Islamic Guide Malawi

Islamic Guide Malawi this is an islamic page the place where we advise fellow muslims islamically

23/03/2024

Assalaam alykum warahmatullah wabarakaatuh

Monga umo ndinalonjezera iyi ndi hadith yofooka tisamale

330- حديث: ((سُئل النبي صلى الله عليه وسلم عن رجل قبَّل امرأته وهما صائمان؟ قال: قد أفطرَا)).

الدرجة : لا يصح.

Anafunsidwa mtumiki saw kuti mzibambo wina anakuhaga mkazi wake swaum ili mkamwa ndipo mtumiki saw adanena kuti munthu ameneyo wsmasula swaum yake

Hadith imeneyi tisaimvere siyoona ayi

23/03/2024

Assalaam alykum warahmatullah wabarakaatuh

Lero tiyamba kumakuonetsa Ena mwa ma hadith ofooka komanso onama khalani pomwepo ndipo panga like page yathuyi kuti muziphunzira zambiri

Chifukwa anthufe tikumangotsatila kuti Bola ili hadith Inalembedwa chi Arab basi timati ndi hadith imeneyi pomwe sizili choncho

Khalani nafe kuti mudziwe kuti kodi lero tiyamba ndi hadith itiyo

10/03/2024

Assalaam alykum warahmatullah wabarakaatuh!

Nthawi ija ndi iyi today or tomorrow tikhala tikulandila mulendo wabwino kwambiri Ramadhaan.

Komano m'mwezi umenewu pamene ambiri amakhala akukolola zabwino Ena akhala busy kupeza nsambi ponyoza azitsogoleri achisilamu M'malawi muno.

Mwezi uno ndipomwe timaona ma Fatwa opangidwa ndi anthu osasoma ndipo aliyense amakhala Ali ndi kukamwa kwakukuru pochilankhulira chisilamu

Abale tiyeni tizimuopa Allah

Mtumiki Muhammad saw adalankhula kuti⤵️

من أضمن لي ما بين الحييه ورجليه أضمن بي الي ابجنة
Munthu yemwe angapanilile zapakati pandevu ndi miyendo adzatetezedwa naye poikidwa ku jannah

Apa.amatanthauza yemwe angasunhe lilime ndiumaliseche

Tsopano kafukufuku wapeza kuti ngati kuli dziko limodzi lomwe anthu ake amatukwana atsogoleri awo ndi kuno kwathu Kumalawi tiyeni tilape

24/10/2023

Assalaam alykum warahmatullah wabarakaatuh

Nthawi zonse okondeka abale anga achisilamu tiyeni tisaiwale imfa

Mtumiki wathu Muhammad saw adatilangiza kuti,

لا تنسوا الموت فإن الموت لا ينساك

Tisaiwale imfa chifukwa imfa siimatiiwala ayi

31/01/2023

Assalaam alykum warahmatullah wabarakaatuh

Abale okondeka tisaiwale kuti Mtumiki saw adanena kuti⤵️

من يرد الله به خيرا يفقهه في الدين

Munthu yemwe Allah wamufunila zabwino amamupatsa kuchimvesetsa chipembedzo cha Chisilamu.

Mawu awa akubwera kamba koti asilamu ambirife tinangopanga zinthu moloweza nde pamene tikumamva mauthenga osiyanilanapo ndizizolowezi zathu tikumanyoza m'malo mofunsa bwinobwino.

Dziwani kuti munthu yemwe sanapite ku madrass sakuloledwa kutsutsa pamene wamva zokhudza deen

Tiyeni tisamale

31/01/2023

حَدَّثَنَا أَبُو الْيَمَانِ، قَالَ أَخْبَرَنَا شُعَيْبٌ، عَنِ الزُّهْرِيِّ، قَالَ أَخْبَرَنِي عُرْوَةُ، عَنْ أَبِي حُمَيْدٍ السَّاعِدِيِّ، أَنَّهُ أَخْبَرَهُ أَنَّ رَسُولَ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم قَامَ عَشِيَّةً بَعْدَ الصَّلاَةِ، فَتَشَهَّدَ وَأَثْنَى عَلَى اللَّهِ بِمَا هُوَ أَهْلُهُ ثُمَّ قَالَ ‏"‏ أَمَّا بَعْدُ ‏"‏‏.‏ تَابَعَهُ أَبُو مُعَاوِيَةَ وَأَبُو أُسَامَةَ عَنْ هِشَامٍ عَنْ أَبِيهِ عَنْ أَبِي حُمَيْدٍ عَنِ النَّبِيِّ صلى الله عليه وسلم قَالَ ‏"‏ أَمَّا بَعْدُ ‏"‏‏.‏ تَابَعَهُ الْعَدَنِيُّ عَنْ سُفْيَانَ فِي أَمَّا بَعْدُ‏

حضرت ابو حمید ساعدی سے سے روایت ہے کہ انہوں نے بیان کیا کہ رسول اللہﷺ رات کو (عشاءکی) نماز کے بعد کھڑے ہوئے اور تشہد پڑھا اور جیسے اللہ کو لائق ہے ویسی اس کی تعریف کی، پھر فرمایا: اما بعد! زہری کے ساتھ اس حدیث کو ابو معاویہ اور ابو اسامہ نے بھی ہشام بن عروہ سے روایت کیا۔انہوں نے عروہ سے انہوں نے ابو حمید سے انہوں نےنبی ﷺسے کہ آپﷺنے فرمایا: اما بعد اور ابوالیمان کے ساتھ اس حدیث کو محمّد بن یحییٰ عدنی نے بھی سفیان سے روایت کیا اس میں صرف امابعد ہے۔

Narrated By Abu Hummaid As-Sa`idi : One night Allah`s Apostle (p.b.u.h) stood up after the prayer and recited "Tashah-hud" and then praised Allah as He deserved and said, "Amma ba`du."

22/01/2023

قَالَ اللَّهُ عَزَّ وَجَلَّ إِنَّ أُمَّتَكَ لاَ يَزَالُونَ يَقُولُونَ مَا كَذَا مَا كَذَا حَتَّى يَقُولُوا هَذَا اللَّهُ خَلَقَ الْخَلْقَ فَمَنْ خَلَقَ اللَّهَ
Yochokera kwa Anas bin Malik kuti Mtumiki saw adalankhula kuti, Allah wapamwamba anati ndithudi anthu ako sadzasiya kufunsa kuti izi zakhala bwanji nanga izi zili chonchi chifukwa ninji?
Mpaka adzati inde Allah ndimulengi wachilengedwe nanga Allah yo analengedwa ndindani?

Sahih Muslim

20/01/2023

Assalaam alykum warahmatullah

Dziwani kuti mzimayi atha kuzinga chinyama mchisilamu or amuna ali pomwepo

Dziwani kuti kuyang'ana ku Qibla pozinga palibe umboni ogwilika mu deen yathu.

Dziwani kuti ngati muyuda kapena Mkhristu wazinga chinyama nde ife ngati asilamu takaikila ngati watchula dzina la Allah pozinga ifeyo tikuuzidwa kuti titha kutchula Bismillah Allah Akbar then ndi kudya nyamayo

Dziwani kuti utha kuzinga or ulibe Twaharah nyamayo ikhala ya halaal ndithu

12/12/2022

Assalaam alykum warahmatullah wabarakaatuh

الحمدلله الذي بنعمته تتم الصالحات والصلاة والسلام على رسول الله صلى الله عليه وسلم

Uthenga wa padera ndioti,

Asilamu tikhale busy kumapanga zomwe Allah analamulira tisatanganidwe ndizinthu zopeka mu deen.

Mukudana ndimunthu kamba koti samapanga nawo za Arubain

Koma osaswali mu kumayanja a naye kodi asilamu vuto lathu ndichani?

Zoti chisoti ndi sunnah chabe ndipo sunnah yake siyokakamidwanso ayi koma mukuletsa munthu kuswali chifukwa alibe chisoti kodi zimenezi mumazitenga kuti?

Zoti maliseche amunthu wamamuna amayambila pamchombo kulekerera mmabondo timazidziwa koma kapena zimaonedwa kwa inu ngati zabodza?

Zoti ثعلب ابن خطاب ankangovala salu yokha pokaswali koma Mtumiki saw sankamubweza mukuzidziwa kapena ayi?

Nanga zoti swalah opanga sitoko ndi Allah osati munthu Kaya mukudziwapo?

Nanga zoti Mtumiki saw adati Swalah zisanu ndi tsiku la Jumuah mpaka Jumuah Imzake

Nde inu chomaswaliranso Dhuhur pambuyo poti Jumuah mwaswali. Vuto lanu nde mwati kwenikweni ndichani?

Nanga zoti Jumuah inaikidwa mu nthawi ya swalah Ina inu osadabwa?

Tiyeni tiyende Muchiphunzitso chenicheni osati kuyendera zammutu. Mwaumbuli tidzapezeka kuti tili pa deen Ina osati deen yomwe anailandila Mtumiki saw

10/12/2022

Assalaam alykum warahmatullah wabarakaatuh!!!!!!

Kuyamikidwa konse ndikwa Allahu Taala mafuno Abwino apite kwa mtumiki saw a kubanja kwake komanso ndi masahabah ake.

LERO TIYENI TIPHUNZIRE ZA TWAHARAH.
🖋️🖋️🖋️🖋️🖋️🖋️🖋️🖋️🖋️🖋️🖋️

Twaharah ndi liwu la Chiarabu lomwe tanthauzo lake ndi kuyera kapena kuti Ubwino wa kusakhala ndi umve ulionse.

Ndipo Twaharah imayang'anidwa mmagawo anayi⤵️

1 Twaharah yapathupi
2 Twaharah yamuzovala
3 Twaharah yammadzi
4 Twaharah ya pamalo oswalira

Choncho mitundu imafunika kuilabadila pa nthawi yomwe tikupanga za Twahara

Mtumiki saw Adalankhula kuti,

ألطهور شطر الإيمان
Ndithu ukhondi ndigawo lachikhulupiliro chachislamu.
🌴🌴🌴🌴🌴🌴🌴🌴🌴🌴🌴
Komanso Mtumiki saw adalankhulanso kuti, ⤵️
ألطهور مفتاح الصلاة
Ukhondo(kuziyeretsa) ndimakiyi aswalah

Choncho msilamu kuti akhale wa chire watayali pa ibadah akuyenera kukhala waukhondo nthawi zonse.

Nde mmene tafotokozera poyamba muja

Twaharah tikuyenera kuyang'ana mmagawo anayi amenewa.

Ungathe kukhala nditwahara yapathupi koma zovala zilibe Twaharah zikatero swalah sizingatheke.

Utha Kukhala nditwahara m'thupi ndimuzovala koma Malo oswalira ndikukhala opanda Twaharah,
Kapena tingathe kukhala oti tasamba bwinobwino komanso tachapa bwinobwino koma ndikukhala opanda Twaharah chifukwa cha madzi omwe tagwilitsa ntchito anali opanda Twaharah.................................
Ikupitilira

Pangani like kapena comment post yi kuti tidziwe kuti tikamapanga post awerengi alipo ndipo ife tudzalimbikitsika pomalembapo zambiri pa page pano

#

09/12/2022

Assalaam alykum warahmatullah wabarakaatuh 🌴🌴🌴🌴🌴🌴🌴🌴🌴🌴🌴

Tiyeni tifalitse chislam mopanda mantha alionse

Asilamu panopa tikagona tidzadabwa achibale onse atalowa chikristu
Chifukwa muzaka zinozi asilamu ma Daawah tasiya popanda zifukwa zilizonse

27/11/2022

Assalaam alykum brothers and sisters

Muli bwanji kulikonse komwe muliliko?

Address

Area 49
Lilongwe

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Islamic Guide Malawi posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share