Ntchisi Peace Ministry Youth Organization.

Ntchisi Peace Ministry Youth Organization. Comminuty Page

27/07/2022

🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹


__________________________________________



🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹

.....

Mmawa wake kadzi wa Mr Eliya sanapite ku ntchito mwachangu Anadikira amuna awo achoke kenako anakamuzusa Emanuel ndikumutulusira zovala zake zonse kuumuza kuti achoke pankhomopo....

......

Emanuel Anayesera kuwauza kuti alibe kopita kulikonse Komabe iwo analimba mtima kuti achoke.

"please madam ndilibe kulikonse koti ndikhale mdimveseni ndagwira mwendo wanu".
"palibe zimenezo iwe ukuchoka lero ndipita ku ntchito mochedwa mpaka nditaonesesa kuti wachoka".

Towera anali Ali mnyumba ndipo akaona chilichonse chomwe chinachitika, iye samasangalasidwa ndizoti Emanuel achoke. Anatenga phone yake ndipo anasaka pomwe panali number ya bwana ake a muna (Mr eliya), ataipeza sanachedwe koma kuwaimbila.

"hello bwana".
"yes... Bwanji kumbiila chilichonse chili bwino bwino koma?".
"ayi akadzi anu sanapite ku ntchito mpaka pano ndipo Akulimbana ndi Emanuel kuti achoke amutulusira chilichonse Maka zovala zake". Analakhula mosisa mawu Towera.
"ukunama zimenezo zikuchitika pa nyumba panga?".
"eya moti mukamabwera tsimuzamupeza Emanuel".
"ndikubwera Pompano".
"chabwino bwana".

Ndi mphuma Mr Eliya Anasazika bwana wawo wankulu ku ntchito Kuja..

"bwanji mukuoneka otanganidwa chonchi mukupita kuti?." anafunsa bwana wa Mr eliya.
"pepani zina zake za zizizi zachitika kwathu ndipo ndikuyenera kupita Pompano".
"OK koma mupange changu chifukwa lero Pali ntchito yambiri".
"ndipo osadanda 10 minutes yokha".

Mr Eliya anakwera mu galimoto yawo kupita. Atafika sanawerengeso zoti alowese ku mpanda galimoto yawo, adamgosika ndikuisiya ku njira komwe Kuja galimoto kulowa..

Apa analingana ndi akadzi awo akufuna kuti azituluka...

"eheee ndiye ukuganiza ukupita kuti usanatuluke Emanuel ali kuti?". Apatu Mr Eliya sanali mocheza sinya zinali kumaso konse.
"sono chimene mukunjira ndichani?".
"ndikuuze iweyo lero sukupita ku ntchito mpaka Emanuel atabwera pankhomo pano komanso ngati sakupezeka iweyo ndi ine banja latha pomwepo".

Mkazi wawo anatuluka kupita ku ntchito kwake, Komabe ankalingalira kuti zikatha bwanji ndi mamuna wake akachoka ku ntchito kwakeko.

Mr Eliya analowa mnyumba ndipo anamuitana Towera.

"ndamva kuitana bwana?".
"eheee mmene Emanuel watuluka apapa wamuona amalowera mbali iti?".
"za ku musiku".
"ngati sakupezeka wina asamuka lero lomwe munthu wanji osafuna kusamala amzake,"

Anakakwera ku galimoto yawo kumusatira Emanuel, amayenda kwinaku akufunsa anthu koma mwasoka sanamupeze.

Analibe plan iliyonse koma kubwelera ku ntchito kwawo.

Anagwira ntchito Komabe mtima wawo sunali mmalo, amaona kuchedwa kuti Nthawi yowerukira ifike.

___

Charity anakakhala bwino kwambiri ndi aunt ake ngakhale amuna awo Mr chitsamba ankamuyamikira kwambiri kuti ndi olimbikira ntchito..

"charity tikupita ku ntchito anawa akasamba ukawasiya ku school wamva koma osaiwala kukawatenga Nthawi ikakwana". Anatero aunt uku akunyamula handbag yawo.
"nditero aunt sindingaiwale".
"OK chabwino, kuli nyemba ku kitchen utakhala kuti wapeza mpata uziteleke ngati ungakhale busy utha kuzisiya ndiye kuti tizadya zomwe zasala zija".
"ndiyesera nditha kuzitereka uku ndikugwira ntchito Zina".
"oohh OK basi ndanyamuka tionana mazulo ano".
"zikomo aunt".

Aunt ake aja atanyamuka anasala pakhomo ndi ana aja Nthawi imeneyi anali akukozeka kuti azipita ku school.

"kodi simunamalizebe muzadye apa nsanga ndikakusiyeni ku school".
"tasala pang'ono".

Kenako anabwera pa sit room kudya breakfast. Atamaliza kudya charity anawatenga kukawasiya ku school, ubwino wake school imene amaphunzira anawa inali pafupi ndi mnyumba yaoyi.

Anabwelera pakhomo kuyamba kugwira ntchito Zina, Nthawi imeneyi mkuti charity anasala yekha pakhomo, Moyo ankaumva kukoma kwambiri ngati asazabweleresno kumudzi.

__

Cathy Moyo wake wa banja umayenda bwino kwambiri ndipo sanankaona vuto lililonse ngakhale anthu amati wakwatiwa ndi agogo ake..

"amuna anga ndimafunatu ndikawaone amayi nanga monsemuja paka pano sindinapite". Anatero Cathy.
"mmmmhhh OK chabwino palibe vuto utha kupita ukakonzeka uchiuza ndikupase ndalama yoti uwagulire zinthu zofunika."
"OK zikomo kwambiri".

Tsiku litafika loti apite akaone mayi ake, Mr Adam amamupasa ndalama ndipo anakagula zinthu zosiyanasiyana kuti awapasa mayi ake komanso anamupasa ndalama zoti akawapase.

"wamaliza kugula zimene umafuna?".
"eya amuna anga". Anayankha Cathy.
"chabwino aaaahhh uyenda ndi driver pa galimoto iyo koma chonde ukabwelere lero lomwe".
"yaaa sindimagona ndithu".

Driver (Martin) anakweza zinthu zija mu galimoto ndipo naye Cathy anakwera ku sogolo limodzi. Martin Analiza galimoto kusonyeza kuti ulendo wayamba.

Ali mu njira Martin ankamuyang'ana Cathy mwachidwi..

"bwanji ukundiyang'ana ngati sukundiziwa"?. Anafunsa Cathy.
"ndikukuziwani ndinu madam anga mkadzi wawo a bwana anga".
"ine si madam ako wamva eti, dzina langa ndine Cathy ndipo utha kumandiitana palibe vuto".
"mmmmhhh koma sindingaitane Pali amuna ako aja ndingapalamule".
"kodi iwe umamuopa amene uja"?
"kwambri chifukwa ndi amene amandipasa ndalama, koma iweyo unalimba mtima bwanji kukwatirana ndi akulu ngati amene aja?". Anafunsa Martin.
"vuto ndi mayi anga ndi amene amandikakhila kwambiri kuti ndipange zimenezi koma tsiku ndi limodzi ndizathawa".
"heeyi atha kukusaka mpaka atakupeza nkulu amene uja".
"aaaahhh iwe ukuyesa ngati ndimakondwera ndikamakhala ndi amene aja".
"Mesa ndi zomwe unasakha iweyo?".
"mmmmhhh ayi kusankha kwa mayi anga ineyo kumene ndizathawireko ndikapeza size yanga basi".

Martin anamuyang'ana momusisa.....

"lakhula wayamba kale kundisisa ndi maso".
"ayi.... Ndilibe mau chifukwa ndiwe mkadzi wa abwana".
"osamapepera nanunso mkadzi wa abwana ndindani kumene tili kuno kuli abwana amene ukuwanenawo kumamasuka ngati mnyamata".
"ndikumakupasa ulemu kwambiri chifukwa chake".
"ine ndiye za ulemu zakozo ayi ndine mwana".
..... Onse anaseka....

Akuyandikira mudzi mwa kwawo (kwa Cathy),anaona Lytton akubwera chakusogolo...

"Martin wamuona mnyamata akubwera ku sogoloyo?".
"eya watani"?.
"tikamuyandikira uime funa ndilakhule naye"?.
"chabwino palibe vuto ndipanga mmene mwanenela".

Atamuyandikira Martin anaimisa galimoto, Cathy anasisa glass...

"hello Lytton..."?.
... Lytton anaima kuyang'ana mu galimoto koma analephera kuti akuzindikire Cathy ndi mmene amaonekera....

"ndinu ndani, mwandiziwa bwanji?". Anafunsa Lytton akudodoma.
"aaaahhh tiziti wandiiwala ineyo".
"kunena monenesa sindikukuziwani".
.. Cathy anaseka kwambiri.....

"ndine Cathy mlongo wake wa Emanuel....
" ndikulota kapena chani, ndi iwedi koma ayi anzathu Bola banja lakuyanjani mpaka mwayamba kuyendera galimoto". Anatero Lytton atasamila galimoto lija.
"si zanga izi za amuna anga... Tatenga ka ndalama aka ukagule Fanta wamva". Cathy anatulusa ndalama yokwana k10, 000 kumupasa Lytton.

Mwamanyazi momwemo Lytton analandira ndikusunga muthumba,

"usananyamuke Cathy ndikufunse Kaye ngati mkotheka ngakhale panopa ndikuziwa kuti si inu type yathu sopano".
"tangofunsani basi".
"kodi Emanuel ukulakhula naye?".
"number yake inanditaika tandipase chonde".
"ndikupasa chonde panopa zikuonesa ngati uli pa ndalama uyesese umutumizireko, chonde ndagwira mwendo wako, akuvutika kwambiri ndikunena pano kumene amakhala wathamangisidwanso".
"bodza limenelo". Anatero Cathy.
"ndili serious ndipo sindikuseka".

Nthawi yomweyo Cathy anaimba phone ya Emanuel mwamwayi inayamba kuitana...

"hello ndine Cathy sister wako..".
"pepani mwini wa phone wachita ngozi panopa tikuthamangira naye ku chipatala".

Cathy anangomva izi misonzi iyamba kugwa kenako anagwa pansi ndikukomoka.

🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹

Tikumane next part
__________________________________________

WhatsApp group +27782176868

Pangan follow Atwa Mw stories

🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹🌹

Address

Ntchisi
Lilongwe

Telephone

+265996514255

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Ntchisi Peace Ministry Youth Organization. posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share