11/08/2023
Ekisodo 16:23
Ndipo ananena nao, Ici ñdi comwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; cimene muzioca, ocani, ndicimene muziphika, phikani; ndicotsala cikukhalireni, cosungika kufikira m'mawa.
Mmadera onse amene tiri, Mulungu akutiyankhula tsopano lino kuti tikumbukire kukozetsera Sabata lake. Kugwira ndikumaliza ntchito zanthu zonse ndikuti mmene dzuwa likhale likulowa Sabata nkuyamba, tikhale okozeka kusaliyipisa Sabatalo.
Kukamba zokozekera Sabata, sinkhani yongomaliza kugwira zanthu kokha ai, komanso kudzikozetsera ife eni za Ufumu wa Mulungu popepha chikhululukiro cha Yehova ndikuti pamene tikukayima mmalo ake Oyera tikakhale ndikuchita ma utumiki osiyanasiyana komanso kupembedza tikakhale osambitsidwa mmwazi wa mwana wa nkhosa.
Mulungu Akudalitseni nonse!