25/05/2026
Impact Mozambique
ππππ’π π’ ππ§π¨π πππ πππ¨ π ππππͺπ
Mtsogoleri wa maulaliki mu mpingo wa Seventh-day Adventist mdziko muno abusa a Aaron Shakier athokoza abusa komanso alaliki onse omwe anapita kukalalikira ku Mozambique mu chilinganizo cha Impact Mozambique. Abusa a Shakier anenanso kuti akuthokoza kwambiri Malawi Union Conference, makamaka mtsogoleri wa Union-yi abusa Petro Sukali ndi gulu lonse, chifukwa chopatsa alaliki mwayi wotumikira kunja kwa dziko lino ndi kufalitsa Uthenga Wabwino ku Mozambique.
A Shakier ayamikanso chiyamiko atsogoleri onse a Personal Ministries, ndi atsogoleri onse amene anakonza ndikukonzekeretsa alaliki kuti atenge nawo mbali pa ntchito yopulumutsa miyoyoyi. Adati kudzipereka kwawo, nthawi yawo, komanso khama lawo sizidzapita pachabe, ndipo adawapempherera kuti Mulungu akulitse malire a utumiki wawo ndikuwadalitsa mochuluka.
Kwa abusa onse ndi abale ndi alongo amene anagwira ntchito molimbika ku Mozambique, abusa a Shakier ati akuthokoza kwambiri chifukwa mwachita ntchito yabwino ndi yotamandika. Adawapempherera kuti mvula yamadlitso ichoke Kumwamba iwatsikireni, ndipo Mulungu akukonze malo apadera mu Ufumu Wake. Anathokozanso onse amene anathandizira ndi zopereka zandalama komanso mapemphero panthawi yonse ya Impact Mozambique.
Pomaliza, alimbikitsa mpingo kukonzekera ntchito zikubwerazi za umishonale: OneVoice27 mu 2027, Impact Zimbabwe mu 2028, Impact Malawi mu 2029, ndi Impact Angola mu 2030.
Abusa a Shakier atseka ndi mawu akuti, βMuyezo wa mpingo wopambana si kuchuluka kwa anthu amene amakhala pansi, koma ndi kuchuluka kwa anthu amene amatumizidwa.β Zikomo atumiki aku Malawi. Kwa Mulungu Ukhale Ulemerero.
Olemba : McAllan Mapinda
EMC Media