Ebnezer ministries

Ebnezer ministries Ebnezer ministries ndi utumiki chabe sukuyimira mpingo uli onse , Lapani ndipo tembenukani mtima chi

30/10/2020

Moni abale ndi Alongo kuli konse komwe muli.

NTHAWI YA UTHENGA

YESAYA 61:1
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine , pakuti Yehova wandizodza ine ndilalikire mawu abwino kwa ofatsa.Iye wandituma ndikamange osweka mtima , ndikalalikire kwa a msinga mamasulidwe , ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa mndende. aleluyaaa!
KODI VUTO LANU NDICHANI ?
Mmene tawerengera mawuwa tikumva za cholinga chimene Yesu khristu anabwerera pa dziko lino lapansi .Cholinga choyambirira akufuna alalikire " UTHENGA WABWINO" Akuti akapolo akhale omasulidwa .Kodi inu okondedwa satana wakumangani magoli otani?

Ngati mukukumana ndi mavuto osiyana siyana , ndipo mwayesera apa ndi apo koma zinthu sizikutheka.Yesu khristu mamuna wamtanda akulankhula nanu lero kuti cholinga chake potifera pa mtanda paja inu ndiine kuti titonthore pa vuto lomwe tili nawo, chofunika mupereke moyo wanu kwa Mulungu .Ndipo mndende zimene mwamangidwa nazo , kaya banja likuvuta , kaya mukufuna machiritso .Ambuye Yesu akuti mukangozipereka inuyo mogonja ndi mozichepesa achosa zonsezo .

Apapa nkhani ndiyoti yesu khristu anabwerera inu ndiine mcholinga choti tisavutike ndi zovuta za dziko lino lapansi .Vuto lanu lirilonse limene likuoneka losatheka taliperekeni kwa mbuye wathu yesu khristu , ndikukutsimikizirani lero kuti mudzamulemekeza ndipo muzakhala mboni .Asing'anga asakunamizeni dziwani kuti kwa yesu kokha nkomwe kuli mayankho . YEREMIYA 33:3 Tawerengeni chapter chimenechi pali mawu achirimbikitso Mulungu kudalitseni nonse ndipo ndipo ndikukufunirani Week end yopambana Amen👏

19/10/2020

Muli bwanji okondedwa kulikonse komwe muli? Kuno kuchigumula ku Blantyre chilichonse chiri bwino.

MAWU ACHIRIMBIKITSO

YEHOVA afikire dera lirilonse pa moyo wanu limene inuyo simungafikire .Ena akhoza kukuonani mwa mtundu wina, koma Mulungu amaona mosiyana ndi munthu .Okondedwa lero nyengo zanu zili mmene zililimo , mukulira komanso kudandaula.koma dziwani ichi , chimwemwe chanu chiza mmamawa Vuto ndiloti sitidziwa za mmawa lathu .Okondedwa musataye mtima simukudziwa kuti YEHOVA akupatsani yankho lotani .Ndikudziwa ndithu kuti pena umafika nkumaona ngati ndi boza zoti ukapempha kwa Mulungu amayankha, Zimafika nyengo zina kupemphera komanso kusala kudya kumene koma mmmmmm nyengo kungofikanso pa Worse moti iwenso nkuyamba kutaya mtima .

Koma mulungu ndiokhulupilika okondedwa , pali zina amangofuna kuti ukulu wake uoneke pa inuyo mukadutsana ndi zimenezo.Ndikuuzeni okondedwa, Mulungu ali wamkulu kuposa vuto lirilonse limene mukudutsamolo .Palibe ankadziwa kuti LAZARO nkukhalanso ndi moyo atagona mmanda masiku anayi.

Ndikuchimva nane kuti mwadikira nthawi yayitali , ndipo kudikira ndikowawa mkutheka mwatopa ndikupemphera chirichonse mwapanga chakhumi kupereka mokhulupirika , Midnights prayers mukuchita ndithu .koma ndikufuna ndikulimbikitseni mulungu sangakusiyeni choncho yankho lanu lilipo ndithu musafooke ndipo musataye mtima .
Daniel ataponyedwa mudzenje lamikango ena onse ankaona ngati athana naye , koma Mulungu ankaona ukulu wake pa anthu onse , YEREMIYA 32:27 Komanso YEREMIYA 33:3 Ndimapezapo mayankho.mulungu akudalitseni nonse , Usiku wabwino. Amen

15/10/2020
15/10/2020

GENESES 18:14
Kodi chilipo chinthu chomkanika YEHOVA ? pa nthawi yoyikidwa ndizabwera kwa iwe , pakufika nyengo yake , ndipo SARAH adzakhala ndi mwana wamwamuna.

Okondedwa, mkutheka munamulandira yesu khristu kukhala mbuye komanso mpulumutsi wa moyo wanu.Ndipo mwakhala mukupemphera nthawi yayitali, ena mwakhala mukutenga ma fasting osiyana siyana pa vuto lomwe muli nawo .koma mpaka pano mayankho pa vuto lanu sanabwerebe ....ALELUYAA!!

Koma ndikufuna ndikutsimikizireni kuti YEHOVA Wamva pemphero lanu , Ndipo panthawi yoyikidwa ayendera nyengo zanu .Apatu tikumva zoti , " Kodi chilipo chomlaka yehova?Tatiyeni tione zimene zinachitika ndi SARAH, anakhala ndi mwana ali ndi zaka zopitilira 90 .Koma ngakhale anakhala nthawi yayitali opanda mwana mmbanja mwawo izi sizinawapangitse kuti asiye kutumikira Mulungu...Aleluyaa..

Mwina mkutheka nanunso pa Vuto lanulo mwakhala nthawi yayitali , ndipo mwatopa ndikupemphera , mulibenso chiyembekezo kuti zidzayenda .Ndikufuna ndikudandaulireni musachoke pamaso pa Mulungu , Dikilirani Zopempha zanu mchikhulupiliro komanso mchiyero .Mulungu wathu ndi Mulungu oyankha sachedwa komanso safulumira , ayankha posachedwa .
Mulungu akudalitseni nonse ndipo akupatseni chokhumba mtima wanu. amen.

11/10/2020

Zimene zikuchitika mseri inu osadziwa YEHOVA wadzidziwa ndipo akumenyerani nkhondo zobisikazo .Matembelero, Zamatsenga, Minyama ndi matsoka aku mtundu wakwanu .Zimene anakunenerani , musazakhalenso pa banja, kaya kuti muzafe mphawi , mukamaima mimba zizingochoka kumangopitisa padera.

Ku banja kwanu kumadabwa inuyo nokha kungokhala waminyama basi.Ana obadwa mbuyo azing' ono anu zinthu zawo zikuyenda koma inu ayi .Ndikuphwasula ndikuononga magoli onse amene satana anamangira moyo wanu ndi mwazi wa YESU KHRISTU mamuna wamtanda.Ndikuswa mabotolo onse amene munayikidwamo kuti musazapange kathu.Moto onyeketsa wamzimu oyera umene anatsitsa Eliya pa Aneneri a Baala utsike malo ena ali onse kumene muliko ndipo unyeketse thembelero lililonse pa moyo wanu.

Mlongo , Ulendo uno ukayima supititsanso padera mudzina la YESU KHRISTU mamuna wa mtanda .Ndikufuna mudzabwere ndi umboni malo ano , Mulungu apanga zadzikulu zimene simunaziyembekezere YEREMIYA 33:3.Dziwani kuti mawu awa ali amoyo ndipo amachita koposa Palibe chida chotsuludwira inu chimene chizapindule, ndi lirime lilironse lotsutsana nanu lizapindure mudzina la YESU KHRISTU pa YESAYA 54:17 Muona kusintha khalani ndi chikhulupiliro Amen.

03/10/2020

1 SAMUEL 17: 45
DAVIDE anati kwa mfristiyo , iwe ukudza kwa ndi lupanga mikondo ndi mnthungo .Koma ine ndafika iwe mdzina la YEHOVA wamakamu , Mulungu wa a nkhondo a Israeli amene iwe unawanyoza .Aleluyaaa.

Okondedwa, Vuto lingakule bwanji pa moyo wanu koma ndi kwabwino kudalira pa YEHOVA. Yes ' mukhoza chita mantha inuyo kuoneka ngati zakuvutani , Chiyembekezo pa moyo wanu chatheratu , koma pa YEHOVA ndife oposa agonjesi a dziko lapansi .

Okondedwa, pamene mwataya chikhulupiliro chanu pamenepo Goliat waima patsogolo ndi Zida zake zoopsa.Muli mchipsinjo chachikulu kuchokera kwa Satana , Ndikuuzeni okondedwa palibe vuto lalikulu msinkhu pamaso pa YEHOVA Itanirani pa dzina lake basi YEREMIYA 33:3 komanso MASALIMO 50:15... Mulungu akudalitse nonse mukhale ndi week end yopambana ..Amen

03/10/2020

Bunthu la NAAMAN zilibe kanthu kuti anali kapolo , analibe maonekedwe abwino, analibe chirichonse komanso anali osaphunzira . Koma Bunthu limeneli linalalikira Machiritso kwa Mbuye wake NAAMAN ...Aleluyaa.
Mulungu akafuna kumugwiritsa ntchito munthu samaona maonekedwe ngati ife ...Amen, pompano pa EBENEZER MINISTRIES pa facebook zikhoza kumaoneka zocheza , Uthenga nkumangowutenga mwachizolowezi koma simukudziwa kumene mungapezereko thandizo pa vuto lanulo.

Zikhoza kumagwetsa mphwayi osamaliza nkomwe kuwerenga uthenga, Post kumayiona kutalika penanso mumangolemba kuti Amen mwachizolowezi .okondedwa simukudziwa ma plan a mulungu ndi otani pa moyo wanu , NAAMAN akananyozera khate lake sakanachiritsidwa .okondedwa dziwani kuti mawu a Mulungu ali ngati lupanga lokuthwa konse konse , Ambiri mwakhala mukulemba makomenti anu kuti uthengawu Abusa wangoti nde nde nde ndi nyengo zanga .dziwani kuti amakhala YEHOVA akuyankhula ndi moyo wanu.

Inu ndiine sitinaonanepo , komanso mavuto anu sindikuwadziwa koma Mulungu akukudziwani malo amene muliwo ngakhalenso nkhawa zanu kuposa ine , Ine ndangokhala chotengera cha mawu ake ..Aleluyaa.

Mawu awa ndikufuna Ndikulimbikitseni , ndikudziwa kuti ndiinu ABUSA, MAYI WAMVANO KAYA NDINU MAYI BUSA ndipo Bible mumalidziwa kuposa ine .Zimenezo siyani kaye pambali Zichepesetseni ngati Nekodemo, muzimaliza kuwerenga komanso kumvetsera kuti mulungu akulankhula nanu kuti chani ..
Mulungu akudalitseni nonse , ndipo ziwani kuti ndiinu m'dalitso pa PAGE lino zikomo👏

24/09/2020

MUSAKUMBUKIRE ZIDAPITAZO NGAKHALE KULINGALIRA ZOMWE ZIDAPITAZO KALE

YESAYA 43:18
Za dzuro zapita, kulephera kwanu kwa dzulo, zomwe zachitika dzulo lija , zitsakugwetseni mphwayi ndipo zisakufooketseni okondedwa.
Munakhumudwa inde ndi zoona, koma zisakudyeni moyo , zisakulandeni mdalitso wanu wa lero.Lero ndi tsiku lina , Dikirani muone kuti YEHOVA akupangirani zotani lero .Zachitika zija , kaya ndi chaka chatha , kaya ndi mwezi watha, kaya dzana mwinanso dzuro , mwaphunzirapo china chake .Lero YEHOVA akumalizitsa ntchito yake yonse pa moyo wanu . Mulungu akudalitseni nonse pano pa EBENEZER MINISTRIES Ndipo akutetezereni mu usiku umenewu Amen

18/09/2020

4 SIMPLE STEPS TO YOUR BREAKTHROUGH....

__Locate the area of ur need to breakthrough, so that this will help u to shoot accurately.
__Search what the scriptures says about your need , there always God's promises for every situation.
__ Purse it with deligence the proof of your desire is pursuit.
__Thank God for it , what so ever things u have prayed for believe that u have recieved , and u shall have them.

Read Jeremiah 33:3 and 32:27 ...

17/09/2020

Muli bwanji okondedwa kulikonse komwe muli madzulo ano, Ine kuno Zisomo zokha zokha Aleluyaa...

Kodi mukudziwa zoti Mulungu akati akukondere ma Interviews anthu 100 kumafuna munthu mmodzi amakhoza kukulemba iweyo ntchito even popanda wachibale aliyense.Anthu akhoza kukuyikira malire kuti zako zada basi , Matenda ukudwalawo suchira , mwinanso mkumati enanso anamwalira ndi matenda omwewo.okondedwa , YEHOVA akati akukondere umachiritsidwa .Ukhoza kuchita ngozi kutembunuzika galimoto koma iweyo mkutulukamo wamoyo , koma wina kungogwa imfa nkukhala yomweyo.

Anthu akhoza kukupangira maupo , kukukumbira mayenje koma YEHOVA akati apange za iweyo Adani ako amenyana okha okha. Mfumu Nebukadnezer ankati akusonkheza moto kwa anyamata aja: Shadreck, Misheck, ndi Abdnego osadziwa kuti Mulungu anali ndi cholinga.

Okondedwa , ndikuuzeni Mzeru za satana amaona ngati akukukhaulitsa , amakuponyera zinthu iweyo ukaziona mkumati apa ndidutsa bwanji? Koma zisomo za YEHOVA Umangoona wadutsamo iwenso nkudabwa kuti zatheka bwanji ndi momwe ndinapsinjikiramu.
Mwinatu okondedwa uli mkati mwa dzenje lozama , ndipo walema ndi kulira , uli mu Gori sukudziwanso kuti zikuthera bwanji .koma YEHOVA apanga za iweyo khalani ndi chikhulupiliro , tangokumbukirani mzimayi uja anangolakalaka kukhuza mphonje ya chovala cha Yesu ndipo anachiritsidwa.Inunso okondedwa malo muliwo mungokhala ndi chikhulupiliro Yehova apanga za inuyo , musaone kukula kwa vuto lanulo koma muone Mulungu akukhala wa mkulu kuposa chipsinjo chanucho. Musayiware page ino tikuyima kwambiri pa YEREMIYA 33:3 .Mulungu akudalitseni nonse ....Amen

12/09/2020

MASALIMO 125:1

Iwo akukhulupirira YEHOVA akunga phiri la Ziyoni losasunthika, likhazikika kosatha.

Munthu amene wapanga chisankho chomtumikira Mulungu wakumwamba, akuyenera kukhala munthu okhazikika muuzimu ndi muchoonadi. Ndizoonadi mphepo ya Namondwe imatha kuombera pa ana a Mulungu , koma DAVIDE akuti " Tikhazikike ngati phiri la Ziyoni ngakhale mphepoyi iwombe pamoyo wathu.

YOSWA 1:9 Kodi sindinakulamulire iwe? Khala wamphamvu , nulimbike mtima , usaope , kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kuli konse umukako . Amen

11/09/2020

Pemphero kwa akhristu nonse pano pa Ebenezer Ministries:

Mulungu wamayankho uyu akuyankheni mapemphero anuwo, Ndipo akumane ndichosowa cha moyo wanu .Afikire Madera onse amene inuyo simunafikire , Ye bogsp akuzebe malire anu .Chirichonse dzanja lanu chitagwire YEHOVA achidalitse kopambana, ALEFA NDI OMEGA chiyambi ndi chitsiridziro .Ndikupemphera kuti ntchito yonse imene anayiyamba pa moyo wanu ayimalidzitsa .kulephera kwa mtundu uli onse Simbalinso yamoyo wanu.

Mwezi uno ukhale okolora , Zisomo za Yehova zivumbe ngati mvula pamoyo wanu.Mulungu adalitse business yanuyo mofanana ndi mmene anachitira ndi YABEZI. kuntchito komwe mukugwirako ndikupemphera kukonderedwa komanso zisomo zochuluka .

Ndikupemphereranso mtendere pa banja lanulo, YEHOVA akupatseni chikondi, kumverana komanso kulolerana pakati panu .okondedwa ndipemphero komanso pembezero langa kuti mwezi uno ukhale olandira zisomo pamoyo wanu.Zisomo zomwe anaziona YOSEFE mnyumba yachifumu zichitike ndi moyo wanu.Mimba youmayo Mulungu akumasuleni ngati HANNA, chaka cha mmawa mmanja mwanu muzanyamura mwana wanu , keep this post and date .ndikupemphera ndi mtima wonse komanso chikhulupiliro musayiwale okondedwa EBENEZER MINISTRIES tikuyima pa YEREMIYA 33:3 Mulungu akudalitseni nonse AMEN.

Address

Mandala

Telephone

+265999031606

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Ebnezer ministries posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share