03/12/2024
LONJEZO LA EMMANUELI
Yesaya 7:14 Onani, namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli. Ndilo losandulika, Mulungu nafe. (Mateyu 1:23)
Yesaya mneneri analosela kuti namwali adzakhala ndi pakati nadzabala mwana wamwamuna amene adzakhala Mulungu pakati pathu.
Ndipo munthawi yoyikika Mariya namwaliyo anawuzidwa ndi mngelo, "Taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu. Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe, chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu. (Luka 1:31,35)
Mngelo anapitiliza kuti, "Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo kunthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha. (Luka 1:32-33)
Zonsezi zinali kupherezela mau aYesaya, "Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife, ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake. Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.
Ulamuliro ndi mtendere wake zidzakhala zopanda malire. Iye adzalamulira ufumu wake ali pampando waufumu wa Davide, ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikiza mwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamo kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza kuchita zimenezi. (Yesaya 9:6-7)