God's Embassy Rabbi Ministries

God's Embassy Rabbi Ministries GEM is a Christ centered Ministry that believes in salvation through Christ and discipling others to develop a good relationship with God on a personal level.

Our desire is to equip more people for Ministerial work so that the gospel is preached to all.

15/05/2026

Faith without work is dead faith

AbaleTiyeni tiyimebe mu chikhulupiliro posatengera nyengo yomwe tidutsamo m'masiku ano wotsiliza. Tili mu nthawi yomwe m...
12/05/2026

Abale
Tiyeni tiyimebe mu chikhulupiliro posatengera nyengo yomwe tidutsamo m'masiku ano wotsiliza. Tili mu nthawi yomwe malemba adachenjezeratu kuti mavuto adzakhala akuchulukirabe. Ndipo ambili adzataya chikhulupiliro chifukwa Cha nyengo zomwe akudutsamo koma ife tiyeni tiyimebe mu chikhulupiliro ndi kusatekeseka pozindikira kuti mavuto onse ndi akanthawi kochepa ndipo tidutsa pokhala Mulungu ali nafe ndipo tilibe mantha.

Yesaya 43:1
1. Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israyeli, Usaope, cifukwa ndakuombola iwe, ndakuchula dzina lako, iwe uli wanga. 2. Pamene udulitsa pamadzi ndiri pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsya; ngakhale lawi silidzakutentha.

07/05/2026

Fellow believers,
Let us live out our faith by speaking positively about who we are in Christ, declaring blessings and not curses, with our words reflecting God's love and life, knowing the small yet powerful tongue can bring life and death.

Stay blessed🙏

04/05/2026
01/05/2026

-highlights

13/04/2026

Mu sabata imeneyi tiyeni tiyende ndi Yesu amene atitsimikizirw ife za Moyo wosatha kwa muyaya.

Performance by: Muntchi choir

đź“–đź“–đź“–đź“–đź“–đź“–đź“–Ezekieli 15:5 "Ngati pamene unali wosapsa sukanatheka kuwugwiritsa ntchito, nanga bwanji utapserera ndi moto, adz...
10/04/2026

đź“–đź“–đź“–đź“–đź“–đź“–đź“–

Ezekieli 15:5 "Ngati pamene unali wosapsa sukanatheka kuwugwiritsa ntchito, nanga bwanji utapserera ndi moto, adzawugwiritsa ntchito bwanji?"

Uwu ndi mtengo wampesa, sunapindule unakali wanthete ndi osapsa, nanga kuli kotani moto utautentha, ndikuupsereza?

Muli bwino choncho, muli wangwiro m'malingaliro, muli ndimphamvu choncho, mukukwanisa kuzichitira nokha zinthu, opani mawa, konzekerani mawa.

Fesani mbewu yabwino m'moyo wanu, khalani pamtendere ndi anthu ndi banja lanu, chitani chokoma, funirani ena zabwino, zichepeseni m'moyo uno, ndipo opani Mulungu.

Kodi mukudziwa kuti m'moyowu pali nthawi ngati iyi:

Yohane 21:18 "Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti uli wamngĘĽono unkadziveka wekha lamba ndi kupita kumene unkafuna; koma ukadzakalamba udzatambasula manja ako ndipo wina wake adzakuveka ndikukutsogolera kupita kumene sukufuna kupita."

Nthawi imeneyi imafika, zomwe sunadzifune zimatha kufika, nyengo imene sunayiyembekeze imatha kufika, moyowu pena mphamvu zimatha, kudziwa kumatha, kuchenjera kumasanduka kupusa, kudzikuza kumachepa.

Ngati mukulephera kukhala bwino munthawi yanu yanthete, moto ukadzakupserezani muzakhala pati!

Tsiku lililonse litengeni kukhala chisomo, ndikuyenda molondola kudziko lapansi. Yanjanani ndi Mulungu, khalani bwino ndi ena, opani mawa!!!
________________________


2 MBIRI 24 : 2"Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku onse a Yehoyada wansembe."Sibwino kuyika moyo wath...
17/03/2026

2 MBIRI 24 : 2

"Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku onse a Yehoyada wansembe."

Sibwino kuyika moyo wathu wa uzimu m'manja mwa munthu wina, tamvani za Yowasi amene anachita zolungama chifukwa Yehoyada anali moyo, atamwalira Yehoyada, Yowasi anabwelera m'mbuyo pamodzi ndi a Yuda onse.

2 Mbiri 24 : 18 "Iwo anasiya Nyumba ya Yehova, Mulungu wa makolo awo ndipo anapembedza Asera ndi mafano. Chifukwa cha kulakwa kwawo, mkwiyo wa Yehova unabwera pa Yuda ndi Yerusalemu."

Mkofunikira kukhazikitsa ubale wathu wabwino ndi Mulungu, umene siudalira kapena kuyang'anira kupezeka kwa munthu kapena ayi, kapena zomwe ena akuchita. Funitsitsani kumudziwa Ambuye mwanokha, ndikukula mu chidziwitso chake tsiku ndi tsiku.

Akolose 1 : 10 "Ndipo tikupempherera zimenezi ndi cholinga chakuti inu mukhale moyo oyenera Ambuye ndi kumukondweretsa mĘĽnjira zonse. Kubereka chipatso pa ntchito iliyonse yabwino, ndi kukula mĘĽchidziwitso cha Mulungu."

_____________AMEN_______________

Here we go, another opportunity to tap into a revelation that transforms life, GEM nothing but Truth all day!!!!"Truth s...
13/03/2026

Here we go, another opportunity to tap into a revelation that transforms life, GEM nothing but Truth all day!!!!

"Truth shall set us free, John 8:32"

Address

Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when God's Embassy Rabbi Ministries posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share