07/06/2021
*Musaweluze sanga*
Nyamata wina amene adali ochokela banja lochita bwino ngakhale nayeso anali ochita bwino kupatula chuma Cha makolo,anayamba kugwa chikondi ndi tsikana wina amene amachokela m'banja lovutika ngakhale pathawiyi sanadziwe kuti akufunidwa. Makolo anyamata yu pamodzi ndi anzake anamuwuza kuti tsikanayo adzangomulora chifukwa chofuna ndalama osati chikondi, nyamata anawumilirabe kuwonetsa chidwi kwa tsikana osauka uja kufikilana anamufusila,ngakhale tsikana yo zinavuta kuti alore nyamata yo koma pakupita kwa thawi awiliwa anayamba ubwezi osililitsa. Thawi Ina nyamata uja anaganiza zofuna kumuwona tsikana uja ngati amamukonda zenizeni,ulendo wina anayitana bwezi lakelo , nyamata uja anayamba kuwuza mkazi uja kuti wapezeka ndi matenda omwe afe nawo nsanga ngati sipapezeka ndalama nsanga zopitila chipatala Cha kunja, nyamata uja ananenetsa kwa tsikanayo kuti alibe ndalama zopitila chipatala Cha kunja,pomwepo anawuza bwezi lakelo kuti chibwezi Chatha apeze nyamata wina poti iyeyo anfa sanga. Tsikanayo anachoka pamalopo mokhumudwa koma sanayakhule kathu. patatha masiku atatu osawonana kapena kulumikizana kwina kuli kose,makolo komaso anzake anyamatayo anamuwuza kuti timanena amangofuna chuma osati chikondi ayi,pomwepo nyamata uja anakhetsa misozi kunzinvere chisoni. Tsiku la chi 4 tsikana uja anawonekela kwa nyamatayo akuwonetsa otopa, nyamata uja ananfusa tsikana yo kuti unali kuti thawi yoseyi,tsikana anayakha kuti ndinapita kukagulitsa malo omwe agogo anga anawasiya mudzina langa kuti ndalama zo upitire kuchipatala,tsikana uja anapereka ndalama zochuluka kwa nyamatayo pomwepo nyamatayo anakhetsa misonzi akulandila ndalamazo ,
Taphuzila po chani pa khaniyi ?