31/12/2025
PHUNZIRO LA SABATA SUKULU (KOTALE) MUCHIGAWO CHA AKULU
Gawo Loyamba:
Kulumikiza kumwamba ndi Dziko Lapansi Phunzirani za Yesu kuchokera m'Mabuku a Afilipi ndi Akolose
PHUNZIRO 1
Mutu: MULUNGU AMAKHALA NAFE, NGAKHALE MU NTHAWI ZOVUTA
LASABATA MASANA
PHUNZIRO LATHU MLUNGU UNO TIWERENGA KUCHOKERA MU:
Aefeso 3:1; 2 Akorinto 4:7–12; Machitidwe 9:16; Filemoni 1:15, 16; Afilipi 1:1–3.
VESI LOLOWEZA:“Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani!” (Afilipi 4:4).
MBUSA WINA WA MPINGO WA SEVENTH-DAY ADVENTIST anamangidwa pa mlandu umene sadaupalamule. Mbusayo anakhala m’ndende pafupifupi kwa zaka ziwiri. Nthawi yoyamba, mbusayo anali wa chisoni ndi wosokonezeka. Ndi chifukwa chiyani Mulungu analola kuti chinthu choipachi chichitikire mbusayu? Kodi Mulungu samasamala za mbusayu?
Posakhalitsa mbusayu anamvetsetsa kuti Mulungu anamtumiza m’ndendemo kukapulumutsa anthu! Pamene anthu a m’ndendemo anazindikira kuti munthu ndi mbusa, anampempha kuti awalalikire. Chotero, mbusayo analalikira za Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu m’ndendemo. Iye anaperekanso mabuku okamba za Baibulo kwa anthu a m’ndendemo. Iye anabatiza andendewo nawadyetsa mgonero wa Ambuye. Mbusayo anati, “Masiku ena ndinkavutika kugwira ntchito m’ndende muno.
Koma ndinalinso ndi chimwemwe chachikulu mu mtima mwanga. Ndinali wachimwemwe pamene ndinaona Ambuye akusinthanso miyoyo ya anthu m’ndendemo. Apa ine ndinaona Ambuye akuyankha mapemphero anga.”
Anthu ankaganiza kuti Paulo ndi Sila analakwa kanthu kena, komatu iwo sadalakwe konse.
Paulo ndi Sila nawonso, anaponyedwa m’ndende. M’dindo woyang’anira ndendeyo “anawaika m’chipinda cha m’kati, namangitsa mapazi awo m’zigologolo” (Machitidwe 16:24). Iwo ali m’ndendemo, Paulo analemba makalata opita ku ziwalo za mpingo wa m’mizinda ya Afilipi ndi Akolose (werengani Afilipi 1:7 ndi Akolose 4:3).
Mulungu uno, ife tiona zimene zinachitikira Paulo m’ndende. Zowawa zimene iye anakumana nazo m’ndendemo zinampangitsa kudziwa dongosolo limene Mulungu anali nalo pa moyo wake. Chitsanzo ichi cha Paulo chitiphunzitse ife nanga kupitiriza kutumikira Mulungu ngakhale pamene tikudutsa m’nyengo zowawa.
TSIKU LOYAMBA
PAULO, MWAMUNA WOPONYEDWA M’NDENDE CHIFUKWA CHA YESU (AEFESO 3:1)
Paulo analemba makalata kwa Afilipi ndi Akolose. Makalata a Paulo amatchedwa makalata a m’ndende chifukwa iye anawalemba ali m’ndende. (Paulo ali m’ndende analembanso makalata ena opita kwa Aefeso ndi Filemoni.) Ambiri a anthu anzeru zakuya ozukuta Baibulo amakhulupirira kuti Paulo analemba makalata opita kwa Afilipi ndi Akolose ali ku Roma, pafupifupi A.D. 60–62 (werengani Machitidwe 28:16).
*Werengani Aefeso 3:1 ndi Filemoni 1. Kodi Paulo akuti chiyani za nthawi imene iye anali m’ndende?*
Paulo anapereka moyo wake wonse kutumikira Yesu. Ngati Mulungu akadafuna kuti Paulo aponyedwe m’ndende iye anali wokonzeka kukhala m’ndendemo. Paulo akutiuza chifukwa chimene iye waponyekera m’ndendemo. Iye akuti, “chifukwa cha umene ndili mtumiki wa m’unyolo, kuti mmenemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula” (Aefeso 6:20).
Paulo sanaponyedwe m’ndende iye anayenera maulendo nalalikira Uthenga Wabwino. Iye anakumana ndi mipingo komanso anaphunzitsa atumiki ogwira ntchito ya Mulungu. Mwinanso Paulo ankadzifunsa modabwa, “kodi chifukwa chiyani ndili m’ndende? Inetu ndikadakhala mfulu ndikadagwira ntchito zambiri ya Mulungu!”
Kutsogolo kwake, Paulo analowanso m’ndende kachiwiri.
Iye ali m’ndendemo, analemba 2 Timoteo. Chotero, Paulo ali m’ndende analemba pafupifupi makalata asanu a m’Chipangano Chatsopano.
Paulo sakutiudza dzina la mzinda komwe iye anaponyedwa m’ndendeko. Akatswiri ena ozukuta Baibulo amati Paulo anaponyedwa m’ndende mu mzinda wa Efeso kapena Kaisareya. Koma umboni woti Paulo anaponyedwa m’ndende mu Efeso m’Baibulo mulibe. Koma pali umboni woti Paulo anali pa choopsa pa ulendo wake woyamba wa ku Kaisareya.
Koma pamene iye analemba makalata yake yopita kwa Afilipi, ndi pamene iye anali pa choopsa chachikulu (werengani Afilipi 1:20 ndi Afilipi 2:17). Kalata ya Paulo yopita kwa Afilipi ikutisonyeza komwe iye anaponyedwa m’ndende. Koyamba, Paulo akunena za nyumba ya chifumu yapaderadera. Nyumba ya chifumu imeneyi ikhoza kutanthauza kunyunmba kwa kazembe. Yesu anatengedwa kupita ku nyumba ya mfumu mu Yerusalemu komwe anaweruzidwa ndi Pilato (Mateyu 27:27; Yohane 18:33).
Pamene pa mlandu wa nyumba ya mfumu ndi ndende ya Kaisareya komwe Paulo anatumizidwa kukakhala (Machitidwe 23:35). Koma Paulo sakugwiritsa ntchito mawu oti “nyumba ya mfumu yapadera” kukamba za malo ayi. Iye akugwiritsa ntchito mawuwa kunena za anthu. Iwo onse “m’bwalo lonse la alonda ndi kwa onse ena” amena anamva za Yesu (Afilipi 1:13).
Alonda amenewa anali asilikali odziwa nkhondo kwambiri m'gulu la Chiroma. Iwo anali kuteteza mfumu ya Roma komanso kuyang’anira andende.
Kachiwiri, Paulo anatumiza malonje ochokera kwa oyera mtima, ponena kuti, “oyera mtima onse alankhula inu, koma makamaka iwo a banja la Kaisara” (Afilipi 4:22). Chotero, izi zikuonetsa kuti Paulo analemba kalata yake yopita kwa Afilipi ali m’ndende ya ku Roma. Iye anali kulumikizana ndi anthu amene ankakhala ndi kugwira ntchito ku nyumba ya mfumu.
TSIKU LACHIWIRI
PAULO MU NSINGA (2 AKORINTO 4:7-12)
Pamene Paulo ali ku Makedoniya, akuti iye anaponyedwa m'ndende nthawi zochuluka (2 Akorinto 6:5; 2 Akorinto 11:23; 2 Akorinto 7:5). Nthawi yoyamba imene Paulo anaponyedwa m'ndende kunali ku Filipi (Machitidwe 16:16-24). Paulo anaponyedwanso m'ndende ya ku Yerusalemu, koma kwa nthawi yochepa. Ndipo kenaka iye anaponyedwanso m'ndende ya ku Kaisareya.
Palinso pena pamene Paulo akunena zokhudza kuponyedwa kwake mu "ndende" (Filemoni 1:10, 13). Pamene Paulo anali m'ndende ya ku Roma, iye anali kukhala m'nyumba. M'nyumbamo, Paulo anamangiriridwa kwa msirikali. Msirikali ameneyu anali wa gulu la asirikali a paderadera, omwe anali akatswiri odziwa nkhondo kwambiri m'gulu la ankhondo a Chiroma. M'chaka cha A.D. 300, nayenso Mkhrisitu wina wotchedwa Ignatius anamangiriridwa kwa msirikali wa Chiroma.
Pofofokoza za izi, Ignatius anati khalidwe la asirikali amenewa linali loipa ngati "nyama za kuthengo. Iwo akachitiridwa zabwino ndi anthu ndi pamene amaonetsera kwambiri khalidwe lawo loipalo." -Michael W. Holmes, mkozi wa, The Apostolic Fathers (Grand Rapids, MI: Baker Academic, 2007), tsamba 231, mawuwa ndi okonzedwanso. Izi zikusonyeza kuti moyo wa m'ndende unali wovuta kwambiri.
*Kodi ndi chiyani chimene chinampangitsa Paulo kukhalabe wolimba mtima m'mavuto ake a mu nyengo zokhomazo? Werengani 2 Akorinto 4:7-12 kuti mupeze yankho.*
Pamene zinthu zafika povuta, nthawi zonse Paulo amakhala munthu wa chiyembekezo ndi chikhulupiriro. Chiyembekezo ndi chikhulupiriro chake zinali kumulimbikitsa kukhalabe munthu wamphamvu. Satana anachita chilichonse chomwe akadatha kumumvetsa nacho Paulo kuwawa ndi kumutayitsa chiyembekezo. Koma Paulo anadziwa kuti nthawi zonse Mulungu anali ndi iye.
*Kodi ndi madalitso anji auzimu amene anamuthandiza Paulo kukhalabe wolimba mtima mu nthawi ya masautso? Werengani 2 Akorinto 6:3-7 kuti mupeze mayankho.*
Kawiri kawiri, ife timaona zolakwika zathu zakale ndipo timadziwa kuti ndife ofooka. Timaona zinthu zoopsa zimene zikuchitika pa malo otizingulira ndipo sitikhalanso ndi chiyembekezo. Mu nthawi zoterozi, kuti ife tipeze chipambano timayenera kukumbukira mphatso zonse zimene Mulungu amatipatsa. Baibulo ndilo imodzi ya mphatso zofunikira kwambiri zimene Mulungu amatipatsa.
Ilo limatithandiza kuphunzira kuchokera ku zolakwika za ena. Kuchokera m'Baibulo ife timaphunziramo za mmene anthu ena anagonjetsa mu nkhondo yolimbana ndi choipa. Mulungu amatipatsanso Mzimu Woyera. Mzimu Woyera "amatithandiza kukhala moyo wofunana ndi wa Mpulumutsi. Mzimu amapanga moyo wathu kukhala moyo wopanda chodetsa ndi wa chiyero.
Iye amatithandiza kuti m'mitima mwathu tikhale ofanana ndi Mulungu. Yesu anatipatsa Mzimu Wake kuti atithandize m'mitima mwathu kugonjetsa mu nkhondo yolimbana ndi uchimo komanso choipa. Mzimu amatithandiza mpingo wa Mulungu poudzaza ndi moyo wa chiyero komanso chikondi Chake." -Ellen G. White, The Desire of Ages, tsamba 671, mawuwa ndi okonzedwanso.
TSUKU LACHITATU
PAULO MU FILIPI (Machitidwe 9:16)
Paulendo wake wachiwiri wokalalikira Uthenga Wabwino, Paulo anayenda ndi Timoteo komanso anzake ena. Posakhalitsa, Mzimu akuletsa Paulo kuti asaolokere ku Asiya (Asia Minor) (Machitidwe 16:6). Asia Minor lero amatchedwa Turkey. Usiku umenewo, Paulo akulota loto. Mu lotolo, iye akuona munthu wina wochokera ku “Makedoniya.
Munthuyu adaima pamenepo nanena kwa Paulo, "muolokere ku Makedoniya kuno, mudzathitangate ife'” (Machitidwe 16:9). Pomwepo, Paulo ndi anzakewo anayenda pa nyanja kuchokera ku Trowa. Pa ulendowo Paulo anali ndi Sila, Timoteo, ndi Luka. Luka anawapeza anazekwo ku Trowa (Machitidwe 16:11). Paulo ndi anzake wo anayenda pa nyanja kupita ku mzinda wina wa m'dziko la Greece. Koma kumeneko iwo sanalalikire. Ndipo gululo linapita ku Filipi.
Filipi unali "mudzi wa ku Makedoniya, waukulu wa m'dzokomo." (Machitidwe 16:12). Filipi unalinso mzinda wolemekezeka kwambiri pakati pa mizinda ya ufumu wa Roma. Anthu okhala mu Filipi adali ndi ufulu woponya voti pa chisankho kapena kukhala ndi malo a munthu mwini mofanana ndi nzika za Roma zomwe zinkakhala mu Italy. Ndiponso Afilipi sankalipira misonkho ina. Aliyense wobadwira mu mzinda wa Filipi anali nzika yeni yeni ya ufumu wa Roma.
Filipi anali malo wofunikira kwambiri womwe anthu amaima ndi kupumula pa ulendo wopita ku Via Egnatia. Via Egnatia unali msewu wofunikira kwambiri wolumikiza Roma ndi maiko a kummawa. Chotero, Paulo adafuna kukhazikitsa mpingo mu Filipi. Mpingo wa mu Filipi ukadathandiza Paulo ndi gulu lakelo kulalikira Uthenga Wabwino ku mizinda ina yapafupi. Ina ya mizinda imeneyi ikuphatikizira Amfipoli, Apoloniya, Atesalonika ndi Bereya (werengani Machitidwe 17:1, 10).
Mu nthawi ya Paulo, Afilipi anali kulankhula chilankhulo cha Chilatini. Koma ku misika ndi m'mizinda yozungulira anthuwo anali kulankhula Chihelene. Luka akutiuza mmene Paulo ndi gulu lakelo analowera mu gulu la anthu amene anali kupemphera mphepele mwa mtsinje. Kumeneko, Lidiya pamodzi ndi antchito ake ndi ena okhala nawo m'nyumba mwake, analowa Chikhrisitu (Machitidwe 16:13-15). Lidiya anali mkazi wochita malonda amene ankagulitsa nsalu za chibakuwa.
Lidiya anagwiritsa ntchito ndalama zake kuthandiza ntchito ya Mulungu imene Paulo ankagwira. Mu nthawi yomwe Paulo ndi Sila anali mu Filipi, iwo kwambiri anakhala m'ndende. Kukhala kwawo kwa ndendemo kunapangitsa mdindo woyag'anira ndende kulowa Chikhrisitu. Anthu onse a panyumba pake, nawonso analowa Chikhrisitu!
Mzinda wa Filipi unali wofunikira kwambiri ku mpingo wonse. Mpingo wa mu Filipi unathandiza anthu a Mulungu kufalitsa Uthenga Wabwino ku Ulaya. Kumena zoona, Paulo ndi gulu lake anasautika chifukwa cha chikhulupiriro chawo mu Filipi. Mulungu akhoza kugwiritsa ntchito masautso athu ndi cholinga chofuna kukhudza mitima ya anthu ndi Uthenga Wabwino.
*Werengani Machitidwe 9:16. Kodi vesili likutithandiza bwanji kumvetsetsa masautso amene Paulo anakumana nawo? Nanga nafenso likutithandiza motani?*
TSIKU LACHINAYI
PAULO NDI KOLOSE (Filemoni 1:15, 16)
Baibulo silikunena kuti Paulo anafikapo mu mzinda wa Kolose. Koma ife tikudziŵa kuti Epafra ndi amene anakhazikitsa kumeneku (Akolose 4:12). Epafra anali munthu woyamba kulalikira Uthenga Wabwino wa Yesu mu mzinda wa Kolose (Akolose 1:7). Funso nkumati, kodi Epafra analowa bwanji Chikhristu? Kunena zoona, ife sitikudziwa. Mwina Epafra analowa Chikhristu nthawi imene Paulo anali kukhala mu mzinda wapafupi, wotchedwa Efeso, pakatikati pa zaka za A.D.-50.
Chifukwa cha ntchito ya Paulo “kotero kuti onse akukhala m’Asiya anamva mawu Ambuye, Ayuda ndi Ahelene” (Machitidwe 19:10; yerkezani ndi Machitidwe 20:31). Buku la Chivumbulutso likutiuzanso kuti otsatira a Mulungu analalika Uthenga Wabwino ponse ponse mu Asiya (Chivumbulutso 1:4). Kodi ndi chifukwachi chiyani iwo anapambana? Yankho ndi loti, chifukwachi cha ulaliki wa Paulo.
Anthu anamva uthenga woyamba kuchokera kwa Paulo mu Efeso. Efeso unali mzinda wofunika kwambiri mu Asiya komanso ku doko lalikulu, chotero, Epafra ananva Paulo akulalikira mu Efeso. Iye anakhalanso mmodzi wa anthu ogwira ntchito limodzi ndi Paulo. Ndipo kenaka Epafra anabwerera kwawo ku Kolose nalalikira Uthenga Wabwino kumeneku.
Mzinda wa Kolose uli pa mtunda wa zipumulo khumi ndi mphambu zisanu (15) kum’mera cha kum’mwera kwa Laodekaya.
Anthu a zotumbatumba tsopano ayamba kukumba mu mzinda wa Kolose. Chotero, kufikira lero ife sitikudziwa zambiri zokhudza mzindawu. Tikudziŵa kuti mu mzindawu munali kukhala Ayuda pafupifupi 10,000. Ndalama zachitsulo za ku Kolose zimasonyeza kuti mu mzindawu munali anthu opembedza milungu yochuluka kwambili.
Chotero, Akhristu anali kukumana ndi mavuto ochuluka polalikira Uthenga Wabwino mu mzindawu. Komanso, mu mzinda umenewu zinali zowuta kwa Akhristu kukhala moyo womvera Mulungu. Filemoni anali mmodzi wa Akhristu amene anakhalabe mu Kolose. Mwina Filemoni analowa Chikhristu mu nthawiyi yofanana ndi Epafra.
*Werengani Filemoni 1:15, 16. Werenganinso Akolose 4:9. Kodi Paulo anampempha Filemoni kuchitira Onesimo chiyani?*
Lamulo la Chiroma linati Paulo anayenera kubweza Onesimo kwa mbuye wake, Filemoni. Koma Paulo anapempha Filemoni kuchitira Onesimo chifundo. Onesimo anali kapolo wa Filemoni. Koma Paulo anapempha Filemoni kuti amtenge Onesimo monga mbale wake mwa Yesu Khristu (Filemoni 1:16).
*Kunena zoona, ukapolo ndi chinthu choipa. Ife tikadakonda kuti Paulo auze Filemoni amasule Onesimo kukhala mfulu. (Mu nthawiyi ukapolo mu America, Ellen G. White anauza Akhristu a mpingo wa Seventh-day Adventist kuti asamatsatira lamulo lokhudza kapolo wothawa mbuye wake. Lamuloli linkalamula anthu kubweza akapolo othawa kwa ambuye awo.) Momwemo, kodi ife tingafotokoze motani ganizo la Paulo lopita kwa Filemoni?*
TSIKU LACHISANU
MIPINGO MU FILIPI NDI KOLOSE (Afilipi 1:1–3)
*Werengani Afilipi 1:1–3 ndi Akolose 1:1, 2. Kodi Baibulo likutiuza chiyani zokhudza mipingo ya mu Filipi ndi Kolose? Nanga ndi chifukwa chiyani chidzivitsoche chili chofunikira kwambiriri?*
Paulo m’makalata ake kawirikawiri akupereka malonje kwa Akhristu powatchula monga oyera mtima. Chifukwa chake ndi choti iwo anali atabatizidwa mu mpingo. Ubatizo unali kusonyeza kuti iwo anali olekanitsidwa ndi njira za moyo wawo wakale nakhala anthu a Mulungu apadera. Namonso mu Chipangano Chakale, Mulungu anasankha Aisrayeli kukhala anthu Ake apadera.
Mulungu analamula ana a Israyeli kulandira mdulidwe monga chizindikiro. Mdulidwe unkachitika pa ana aamuna a Israyeli. Chizindikiro chimenechi chinkasonyeza kuti Aisrayeli anali olekanitsidwa ndi anthu a mitundu ina, ndiponso iwo anali anthu a mwini Wake Mulungu. Iye ankawatenga iwo monga chuma chake chapadera. Iye anafuna Aisrayeliwo akhale oyera (Eksodo 19:5, 6; yerekezerani 1 Petro 2:9, 10).
Momwemonso, Mulungu akufuna Akhristu nawonso akhale oyera. Ubatizo umasonyeza kuti ife ndi a Mulungu mwini.
Tiyeni tiyerekezere malonje a Paulo m’kalata yake yopita kwa Akhristu mu Filipi ndi malonje a m’kalata yake yopita kwa Akhristu a mu Kolose. Paulo akulemba makalata ake kwa akulu akulu a mu Filipi, pamodzi ndi “oyang’anira ndi atumiki” a mpingo (Afilipi 1:1). Paulo akulembanso kwa “oyera mtima onse mwa Khristu Yesu” amene akukhala mu Kolose (Akolose 1:2).
Pamene Chipangano Chatsopano chikunena za “abale okhulupirika,” ife timawerenga anthu amene awo amene akugwira ntchito ya Mulungu yapadera mu mpingo (werengani Aefeso 6:21; Akolose 4:7; ndi 1 Petro 5:12). Chotero, Paulo akulankhula kwa ziwalo za mpingo pamodzi ndi akulu a mpingo mu Filipi ndi mu Kolose. Mu zigawo zina za Baibulo, ife timamva za ntchito ya Mulungu imene akulu ampingo akugwira mu mpingo (Werengani 1 Timoteo 3:1–12 ndi Tito 1:5–9).
Ntchito zosiyanasiyanazi zimathandiza kumvetsetsa kuti utsogoleri unali chinthu chofunikira kwambiri mu mpingo wa Mulungu kuyambira kumayambiriro kweni kweni.
Paulo anaphunzitsa ntchito Timoteo, Epafra, ndi Akhristu ena kukhala atsogoleri a mipingo ya kwawo. Paulo ankadziwa kuti kuphunzitsa atsogoleri inali ntchito yofunika kwambiri. Akulu a mpingo anathandiza Paulo kulalikira Uthenga Wabwino m’mizinda. Paulo anali ndi ndondomeko yolalikira Uthenga Wabwino komanso kupereka upangiri kwa atsogoleri a mpingo.
N’choncho atsogoleri amene anayambitsa mpingo wathuwu wa Seventh-day Adventist anatsata dongosolo lomweli. Zaka zambiri zakumbuyo, Paulo asadalembe makalata ake opita ku mipingo ya Filipi ndi Kolose, mpingo wa mu Yerusalemu unali kutsata kale dongosolo limeneli (werengani Machitidwe 6:1–6 ndi Machitidwe 11:30). Mpingo wa mu Yerusalemu “unali chitsanzo cha utsogoleri kuti mipingo ina itsatire.”—Ellen G. White, The Acts of the Apostles, tsamba 91, mawuwu ndi okonzenso.
TSIKU LACHISANU NDI CHIMODZI
KUPITIRIZA PHUNZIRO:
“Mulungu anasankha inu kuti mupulumutsidwe. Iye akufuna kukukupangani inu kukhala woyera. Chikhulupiriro chanu mu choonadi cha Baibulo chidzikupangani kukhala oyera. Chotero, khalani amphamvu… Ngati mumvera Mulungu, anthu adzalimbana nanu chifukwa cha chikhalupiriro chanu. Inu musakwiye pamene wina wakuputani. Musamabwezera. Khalani olimba mwa Yesu.
Inu musadalaule pa zimene zina akukunenani. Inutu simukuyenera kuwaletsa kuchita zimene akufuna kuchita. Ntchito yanu ndi yochotsa kunyada konse mu mtima mwanu. Chitani ntchito imeneyi ndi mtima wanu wonse komaso mphamvu zanu zonse. Inu simukuyenera kugwetsedwa mphwayi. Khulupirirani mwa Mulungu. Kodi ntchito yanu ndi ntchito yofunikira bwanji? Mwina inu simungathe kudziwa yankho la funsoli m’moyo uno. Komabe panopa inu mukhoza kudziwa mtengo wa moyo wanu: Mulungu anapereka Mwana Wake kuti akupulumutseni.
Izi zikuwonetsa kuti inu ndi a mtengo wapatali kwambiri…”
“M’Khristu woona aliyense adzadutsa m’nyengo zovuta. Satana adzayesetsa kukulepheretsani kukhala ofanana ndi Khristu mu mtima mwanu. Koma yang’anani ku mtanda. Pamene tikukayang’ana ku mtanda, ife tidzapambana. Yesu akutiphatsa lonjezo ili: ‘Sindidzakusiya konse, ngakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.’ (Ahebri 13:5). Ndipo ‘onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawiyi ya pansi pano’ (Mateyu 28:20).”—Ellen G. White, mu The Youth’s Instructor, November 9, 1899, mawuwu ndi okonzenso.
MAFUNSO OKAMBIRANA:
*1. Paulo anaponyedwa m’ndende nthawi zochuluka. Iye sanalakwe kena kalikonse. Kodi inu mumamva bwanji ngati anthu ena akukuchitirani zinthu zopanda chilungamo kapena kukuchitirani nkhaza? Nanga ndi malonjezo ati a m’Baibulo amene amakuthandizani mu nthawi zovutazi?*
*2. Tertullian anali mtsogoleri wa mpingo wa Chikhristu woyambirira. Pamene Aroma anali kuvulaza ndi kupha Akhristu, Tertullian analankhula mawu awa, “Nthawi imene inu mukupha ambirimbiri pakati pathu, ndi pamene chiwerengero chathu chimanka chikulira—kulira. Mwazi wa ophedwawo uli ngati mbewu.” Pa nthawi yokhayokhayo, mtopola umene unkachitikira Akhristu nthawi zina unkapangitsa kuti ntchito ya Mulungu ikhale yovuta kalero, komanso ngakhale lero. Kodi ife tichite chiyani kuti tithandize Akhristu amene akuchitidwa ntopola chifukwa cha chikhulupiriro chawo?*
*3. Taganizireni za mmene Paulo anavutikira. Tsopano werengani vesi loloweza la mlungu uno. Kodi mawu oti, “kondwerani mwa Ambuye nthawizonse” akutanthauza chiyani? (Afilipi 4:4). Nanga ife tingakondwerera bwanji mwa Ambuye nthawi zonse? Nanga bwanji pamene wokondedwa wanu wadwala kapena kumwalira kumene? Kapena pamene mwachotsedwa ntchito? Kapena pamene mukumva ululu woopsa kwambiri? Ife monga Akhristu, kodi ndi chiyani chimene chiyenera kutipanga kukhala okondwera nthawi zonse?*
MATHERO A PHUNZIRO LATHU.
Bronnex C PHIRI MPESA SDA DURBAN In list 3 items