Kufunafuna chipulumutso

Kufunafuna chipulumutso CHIPULUMUTSO SICHOMPWEKA

20/12/2025

ziwani KUTI chipangano chakale chili magawo atatu

1 Torah
2 prophets
3 writting
Ndipo Torah ndigawo limodzi la magawo atatu amabuku achipangano chakale
Limine lidalembedwa mosogozedwa ndi Mose
Limeneso mu Qur'an amalinena kuti lidapasidwa kwa neneri Mose

Torah ndimabuku monga;Genisis,exodo, levitiko,numero ndi detronom

05/11/2025

*Moni mpingo*
Lero titaziwisanako za *zakudya zoyenera ana a Mulungu*
๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡๐Ÿง‡
Tiyeni tiphunzire limodzi tonse

Poyamba timaona kuti Mulungu sadawasankhire anthu zinthu zoti azidya

Kufiki tidaona kuti Mulungu adausakhira mtundu wake okondedwa mwa Abraham (ana a Israeli)
Levitiko 11:2_โฌ‡๏ธ

*Mwakuthupi komaso motengera nthazi lamunthu ineyo ndimaona kuti Mulungu sadafune kuti azidya zakudya zomwe zimatengedya kuti zodesedwa chifukwa zidali nkhokwe yamatenda*

```Nyama yokufa yokha imapereka chiopsezo choti kutheka yafa ndi poison yemwe munthu angamupweteke atadya
Komano

*komaso*

Mwazina sayasi imatiuzaso kuti nkhumba ili nditizilombo tomwe nditosusana ndiumoyo wamunthu

Mwazina nyama zomwe zidanenedwa kuti ndizodesedwa zimapereka chiopsezo chamatenda kwamunthu kusiyana ndi nyama zomwe zidanenedwa kuti ndizoyelesedwa```

*tipitilize chochi*

Motengera muudzimu ndikuona kuti Mulungu adapereka fanizo Motengera za amitundu ndi akudulidwa

*Awa ndi malamulo omwe adaperekedwa kwa amitundu*

Machitidwe a Atumwi 21:25
*Koma kunena za amitundu adakhulupirirawo, tinalembera ndi kulamulira kuti _asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola,_ ndi dama.*

Machitidwe a Atumwi 15:19
Chifukwa chake ine ndiweruza, kuti tisavute a mwa amitundu amene anatembenukira kwa Mulungu,
Machitidwe a Atumwi 15:20
koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi

*kutanthauza kuti ife amitundu tili oyenera kudya nyama iliyonse imebe imadibwa kupatula *nyama yokufa okha (chifukwa ili ndimwazi)*
Osadya nyama imene yaperekedwa nsembe yamafano _(khristu sapitisa chiweto kwa shehe kuti amusingile komano amadula yekha mudzila la yesu)_
Chifukwa slam amanenera mau omwe chiwetocho amachipereka nsembe kumulungu wawo

Komaso osaphika magazi yomwe atuluka muchiweti popewa mwazi

[05/11, 3:51 am] IBRAH: 1 Akorinto 10:25
Chonse chogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu chifukwa cha chikumbu mtima;
[05/11, 4:03 am] IBRAH: *zakumwa*

1 Akorinto 10:21
Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.

_pazakumwa ndingochenjeza kuti tasamamwe chomwe mabotolo ake adaikidwa zidindo zoopya kapenaso zopanda tanthaunzo lowika bwino_

_osamwa zolezelesa_ Numeri 6:3
azisala vinyo ndi kachasu; asamwe vinyo wosasa, kapena kachasu wosasa, kapena chakumwa chonse cha mphesa, asamwe; asadye mphesa zaziwisi kapena zouma.
Levitiko 10:9
Usamamwa vinyo, kapena choledzeretsa, iwe ndi ana ako omwe, m'mene mulowa m'chihema chokomanako, kuti mungafe; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu;
Tipewe zakumwa zomwe zimakha ndi chemical ya alcoholic

ZIKOMO

04/11/2025

*ziwani kuti masewera ampira ndi tchimo pamaso pa Mulungu*

Sizonse zomwe malemba adaonesa kutsusana nazo pozitchula kuti usamenye mpira ai
Komano mogilisa ntchito malemba ena timapeza tathauzo loti mpira suli oyenera kwa ana a Mulungu
Monga mau amati *chosalungama chilichonse ndi ntchimo* izitu zikutanthauza kuti ngati chinthu chomwe ukuchotacho sichikumusalasa Mulungu ndiye kuti wasangalada oipao monga ; mpira,kuvemara mau/nyimbo/sewero lasamulemekeza Mulungu

Mu BIBLE pomwe pakupezeka mau a mpira ndi Yesaya 22:18
Iye ndithu adzakuzunguza, ndi kukuponyaponya ngati mpira m'dziko lalikulu; kumeneko iwe udzafa, ndipo kumeneko kudzakhala magaleta a ulemerero wako, iwe wochititsa manyazi banja la mbuye wako.

25/08/2025

*WANZERU ATENGAPO KANTHU*
Company ina yomwe imachitisa mpikisano. Itaona K*t mzimayi wina wawina k10,000,000 idatumiza munthu wabambo woti akamukonzekeletse mayi uja zakalandilidwe ka ndalama ija poopa K*ti akamudzidzimutsa atha kumwalira kapena kukomoka ndichisangalaro!!!
Atafika bambo uja adalonjelana ndipo Macheza adayambika
*Bambo* ; Kod mayi munthu atakupatsani 1 million mungatani??

*Mayi* ; ndikhoza kusangalara kwambiri.
*Bambo* ; nanga 5 million??
*Mayi* ; eeeee ndikhoza kupita Ku China ndi banja langa kkkk
*Bambo* ; kkkkk ok nanga nditati ndakupatsani 10 million ??
*Mayi* ; mmmmmm nditha kupita kunja kumakatenga katundu nkumagulitsa.
Atacheza mwakanthawi bambo uja adawauza mayi aja kuti Mwawina 10 million kwacha.Ndipo mmayi adadumpha ndichimwemwe!! Pofuna kumuthokoza bambo uja mayi adati abambo inu ndinu abwino ndikupatsani 1 million pa ndalama yomwe ndawinayi!!
Bambo poyiganizila 1 million adagwa pansi nkukomoka poti kuncthito kwake amalandila 100 thousand ndipo ndikoyamba kuti apeze 1 million pakamozi!!!

# *PHUNZIRO* : bambo uyu amakonzekeretsa mayi kulandira 10 million pomwe iye asali okonzeka kulandila ndi 1 million yomwe!!! Chimodzimodzi masiku ano ambili Tili pa kalikiliki kukonzekeletsa amzathu za moyo wakumwamba pomwe Ife sitili okonzeka kuulandira!! Tikamamuuza mzathu K*ti lapa tidziyamba Kaye talapa ifeyo nkumauza bwino amzathu!!!
Khalani ndi tsiku lopambana ambuye akudalitseni nonse

*AMEN๐Ÿ‘๐Ÿ‘๐Ÿ‘๐Ÿ‘*

14/08/2025

๐€๐ซ๐จ๐ฆ๐š 1:18 ๐๐š๐ค๐ฎ๐ญ๐ข ๐ฆ๐ค๐ฐ๐ข๐ฒ๐จ ๐ฐ๐š ๐Œ๐ฎ๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐ฎ, ๐ฐ๐จ๐œ๐จ๐ค๐ž๐ซ๐š ๐Š๐ฎ๐ฆ๐ฐ๐š๐ฆ๐›๐š, ๐ฎ๐จ๐ง๐ž๐ค๐ž๐ซ๐š ๐ฉ๐š ๐œ๐ข๐ฌ๐š๐ฉ๐ž๐ฆ๐›๐ž๐๐ณ๐จ ๐œ๐จ๐ง๐ฌ๐ž ๐ง๐๐ข *๐œ๐จ๐ฌ๐š๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐š๐ฆ๐š* ๐œ๐š ๐š๐ง๐ญ๐ก๐ฎ, ๐š๐ฆ๐ž๐ง๐ž ๐š๐ค๐š๐ง๐ข๐ค๐ข๐ณ๐š ๐ฉ๐š๐ง๐ฌ๐ข ๐œ๐จ๐จ๐ง๐š๐๐ข *๐ฆ'๐œ๐จ๐ฌ๐š๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐š๐ฆ๐š* ๐œ๐š๐จ;

*๐ฎ๐ญ๐ก๐ž๐ง๐ ๐š*

_๐ฉ๐จ๐ฅ๐ข๐ง๐ ๐š๐ฅ๐ข๐ซ๐š ๐ณ๐š๐œ๐ก๐ข๐ง๐ญ๐ก๐ฎ ๐œ๐ก๐จ๐ฌ๐š๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐š๐ฆ๐š ๐ณ๐ข๐ค๐ฎ๐ญ๐š๐ง๐ญ๐ก๐š๐ฎ๐ณ๐š ๐ค๐ฎ๐ญ๐ข ๐œ๐ก๐ข๐ฅ๐ข๐œ๐ก๐จ๐ง๐ฌ๐ž ๐œ๐ก๐จ๐ฆ๐ฐ๐ž ๐ฎ๐ค๐ฎ๐œ๐ก๐ข๐ญ๐š ๐ค๐จ๐ฆ๐š ๐ฌ๐ข๐ฎ๐๐š๐ญ๐ฎ๐ฆ๐ข๐๐ฐ๐ž ๐ง๐๐ข ๐Œ๐ฎ๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐ฎ ๐ง๐๐ข๐ญ๐œ๐ก๐ข๐ฆ๐จ_
_๐š๐›๐š๐ฅ๐ž ๐ฆ๐ฎ๐ฌ๐š๐ฆ๐š๐›๐ฐ๐ž๐ฅ๐ž๐ฌ๐ž ๐ฉ๐š๐ฆ๐จ๐ฒ๐จ ๐ฐ๐š๐ง๐ฎ ๐ณ๐ข๐ง๐ญ๐ก๐ฎ ๐ณ๐จ๐ฆ๐ฐ๐ž ๐Œ๐ฎ๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐ฎ ๐ฌ๐š๐๐š๐ค๐ฎ๐ฎ๐ณ๐ž๐ง๐ข_
*๐ฆ๐ฉ๐ข๐ซ๐š*
*๐ง๐ฒ๐ข๐ฆ๐›๐จ ๐ŸŽถ ๐ณ๐จ๐ฌ๐š๐ฅ๐ž๐ฆ๐ž๐ค๐ž๐ณ๐š ๐Œ๐ฎ๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐ฎ*
*๐ฆ๐š๐ฌ๐ž๐ฐ๐ž๐ฅ๐จ*
*๐ค๐ฎ๐ฏ๐š๐ฅ๐š ๐ฆ๐š๐ฌ๐ค, ๐ฅ๐ž๐ ๐ž๐ณ๐ข, ๐ง๐๐จ๐ฅ๐จ, ๐ฃ๐ž๐š๐ง๐ฌ ๐ง๐๐ข๐ณ๐จ๐ณ๐ข๐จ๐ง๐ฃ๐ž๐ณ๐ž๐ซ๐š ๐ณ๐š๐ฆ๐›๐ข๐ซ๐ข*

_๐ฆ๐ฉ๐ข๐ซ๐š ๐ฆ๐ฎ๐ง๐ญ๐ก๐ฎ ๐ฌ๐ฎ๐ง๐ ๐š๐ฌ๐ž๐ฐ๐ž๐ฅ๐ž ๐ค๐š๐ฉ๐ž๐ง๐š ๐ค๐ฎ๐จ๐ง๐ž๐ซ๐š ๐ฉ๐จ๐ฆ๐ฎ๐ฌ๐š๐ง๐ ๐š๐ฅ๐š๐ฌ๐š ๐Œ๐ฎ๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐ฎ_ ๐ณ๐ข๐ฆ๐ž๐ง๐ž ๐ณ๐ข๐ค๐ฎ๐ญ๐š๐ง๐ญ๐ก๐š๐ฎ๐ณ๐š ๐ค๐ฎ๐ญ๐ข ๐ฆ๐ฎ๐ค๐ฎ๐ฌ๐š๐ง๐ ๐š๐ฅ๐š๐ฌ๐š ๐’๐š๐ญ๐š๐ง๐š

๐œ๐ก๐ข๐Ÿ๐ฎ๐ค๐ฐ๐š ๐ฆ๐š๐ฎ ๐š๐ค๐ฎ๐ญ๐ข๐Ÿ‘‡
*1 ๐˜๐จ๐ก๐š๐ง๐ž 5:17๐Ÿ‘‰ ๐œ๐จ๐ฌ๐š๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐š๐ฆ๐š ๐œ๐ข๐ซ๐ข ๐œ๐จ๐ง๐ฌ๐ž ๐œ๐ข๐ซ๐ข ๐ฎ๐œ๐ข๐ฆ๐จ; ๐ง๐๐ข๐ฉ๐จ ๐ฉ๐š๐ฅ๐ข ๐œ๐ข๐ฆ๐จ ๐ฅ๐จ๐ฌ๐š๐ญ๐ข ๐ฅ๐š ๐ค๐ฎ๐ข๐ฆ๐Ÿ๐š.*
_๐ง๐๐ข๐ฒ๐ž ๐ง๐๐ข๐Ÿ๐ฎ๐ฌ๐ž ๐ค๐ฎ๐ฉ๐š๐ง๐ ๐š ๐ฌ๐š๐ฉ๐จ๐ญ๐ข ๐ฆ๐ฉ๐ข๐ซ๐š ๐œ๐ก๐จ๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐š๐ฆ๐š,? ๐ง๐š๐ง๐ค๐ก๐š ๐ค๐ฎ๐จ๐ง๐ž๐ซ๐š ๐“๐• ๐ค๐จ๐ฆ๐š๐ฌ๐จ ๐ฆ๐š๐ฏ๐ข๐๐ž๐จ๐ฌ ๐š๐œ๐ก๐ข๐ค๐ฎ๐ง๐ฃ๐š
๐ค๐จ๐ฆ๐š๐ฌ๐จ ๐ฆ๐ฎ๐ค๐ฎ๐ ๐š๐ง๐ข๐ณ๐š ๐ค๐ฎ๐ญ๐ข ๐ค๐ฎ๐ค๐ก๐š๐ฅ๐š ๐ฆ๐จ๐ฒ๐จ ๐จ๐๐š๐ฅ๐ข๐ซ๐š ๐ฆ๐š๐ง๐ค๐ก๐ฐ๐š๐ฅ๐š ๐ง๐๐ข๐œ๐ก๐จ๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐š๐ฆ๐š
๐ค๐ฎ๐ข๐ค๐š ๐ฆ๐š ๐ฌ๐ญ๐š๐ญ๐ฎ๐ฌ ๐จ๐ฌ๐š๐ฉ๐ž๐ฅ๐ž๐ค๐š ๐ญ๐š๐ง๐ญ๐ก๐š๐ฎ๐ณ๐จ ๐ค๐ฐ๐š ๐Œ๐ฎ๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐ฎ ๐œ๐ก๐จ๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐š๐ฆ๐š?

*๐ค๐จ๐ฆ๐š๐ฌ๐จ ๐ฆ๐ฎ๐ฅ๐ข๐ง๐ ๐š๐ฅ๐ข๐ซ๐ž๐ฌ๐จ ๐ฉ๐š๐œ๐ก๐จ๐ฆ๐ฐ๐ž ๐ฆ๐ฎ๐ฆ๐š๐ค๐จ๐ง๐๐š๐œ๐ก๐จ ๐ค๐ฎ๐ญ๐ข ๐œ๐ก๐ข๐ค๐ฎ๐ค๐ฎ๐ฉ๐š๐ง๐ ๐ข๐ฌ๐š๐ง๐ข ๐ค๐ฎ๐ค๐ก๐š๐ฅ๐š ๐ฆ๐ฎ๐ง๐ญ๐ก๐ฎ ๐จ๐ฅ๐ฎ๐ง๐ ๐š๐ฆ๐š ๐ค๐š๐ฉ๐ž๐ง๐š ๐š๐ข๐Ÿ’

Pangani like pageyi
Komaso ugaweni kumagulu oposera atatu

๐Ÿ‘‹GOD BLESS YOU

11/08/2025

from apostle Saiti

*ABALE CHONDE TAWERENGANI CHENJEDZO ILI MOSAMALITSA KWAMBIRI KUTI MUDZIWE ZOMWE ZIKUFUNA KUCHITIKA POSACHEDWAPA*

*AMBUYE ATICHITILE CHIFUNDO*

Ino ndi 2025 ndipo tsopano kuchokera panopa kupita kutsogoloku mpingo ukupita kwao basi ! Nthawi palibepo ndipo ngati sitigwiritsa ntchito mpata omwe tili nao panopo kulibekonso mpata wina ! Ma Simucard akukalembetsedwa kena kutifikitsa pachimake penipeni pa dongosolo la lemba la chirombo !

Koma mtima wanga ukutsautsika kwambiri poona kuti ino ndi 2025 koma anthu adakalimbanabe za sabata ,za ubatizo ,za mabvalidwe ndi zina zoterozo ,kuiwala Mau a pa Ahebri 6:1-2

Okondedwa! Ndikasuzumira ambiri amene tinayamba ano abwerera mmbuyo ,ena ayamba kumeta mmbali ,ena abwerera ku mabanja achiwiri komanso ena abwerera ngakhale kunjira za aneneri onyenga ineyo ndikusowa kunena kuti chani abale !

2018,2019,2020,2021 ndikamakuchenjedzani ndimaona misonzi ikulengeza mmaso mwa anthu ambiri ndipo pena tikamakaliza kulalikira ndimaona anthu akulira pena uthenga umatha tonse tikulira limodzi ,koma pano kulalikira pamtima umachita kumamva kuti anthu awa atopa nao uthenga wa Mulungu !

Abale takuchenjedzani za mkwaturo, takuchenjedzani za gehena , takuchenjedzani za mabvalidwe , takuchenjedzani za kubwezeretsa ,takuuzani za maloto oipa ndikuthandizana mapemphero ,chatsala ndi chani ? Timatenga nthawi yaitali pa media pano kumalalikira mau a Mulungu mmalo motambalala mmipingo mwathu koma ndikuuzani kuti ifika nthawi simudzationanso pano,kuonana kwachiwiri pakakhala pa kulira kwa lipenga!

Anzathu amene mukukhala maiko a kunja ,eee mukukhala kumeneko koma dziwani kuti nthawi yanu yakutherani yokhala kumeneko ndipo ndipemphero langa kuti mukamakhala kumeneko muziikiratu maziko kumaiko akwanu komanso musaiwale kubwerera mwachangu!

Ikubwera Lock down koma sitikudziwa kuti ndiliti koma ulendo uno masewera kulibe ! Anzathu amene mukusunga ndalama zankhaninkhani ku bank ,dziwani kuti posachedwapa simukwanitsa kutenga ndalamazo pokhapokha mutakhala ndi lemba la chirombo! Chotero yetsetsani kuchotsa ndalamazo mwanthawi yake ndipo muonetsetse kuti simunatsale ndi ngongole kumeneko !

Inu amene Mulungu anakudalitsani ndi ndalama zambiri musachedwenso chonde yambani kuthandiza osowa ndipo chuma chanu mukachipeza kumwamba . Ngati muli ndi mangawa ndi munthu mukhululukireni ,musakhale ndi nthawi yosungira mkwiyo. Inu anzanga amene mumadalira chipatala chonde pemphani chisomo cha Mulungu chikukwanireni chifukwa satilolanso kupezeka mu zipatala za boma popanda kulandira lemba la chirombo!

Ndikukumverani chisoni inuyo ogwira ntchito mboma chifukwa ambirinu mudzakakamizika kukatenga lemba la chirombo chifukwa chotetezera ntchito zanu monga zinalili nthawi ya katemera ija,koma ndikuchondererani kuti chonde musapange zimenezo chonde lolani kudzabvutika koma bola tidzakwatulidwe limodzi . Anthu amene mumakhala mtawuni pa nyumba zobwereka ,inde rent ndikupempheni kuti chonde ngati nkotheka kapezeni malo kumudzi ndikumakalima mbewu zina ndi zina nthawiyo ikafika chifukwa ulendo uno microchip sizaphweketsa

Alaliki amene mwangoyamba kumene ,ngati simunamangidwepo dziwani kuti tikagonako ku chichiri ,maula ngakhale kundende zonse zotsautsa ,anzanufe tinabvomereza osati kumangidwa kokha komanso kufa chifukwa cha khristu.Ngati tinalimbana ndi zirombo zija nthawi ya Covid 19 panonso sitikuopa kapena kufooka koma kuimabe nji pamaso pa Mulungu!Ndipo ngati inu mukuopa kufa ndiye beteli musakhalenso mtsogoleri !

Konzekani ! Konzekani ! Konzekani ! Chifukwa anthu onse azadana nafe chifukwa cha dzina la Yesu koma yekhayo amene adzalimbikire kufikira kumapeto ameneyo adzapulumuka ! Chonde abale ndi alongo ndikukuchondererani panopa musaziyese zochezanso ayi koma nthawi tilibe !

Amene mumagwiritsa ntchito masamba a mchezo a TikTok ,YouTube ,Facebook ngakhale WhatsApp samalani kwambiri,makamaka TikTok ndi Facebook pali akamuna amphamvu amene akuyamwa mizimu ya anthu pamenepo ! Pali ziwanda zadama zomwe zikuwalowa anthu ndikumawayambitsa mizimu ya chiwerewere komanso kuwabwezera mudziko tsono ngati uzimu wanu sunakhwime ndibwino osakhalanso pamasamba a mchedzo amenewa koma kungokhala chabe ndi foni !

Inu amene muli pabanja chonde yetsetsani kumapempherera mabanja anu tsiku lililonse chifukwatu ziwanda zamphamvu zalowa mmabanjamu kufuna kumasokoneza ndikumayambanitsa anthu ,Tsoka lake polira lipenga azakupezani mwanyanyalitsana ,ndiye kuti dziwani kuti simudzakwatulidwa . Tiyeni tipepesane ndikukhululukirana nthawi isanathe chifukwa masiku a mdima ayandikira kwambiri ndipo satana sakuchedza ,sakugona ngakhale kupanga masewera akudziwa kuti nthawi yamuthera kwambiri.

Waika ziwanda zamphamvu zoyambanitsa mabanja ,zophwasula mipingo ,kuyambanitsa azitumiki ndi kuyambitsa nkhondo mmaiko pazifukwa zandale . Satana waika kuti anthu akhale pa umphawi wazaoneni cholinga anthu azichedwa kusakasaka chakudya chalero komatu kwinaku ntchito ya Ambuye ikuonongeka . Ndipo musalole kuti ntchito zanu,

05/04/2024

INU AMENE MUMACITA MWAMBO MWA EASTER ,MUNDIUZEKO POMWE ADALEMBA KUTI EASTER MU BAIBULO.

KOMA NDIYE MUMAGOTENGEKETU.

Ife Akhristu timapanga PASAKA ,ena aziti ai Zikufanana ,Koma vetselani Kuno izi ndizosiyana.

PASAKA KUTANTHAUZA KUPITILILA.

EATSER ,kuyimila milungu yacilendo.

Kupanga PASAKA mpaka kumanyamula mtanda ,izi ndiye ziti kupeputsa ifa ya Ambuye wathu Yesu Mkhristu ,zacibwana basi ,masewelo okhaokha ,mulape.

Akhristu muzipanga nao PASAKA osati kupembedza fano iili mudzina la Easter ai.

Cisankho ndicanu ife kwathu ndikumagoyimba malipenga basi.

AKUTI AI KUGEHENA CHOSECHO AKULOWELA KOMWEKO.

Ambuye mutipatse Mzimu Wachidziwitso m'masiku otsiliza ano.

Amen.

Kafukufuku waonetsa kuti anthu ambiri amene anabayitsa covid vaccine padziko lapansi akumakhala ndi vuto mu ubongo, mmis...
25/01/2024

Kafukufuku waonetsa kuti anthu ambiri amene anabayitsa covid vaccine padziko lapansi akumakhala ndi vuto mu ubongo, mmisempha ngakhalenso spinal cord. Chodabwitsa; ambiri amene akupeza vuto limeneli ndi akazi.

Panopa boma la Malawi likusunga 1 million vaccine amene anapatsidwa ku America. Ndie munthu wagona ndi njala, amubayenso covid vaccine, angapulumuke?

Choyamba, tipemphe a boma athetse njala;
Chachiwiri, afufuze chimene chikuchitika kuti anthu ambiri amene abayitsa katemerayu azikhala ndi vuto la neurological disorder.

24/12/2023

*โœ“ MONI KUCHOKERA KWA AMBUYE MULUNGU* *WAMPHAMVUYONSE AMENE DZINA LAKE NDI YESU KHRISTU WAMOYO WA KU NAZARETI*

*โœ“ UTHENGA UWU SUKUIMILA MPINGO ULIWONSE* *KAPENA UTUMIKI ULIWONSE KOMA UKUPITA KWA OKHULUPILIRA* *ONSE .CHONDE TUMIZILANI OKHULUPILIRA ALIYENSE AMENE MUKUMUDZIWA*

*_MAPANGANO AMENE MULUNGU WAKHALA AKUPANGANA NDI ANTHU_*

*1. PANGANO PAKATI PA MULUNGU NDI NOAH ( GENESIS 9:8-17)*

*โœ“ CHIZINDIKILO CHAKE UTA WA LEZA*

*2. PANGANO PAKATI PA MULUNGU NDI ABRAHAMU*
*(GENESIS 17:9-14)*
*โœ“ CHIZINDIKIRO* *CHAKE MDULIDWE*

*3. PANGANO PAKATI PA MULUNGU NDI ISRAYELI* *( EZEKIEL* *20:12-13 )*

*โœ“ CHIZINDIKIRO* *CHAKE SABATA*

*4. CHIZINDIKIRO PAKATI PA MULUNGU NDI ANTHU AMITUNDU* *( AHEBRI 1:1-4)*

*โœ“ CHIZINDIKIRO CHAKE KUBWERA KWA MULUNGU YEKHA KUDZAKHALA MU* *DZIKO* *LAPANSI*

*โœ“ MZIMU WOYERA AKAKUTHANDIZANI KUMVETSETSA UTHENGA UWU ,NDIYE KUTI* *SIMUDZAPUTSITSIDWANSO NDI ZIPHUNZITSO ZONYENGA ZOMWE ZANGOTI* *BWEE PAKATI* *PATHU*

*FUNSO LILILONSE PA UTHENGAWU CHONDE FUNSANI KU +265 993 408834 .AMBUYE YESU KHRISTU AKUDALITSENI NONSE*

*SHALOM AND* *DIVINE GLORY!!!!!!*

*____________________________________________________________________________*

Address

Machinga

Telephone

+265882400876

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Kufunafuna chipulumutso posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Place Of Worship

Send a message to Kufunafuna chipulumutso:

Shortcuts

Share