Chake zibwezeretsedwe m'dziko lapansi (Masalimo 58:10,11).

Masalimo akukakamiza anthu kuti akweze mawu awo, adzudzule choipa ndipo iwo afune kuti ufumu wa Mulungu udeze m'chidzalo chake. M'masalimo,ife tapatsidwa chitsimikizo cha chitonthozo ndi chiombolo cha umulungu. Yehova adzauka!

Mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu,. .chifukwa cha Ine. Sekerani,
sungalalani. Ndipo Yesu analozera omvera Ake kwa aneneri amene analankhula
m'dzina a Yehova, monga chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima (Yakobo 5:10).

Abele, MKhristu woyamba mwa ana a Adamu, anaphedwa
chifukwa cha chikhulupiriro chake. Enoke anayenda ndi Mulungu, ndipo dziko lapansi silinamuzindikira. Nowa ananyozedwa monga wochita zinthu moonjeza
ndi mokomeza. Koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira,ndiponso nsinga,ndi kuwatsekera m'ndende.

Ena anakwapulidwa, osalola kuomboledwa,kuti akalandire kuuka koposa; Ahebri 11:35,36. -Ellen G White 'Thoughts from the Mount of Blessing,tsamba 33.

MAFUNO OKAMBIRANA: :

1️⃣. Chifukwa chowawidwa mtima kamba ka kupezeka kwa choipa m'dziko lapansi munthu akhoza kukaikira ngati Mulungu akulamuliradi,kodi tingakuze bwanji chikhulupiriro chathu kuti chikhale chosagwezeka chomwe chingaime nji ngakhale m'mayesero? Ndiye kunena kuti, kodi ife chiyang'aniro
chathu pa Chiyani kuti tisunge chikhulupiriro chathu mu chikondi, ubwino ndi mphamvu za Mulungu? Nanga mtanda ukuyenera kutiuza chiyani zokhudza Mulungu ndi khalidwe Ake?

2️⃣. Kodi ndi chifukwa chiyani kuli kofunikira kuti tisadalire njira za anthu (atsogoleri, magulu, ndi mabungwe) monga ndi mayankho opambana a chilungamo m'dziko lino lapansi,koma ife tidalire kwathunthu pa Mawu a Mulungu ndi chiweruzo Chake??

3️⃣. Kodi zotsatira zenizeni za choonadi choti kachisi ndi malo a chiweruziro
cha umulungu ndi chiyani?

4️⃣. Kodi ife
tingamvetsetse bwanji mawu achindunji omwe
anenedwa m'Masalimo ena? Nanga mawu amenewa akutanthauza bwanji kumvetsetsa nyengo zimene alembi a Masalimowa anali kudutsamo??

MATHERO A PHUNZIRO LATHU.

Follow Pastor L Khomera on Facebook

21/01/2024

PHUNZIRO LA (KALASI LA UBATIZO) BIBLE CLASS.

PHUNZIRO:4

Mutu: NTCHITO YA MZIMU WOYERA

VESI LOLOWEZA: "Koma Nkhosweyo, MZimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, lyeyo adzaphunzitsa inu zonse." Yohane14:26.

CHOLINGA: Kuvumbulutsa chifuniro ndi ntchito ya munthu wachitatu wa Mulungu mwa atatu.

GANIZO LOTSOGOLERA: Malembo ndi umboni wake wormwe zímaululira kuti Khristu ndiye Mulungu.

Kuyendayenda kwake m'maonekedwe a umunthu kunalenga chilumikizo cha pakati pa munthu ndi Mulungu.

Pamene lye anabwerera kupita kumwamba lye analinganiza kuti
Mulungu mwa atatu apitirizebe kudzionetsera pa dziko, ndipo lye
anapanga njira ya kuti chichitike.

KODI NDI KUTI KUMENE lFE TIMAPHUNZIRA ZA MZIMU
WAMUYAYA?

Kodi ndi kuti m'Malembo kumene ife tili kupeza umboni woyamba wa Mzimu Woyera? Yobu 26:13; Genesis 1:2.

Kodi ndi lonjezanooani limene Khristu anapereka lonena za Mzimu WoyeraYohane t4.16,17

KUFOTOKOZA: "Mzimu Woyera ndiwo unali mphatso yapamwamba pa mphatso zonse zimene lye anakhoza kukapempha kuchokera kwa Atate Wake chifukwa cha kukwezeka kwa anthu Ake.

Mzimu unali kuti uperekedwe monga chinthu cha kubadwanso, ndipo popanda ichi,
nsembe ya Khristu inali yopanda mtengo.

Uchimo ukanakhoza kukanidwa ndi kugonjetsedwa kupyolera pokhapokha mwa mphamvu ya munthu wachitatu mwa Mulungu wa atatu, amene akanadza popanda mphamyu ya kuyerekeza, koma mwa chidzalo cha mphamvu ya umulungu Ndi Mzimu umene unapangitsa mtima kuchita chimene mombolo wa dziko lapansi anachita.

Ndi mwa Mzimu kuti mtima umapangika kukhala woyera.

Kupyolera mwa Mzimu wokhulupirira
amasanduka wogawana ndi khalidwe la umulungu.

Khristu wapereka Mzimu Wake monga mphamvu ya umulungu kugonjetsa zibadwa zonse zopaliridwa za uchimo, ndi kutsimikiza khalidwe Lake la lye mwini pa mpingo Wake."(DA, tsamba 671).

Kodi ife tili kudziwa bwanji kuti Mzimu Woyera unali kuchitachita m'nthawi ya Chipangano Chakale? Genesis 6:3

Kodi ndani akadatumiza Mzimu Woyera umene Khristu anaulonjeza ? Yohane 14:26

NTCHITO YAKE YA UMULUNGU

Kodi Ntchito zina za Mzimu wa Mulungu ndizo zotani? Yohane
14:26; Yohane 16:8, 13,14.

KUFOTOKOZA: Ganizirani madalitso amene anadza ndi Mzimu:👇👇

a. Kukuphunzitsani inu zinthu zonse
b. Kukumbutsani zophunzitsa za Khristu.
c. Kutsutsa uchimo m'moyo.
d. Kukutsogolerani inu m'choonadi chonse.
e. Kukusonyezani zinthu zilinkudza (Mphatso ya uneneri).
f. Kulemekeza Khristu.

Zili zomveka bwino kuti kuchokera m'Malembo awa kuti Mzimu Woyera
ndiwo woimira Wake wa Khristu pa dzikolapansi.

Ngati mpingo wina uliwonse uyesa kuika munthu monga woimira Khristu wapadera m'malo mwa munthu wachitatu mwa Mulungu m'modzi mwa atatu, kudzakhala kuyesa kupanga kuika munthu m'malo mwa Mulungu.

Kodi Mzimu Woyera unali nayo mbali yotani mwa kulemba za Malemba Opatulika? 2 Petro 121

MPHATSO ZA MZIMU

Kodi ndi umboni wotani wa kunja umene ukusonyeza kuti mumakhala Mzimu mu mntima mwa wokhulupirira? Agalatiya 5:22, 23

Kodi lye angathe kulamulira bwanji miyoyo yathu? Agalatiya 5:16.

KUFOTOKOZA: "Khristu analonjeza mphatso ya Mzimu Woyera ku
mpingo Wake.

Ndipo lonjezano lili kwa ife monga linalili wa akuphunzira oyamba.

Koma monga malonjezano ena onse anaperamadzitcha kuti ali kufunsira lonjezano la Ambuye; iwo amalankhula za Khristu ndi za Mzimu Woyera, koma osalandira phindu.

Iwo sapereka moyo Kuti utsogozedwe ndi kulamuliridwa mwa zoimira za umulungu.

Ife sitingathe kuchita nawo Mzimu Woyera,Mzimu uyenera kuchita nafe.

Koma ndi angati amene sadzalora ichi. Iwo amafuna kudzichitira ichi. Ichi ndicho chifukwa chake salandira Mphatso ya kumwamba.

Kodi ife tingathe kuumvetsa chisoni Mzimu Woyera? Aefeso 4:30.

Kodi ndi mbali iti ya machitachita imene idzaonekera mmoyo wa MKhristu amene ali wodzazidwa ndi Mzimu? Machitidwe 1:8, Mateyu 28:19,20.

MATHERO A PHUNZIRO LATHU

21/01/2024

PHUNZIRO LA SABATA SUKULU KOTALE M'CHIGAWO CHA AKURU.

PHUNZIRO: 4

LASABATA MASANA

Mutu: YEHOVA AMAMVA
NDIPO AMALANDITSA

Phunziro Lathu Mlungu Uno Tiwerenga Kuchokera mu:
Masalimo 139:1-18, masalimo I21: Masalimo 17:8; Mateyu 23:37: 1 Akorinto 10:1-4, Ahebri 4:15,16.

VESI LOLOWEZA:"lwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva,
Nawalanditsa ku masautso awo onse" (Masalimo 34:17).

Masalimo amatsindika mobwereza-bwerera choonadi choti Yehova Wamkulu, Iye amene analenga ndi kugwiriziza miyamba, akudziululanso Yehova monga Mulungu wa anthu onse, Mulungu amene amayambitsa ndi kusunga ubale Wake ndi antha Ake.

Mulungu amakhala pafupi ndi anthu Ake komanso chilengedwe Chake,kumwamba ndi dziko lapansi (Masalimo 73:23, 25). Ngakhale lye "anakhazika mpando wachifumu wake kumwamba" (Masalimo 103:19) ndipo "amakwera pa mitando" Masalimo 68:4), lye amakhala "pafupi ndi onse akuitanira Kwa Onse akuitanira kwa lye m'choonadi," (Masalimo 143:18). Masalimo akulimbikitsa motsindika choonadi choti Yehova ndi Mulungu wamoyo, amasunga anthu oitanira pa dzina Lake (Masaimo 55:16-22). Masalimo ndi othandiza chifukwa ndi olimbikitsidwa ndi opita kwa Mulungu wamoyo, yemwe amanva ndi kuyankha mapemphero.

Tiyenera kukumbukira kuti yankho loyenera ku kukhala pafupi kwa Yehova limaphatikizira kukhulupirira mwa Iye ndi kumvera malamulo Ake Malamulo Ake. Monga momwe yaonetsera mbiri ya Israyeli, Mulungu sadzalandira mulingo wachikhulupiriro ndi kumvera wochepera apa.

TSIKU LOYAMBA

THUPI LANGA SILINABISIKE KWA INU

Werengani Masalimo 139:1-18. Kodi mwa ulakatuli, salimoli likuonetsera motani mphamvu (Masalio 39:1-6, kupezeka (Masalime 397-12 ndi ubwino wa Mulungu (salimo 139:13-182). Kodi ukulu wa Mulungu ukunena zotani pa malonjezo Ake?

Kodi munayamba mwafunapo mutathandiza munthu wina kona munalibe njira zoti mkumuthandizira? Momwemoso, anthu ena anayesera kukuthandizani koma iwe sanamvetsetse zosowa zani. Anthu ambiri kuphatikizirapo iwo amene amatifunira zabwino,saziwa zosowa zathu, koma Mulungu amatidziwa kwathunthu ndipo amadziwanso
nyengo zoilnse zimene ite tikudutsamo ndi njira zotithandizita. Chotero, malonjezo Ake onena kuti adzathandiza ndi kuombola anthu Ake sanangokhala nkhambakamwa chabe,koma anali otsimikizika ndi okhazikika.

Mulungu anamdziwa mlembi wa masalimoyu kwathunthu komanso modabitsa
Kwambiri, moti ngakhale mimba ya amayi wake sikadatha kumubisa pamaso pa Mulungu (Masatimo 39:13, 15), Mulungu umadziwa za nthawi (Masallino 139:2),amadziwa za munthu wa mkati asanabadwe (Masalimo 139:24) komanso amadziwa za malo (Masalimo 139:3), chotero lye ankadziwa za moyo wonse wa mlembi wa
masalimoyu.

Mulngu amadziwa zinthu modabwitsa chotere chifukwa lye ndi Mlengi
komanso chifukwa choti lye ali pa ubale wachikondi ndi woyandikana kwambiri ndi
anthu, ndipo izi zimaonekera mu chisamaliro Chake chodabwita pa iwo.

Choonadi ichi chodabwitsa chomwe chimati Mulungu amatidziwa mwakuya
chisatichititse mantha koma mmalo mwake chitilimbikise kukhala m'manja ma Yesu
ndi kudalir mu zimene lye watichitira pa mtanda. Chifukwa ife pokhulupirira mwa Yesu tapatsidwa chilungamo Chake "Chilungamo cha Mulungu" mwini Wake (Aroma 3:5,21).

Kupezrka kwa Mulungu kwatsindikidwa poonetsera kuti Mulungu amafikira
ngakhale ku gehena" (sheol, "manda") ndi "mdima" (Masalimo 139:8 I, 12), malo
amene kawirikawiri saonetseredwa ngati malo okhala Mulungu (asalimo 56:13).

Kupezeka Kwake kwaonetseredwanso monga kutenga "mapiko a m'bandakucha (kumamawa) kufika malekezeo a nyanja (kumadzulo) (masilalimo 39:9). Zifanizo zimenezi zikutipatsa choonadi chakuti palibe malo ena aliwonse kumwamta ndi dziko lapansi komwe Mulungu sangatipeze. Ngakhale Mulungu sali gawo la kumwamba ndi dziko lapasi, monga mmene ena amakhulupirira. lye amakhala pafupi ndi zonsezi,chifukwa lye sanangozilenga kokha, koma kuti amazigwirizisanso (onani Ahebri 1:3).

Monga lye amene akudziwa za ife kwathunthu, Mulungu akhoza kutithandiza ndi kubwezeretsa.

Kukhala ndi chidziwitso chatsopano chokhudza ukalu Wake kukupangitsa wolemba masalimoyu kulemekeza Malungu ndi mawu okweza ndipo izi zikulimbikitsa chikhulupiriro chake mma Mulunga. Mlembi wa masalimoyu akulolera
Mulungu amfufuze nmonga njira yochotseta vuto lina lililonse mu ubale wake ndi
Mulungu.

*Ena akhonza kuchita antha polingalire zoti Mulungu amadziwa zonse za iwo, ngakhale zinsinsi zawe zobisika ndi zoipa kwambiri. Nanga tsopano ndi chifukwa chiyani uthenga wabwino uli chiyembekezo chathu chokhacho?*

TSIKU LACHIWIRI

CHITSIMIKIZO CHA CHISAMALIRO CHA MULUNGU

Werengani Masalimo 40:1-3, Masalimo 50:15, Masalimo 55:22,Masalimo 121. Kodi Mulungu amakhudzidwa bwanji mu zochitika zathu za tsiku ndi tsiku?

M'Malembo, Yehova akudzionetsera yekha monga Mulungu wamoyo amene athandiza iwo oitanira pa dzina Lake.

Wolemba masalimoyu akuti, "ndaika Yehova patsogolo panga" (Masalimo 16:8). Chotero, mlembi wa masalimoyu akukhulupirira Mulungu ndi kuitanila pa dzina Lake (Masalimo 7:1, Masalimo 9:10). Yehova adzamumva iye ngakhale atafuula kuchokera "m'mozamamo" (Masalimo 130:1, 2), kuonetsera kuti palibe
chochitika china chilichonse cha m'moyo chomwe chingazembe ulamuliro
wamphamvu wa Mulungu. Chotero, wolemba masalimoyu akufualula kunena kuti
kufulumira kwa nthawi sikudzamuchotsera chiyembekezo chake.

Panopa, mu Salmo 121, wolemba masalimoyu akukondwerera mphamvu ya
Mlengi zomwe zimakhala m'moyo mwa wokhulupirira wokhulupirika, Mphamvu
zimenezi kuphatikizira zoti:

(1). "Sadzalola phazi lake literereke" (Masalimo 121:3) Chifukwa cha phazi" kawiri kawiri chimaimira ulendo wa moyo wa munthu (Masalimo 66:9, Masalimo 119:105. Miyambo 3:23) Mawu a Chihebri omwe amatanthauza "kuterereka amanena za chitetezo chimene Mulungu amapereka ku dziko lapansi (Masalimo
93:1) ndi ku Ziyoni (Masalimo 125:1).

(2). Chifanizo cha Yehova monga Wakusunga lsrayeli sadzaodzera kapena kugona chikutsindika za kukhala tcheru kwa Yehova ndi kukhala wokonzeka Kake
nthawi zonse kutithandiza ife ana Ake (Masalimo 121:3, 4).

(3). Yehova ndi "mthunzi wako (Masalimo 121:5,6) akutikumbutsa mtambo ndi wa nthawi ya ulendo wa Israyeli wochoka ku Aigupto kupita ku Kanani (Eksodo 13:21, 22) Momwemonso, Yehova amapereka kwa anthu Ake mthuzi wa ku thupi komanso wa kuuzimu.

(4). Mulungu ali kudzanja lawo lamanja (Masatimo 121:5). Kawirikawiri tikamati dzanja la manja timanena za dzanja lomwe lili lamphamvu kwambiri mwa
munthu, dzanja lomwe limagwira ntchito kwambiri kuposa linzake
Masalime 74:1 Masalimo 89:13). Apa akunena za kuyandikira kwa Mulungu ndi ntchito Zake (Masalimo 16:8 Masalimo 109:31. Masalimo 110:35).

(5). Chitetezo cha Mulungu kwa anthu Ake chatsindikidwa momveka bwino Salmo 121:6-8. Mulungu adzateteza ana Ake ku zoipa zonse. "Dzuwa
"mwezi sizidzawapanda. Mulungu adzawasungira "potuluka" ndi polowa pawo. Mawu a ulakataliwa akutsindika za chisamaliro cha Mulungu cha nthawi zonse kwa anthu Ake onse.

Kodi nkhani yaikulu ndi iti pamenepa? Wolemba masalimoyu ankakhulipilira mu chisamaliro cha Mulungu wokonda.

Ifenso tiyenera kuchita chimodzi modzodzi.

*Kodi ndi mwa njira zanji momwe inu mungamve chisamaliro cha Mulungu mmoyo wanu wa tsiku ndi tsiku? Nanga mungagwirizane bwanji ndi Mulungu pofuna kumulola kuti agwire ntchito mwa inu komanso chifukwa cha inu?*

TSIKU LACHITATU

YEHOVA NDI POTHAWIRAPO MU NTHAWI YA MAVUTO

Werengani Masalimo 17:7-9, Masalimo 31:1-, ndi Maalimo 91:2-1. Kodi wolemba masalimoyu akuchita chiyani mu nthawi ya mavuto?

Wolemba masalimoyu akukumana ndi mavuto osiyanasiyana, ndipo m'mavuto akewo iye akudalira pa Yehova, amene ndi pothawirapo anthu mu nthawi iliyonse ya mavuto. Chikhulupiriro ndi chisankho chomwe munthu amapanga mwa
chifuniro chake, povomereza ukulu wa Yehova pa moyo wake mu zochitika zonse.
Ngati chikhulupiriio sichingagwire ntchito mu nthawi ya mavuto, ndiyetu icho sichingagwire ntchito kwina kulikonse.

Umboni wa wolemba masalimo ukuti, "Ndidzati kwa Yehova Pothawirapo panga ndi linga langa: Mulungu wanga, amene ndikhulupilira (Masalimo 91:1),umboniwu ukuchokera ku zomwe Mulungu anamuchitira kumbuyo zimene tsopano zikumulimbikitsa mu chikhulupiriro chake chamtsogolo.

Wolemba masalimoyu akumutchula Mulungu monga Wamwambamwamba ndi Wamphamvuyonse (Massatimo 91:, 2),kutikumbutsa za ukulu woposa zonse wa Mulungu.

Wolemba masalimoyu akunenanso za chitetezo chimene munthu angachipeze mwa Mulungu"ngaka" (linga" kapena "pothawirapo" ), "mthunzi"
Masalinmo 91:1), "pothawirapo," "linga" (Meslimo 91:2),"mapiko, "chikopa chochinjiriza" (Masalimo 91:4), ndi "chokhalano (Masalimo 91:9).

Molingana ndi chikhalidwe cha Wolemba Masalimoyu,zifuniro zikuimira malo otetezeka. Kuti munthu adziwe za kufunikira kwa mthunzi iye akungoyenera kuganiza za kutentha kwa dzuwa koopsa komwe kumakhala dera lomwe olemba masalimoyu ankakhala mdziko lapansi, komanso kuti amvetsetse za chitetezo chimene chikopa kapena linga limapereka iye akungoyenera kukumbukira za nthawi ya nkhondo mu mbiri ya Israel.

Werengani Masalimo 17:8 ndi Mateyu 23:37. Kodi ndi chifanizo chanji chimene agwiritsa ntchito pamenepa, nanga chifunizochi chikuimira chiyani?

Chimodzi cha zifanizo zotchuka kwambiri ndi chimene chikunena za kukhala mu mthunzi wa mapiko anu" (Masalimo 17:8,17:8,57:1,63:7), Chifunizo chimenechi chikubweretsa chitonthozo ndi chitsimikizo popereka chitsanzo cha chitetezo cha kholo la mbalame kwa ana ake.

Yehova akuyerekezedwa ndi mphungu imene yaika ana ake pansi pa mapiko ake (Eksodo 19:4,Deutronomo 31:11), komanso thazi lomwe likutsonkhanitsa ana ake pansi pa mapiko ake (Mateyu 23:37).

*Komabe, kodi tingachite bwanji zomwe tsoka latigwera,ndipo tikuona ngai tilibe chitetezo cha Yehova! Nanga ndi Chifukwa chiyani kusokonezeka kumeneku sikukutanthauza kuti Yehova sali nafe?*

TSIKU LACHINAYI

MTETEZI NDI MOMBOLO

Werengani 1 Akorinto 10:14. Kodi Paulo akufotokoza motani nkhani ya alendo wa ana a Israelkuchoka ku Aiguputo kupita ku Kanani? Nanga ndi phunziro lanji la uzimu limene iye akufuna kutiphunzitsa pogwiritsa ntchito nkhani imeneyi??

Werengani Maalmo 14. Kodi maomboledwe a anthu a a Israyeli
kutaluka mu Aigupto, afotokozedwa bwanji mu ndakatulo yomwe ili
pamenepayi?

Masalimo 114 akutipatsa chithunzaithunzi chopatsa chidwi kwambiri cha maomboledwe odabwitsa amene Mulungu anachita poombola ana ake mu ukapolo wa Aigupto mu chipangano chakale ndi chatsopano chomwe kuomboledwa kwa Israeli kuchoka ku ukapolo wa Aiguputo kunkaonedwa monga chidzindikiro cha Mphamvu ya Mulungu yopulumutsa anthu Ake.

M'mavesi awa mu Akoriito, Paulo akuonetsa khani yonseyi monga chifanizo chabe, chizindikiro cha chipulimutso chowe tili nacho mwa Yesu Khristu.

Masalimo 114 akuonetseranso chiombole cha umulumgu kupyolera mu ukulu wa Mulungu monga Mlengi polamulira mphamvu za chilengedwe, zomwe iye
anagwiritsa ntchito kupulumitsa anthu Ake pa ulendo wawo wotuluka mu Aiguputo
to kupita ku Kanani.

Nyanja, mitsinje wa Yordani, komanso mapiri atali ndi afupi
omwe, anafotokoaa mwa ulakatuli za mphamvu ya chilengedwe komanso anthu omwe analimbana ndi a lsrayeli pa ulendo wawo wopita ku dziko la Lonjezano (Deuternomo 1:44. Yoswa 3:14-17), Komabe. Mulungu ndi mwamphamvu kuposa zosezi.

Kunena zona, kwa ambiri a ana a Mulungu mu nthawi zonse ndi m'malo
monse, njira yopita ku Yerusalemu watsoapno imakhala yodzazidwa ndi zoospya zambiri. Masalimo akawalimbikatsa iwo kuti aone mopyoza mapiriwo ndi kuyang'an kwa Mlengi wa kumamba ndi dziko lapansi (Masalimo 121:1).

Cholinga chenicheni cha Masalimo 114 chaonetseredwa mu chozizwa chimene Yesu anachita potontholetsa namondwe pa nyanja komanso ulaliki Wake wouza mpingo kuti usaope, chifukwa Iye walilaka dziko Iapansi (Matea 8:23-27,Yohane 16:33).

Zochita zazikulu zikulu za Malungu zinene Iye anachita mmnalo mwa anthu Ake zikuyenera kulimibikitsa dziko lonse lapansi kunthunthumira pamaso Pake (Masalimo 114:71). Kunthunthumira kumene kukunenedwa pamenepaku kuyenera
kumvetsedwa monga kulandira ndi kulambira Yehova osati kuchita naye mantha (Maalimo 96:9, Masalimo 99:1), Okhulupirira sayenera kuchita mantha chifukwa
Malungu ali ndi mbali yawo.

*Kodi ndi zoopsa zina ziti za uzimu zomwe ife monga okhulupirira timakumana nazo, nanga tingaphunzire bwanji kudalira pa mphamvu ya Yehova kuti lye atiteteze kuti tisagonjere ku zoopsa zimene nafenso tikhonza kukumana nazo monga mmene zinalili ndi olemba masalimowo?*

TSIKU LACHISANU

THANDIZO LOCHOKERA M'KACHISI.

Masalimo 3:4,Masalimo 14:7; Masalimo 20:1-3; Masalimo 27:5;
Masalimo 36:8,Masalimo
61:4; ndi Masalimo 68:5, 35. Kodi mavesi amenewa afotokoza kuti thandizo limachokera kuti?

Mutu wokamba za pothawirapo pa uzimu ndi kuthupi komanso komwe kunachokera thandizo watotokozedwa molingana ndi kachisi.

Kachisi ndi malo a chitetezo,ndi chipulumutso. Kachisi ndi pothawirapo pa anthu ovutika. Kuchokera m'kachisi Wake Mulungu amateteza ana amasiye ndi akazi amasiye ndipo uochokera komweko lye amapereka mphamvu kwa anthu Ake, Pamene akuti "Mulungu awalira m'Ziyoni", mokongola mwangwiro" (Masalimo 50:2),akutanthauza kuti ziweruzo za Mulungu za chilungamo zikulalikidwa ,ndipo mdalitso wa Mulungu ukupitirirabe (Masalimo 84:4, Masalimo 128:5. Masalimo 134:3).

Malo othawirapo a m'kachisi wa Mulungu ndi amapereka chitetezo choposa chimene chingaperekedwe ndi malo ena aliwonse mdziko lapansi Chifukwa
Mulungu amakhala m'menemo.

Kupezeka kwa Mulungu m'kachisimo ndi komwe kumapereka chitetezo, osati kachisiyo ngati nyumba yomangidwa molimba ayi. Chimodzimodzinso, Ziyoni pokhala phiri lomwe Yehova amakhalamo, ilo ndi loposa mapiri ena onse ngakhale palokha phirilo linali laling'ono (Masalimo 68:15,16,Yesaya 2:2).

Pakuti sitili naye mkulu wa nsembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu: koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa (Ahebri 4:15,16).

Kodi ndi mu njira zanji mavesi amenewa akufanana ndi zimene wolemba Masalimoyu akunena zokhudza kachisi?

Chiyero cha kachisi wa Mulunau chikukumbutsa wolemba masalimoyu kuvomereza kuti anthu onse ndi ochimwa ndipo sali oyenera konse kulandira ukoma wa Mulungu, ndipo iye akuti chipulumutso cha munthu chagonera pa kukhulupirika kwa Mulungu ndi chisomo Chake chokha basi (Masalimowo143:2,8,12).

Mwa ife mulibemo kena kalikonse kotipanga kukhala abwino pamaso pa Mulungu. Pamene anthu ali mu ubale wabwino ndi Mulungu kupyolera m'kulapa ndi kulandira chisomo ndi chikhulupiliro
Chake, pokhapo ndi pamene iwo akhoza kufunsa za lonjezano la chiombolo.

Utumiki wa m'kachisi unkaimira chipulumutso chopezeka mwa Yesu.

TSIKU LACHISANU NDI CHIMODZI

KUPITIRIZA PHUNZIRO:

Werengani Ellen G White "The Night of Wrestling" masamba 195-203,mu bukhu la Patriarchs and Prophets.

Kodi ife tingaphunzire chiyani kuchokera ku zimene zinachiitikira Yakobo zokhudza mphamvu ya pemphero lokakamira komanso chikhulupiliro chotheratu cha Mulungu?

Masalino analimbikitsa chikhulupiriro chathu mwa Mulungu amene ndipothawira podalirika kwa iwo amene apereka mitima yawo mmanja Ake amphamvu.

"Mulungu adzachitira zazikulu anthu amene akhulupilira mwa iye lye. Chifukwa chimene chimapangitsa kuti anthu Ake avomereze akhale opanda Mphamvu zambiri ndi chakuti kwambiri iwo amadalira nzeru zawo,ndipo samupatsa mpata woti aonetsere Mphamvu zake mmalo wawo.

Mu chilichonse chowagwera modzidzidzi lye adzathandiza ana Ake okhulupirira ngati iwo ataika chikhulupiliro chawo chonse mwa iye ndi kumumvera mokhulupiririka, *Ellen G White,Patriarchs and Prophets tsamba 493*.

Chikhalirecho, Masalimo ena akhoza kubweretsa chachikulu pamene akulonjeza ndi zosemphana ndi nyengo zomwe ife tikudutsamo. Mu nyengo monga izi ife tikingoyenera kuphunzira kukhulupirira mu ubwino wa Mulungu,womwe waonetseredwa mphamvu pamtanda.

Komanso, nthawi zina masalimo akhoza kugwiritsidwa ntchito kulimbikitsa chiyembekezo chabodza.

Zimene Yesu ananena poyankha zomwe Satani anachita pogwiritsa molakwika Masalimowo 91:11,12,zikusonyeza kuti kuyesa Mulungu ndi kukhulupirira Mulungu zili zinthu ziwiri zosiyana (Mateyu 4:5-7), kapena kufunsa Mulungu mwa mwano kuti achite chinthu chosemphana ndi chifuniro Chake ndi chinthu chosemphana kwambiri ndi kukhulupilira Mulungu.

MAFUNSO OKAMBIRANA👇🏽

1. Pakalasi kambiranani yankho la funso lomaliza la phunziro la Tsiku Lachitatu lokhudza kukhulupirira Mulungu pakati pa mavuto ndi nthawi yomwe zinthu zatisokanekera kwambiri. Kodi munthu angamvetsetse bwanji zimenezi ndi mmene zoterezi zingachitikire kwa anthu,ngakhale m'asalimo muli malonjezo opambana onsewa okamba za chitetezo cha
Mulungu?Taganiziraninso izi: kodi wolemba Masalimo,amene analemba malonjezo opambanawa, anakumanapo ndi mavuto kapena kudziwa anthu ena okhulupirika amene anakumanapo ndi mavuto?

2. Kodi ife tingakhale bwanji ndi chikbulupiriro chathunthu mwa Mulungu mu nyengo zonse (mwachitsanzo, Masalimo 91:14: Masalimo 143:8, 10:
Masalime 145:18-20)? Nanga ndi chiyani chomwe chingatitayitse chikhulupiliro chotere? Kodi ndi chifukwa chiyani kukhulupirira Mulungu mu nyengo za mavuto kuli chinthu chofunikira kwambiri pophunzitsa munthu wina kukhulupirira Mulungu ngakhale m'nyeng zovuta kwambiri?

MATHERO A PHUNZIRO LA

Address

Mayadi
McHinji
MCHINJI

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Pastor Chisomo Khomera posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Place Of Worship

Send a message to Pastor Chisomo Khomera:

Share