22/05/2026
Uphungu wanga munawunyoza.
Kudzudzula kwanga simunakusamale.
Ndiye inenso ndidzakusekani mukadzakhala mΚΌmavuto;
ndidzakunyogodolani chikadzakugwerani chimene mumachiopacho.
Chiwonongeko chikadzakugwerani ngati namondwe,
tsoka likadzakufikirani ngati kamvuluvulu,
mavuto ndi masautso akadzakugwerani.
βTsono mudzandiyitana koma sindidzayankha;
mudzandifunafuna, koma simudzandipeza.β
Miyambo 1:25-28