14/04/2022
Msalolele
Chorus
Msalolele Mulungu
Kuti adani andizunze ineyo
Msavomere Yehova andikankhile mudzenje la minga
Kuti adye anawa mulungu, akudalila ine
Kuti avale anawa yehova, akudalila ine.
Mundikhalile thathwe Mulungu
Ndiomboke munkondo wobisika
Mundichile chifundo yehova
Mzimu wanga, mimba yanga zapuwala
Mukandisiya anawa mulungu alila azasausidwa
Mukandisiya anawa mulungu, umasiye uwazunza x2
Mundichitile chifundo mulungu
Adani anga akufuna kundimeza
Mundichitile chisoni yehova
Chigamulo chao chakuta nkhope yanga
Mukandisiya anawa mulungu, akhala opemphapempha
Mukandisiya anawa mulungu, alibe owasamala
Mundikhazike maso mulungu
Ndingagone mutulo{to} tainfa
mundipenyese maso yehova
adani anga anganene ndawalaka
mukandisiya adaniwa mulungu
akondwa azanyoza inu
mukandisiya adaniwa yehova
sazanva zachizuzulo