29/03/2025
KODI PEMPHERO LANU LIMAFIKA KUMWAMBA? MIZIMU YA MULENGALENGA KULANKHULA KUDZERA PA MZINDA WOYERA
Ife a mulengalenga. Mulengalenga muli miyamba imene anthu akamapemphera [pemphero] limayenera lidutse kuti likafikire ku mpando wa chifumu. Kuli miyamba 29, munthu akamapemphera amayenera adutse kukafifa ntambo 29. Amene amakafika ntambo 29 ndi achikulire wa[ILLIMAKHATHUMA]. Ena amangopalapasa. Kumakhala ma tcheni kuyambira pa 1, munthu amayenera adule ma tcheni. Munthu akafika ku ntambo 29 mpingo wake umakhala woopsya, sipachitika zachibwana, ana ake amakhala oopsya. Ndi chifukwa sitilora kuti munthu afike ku ntambo 29, ndi chifukwa anthu mmipingo akulankhula malilime oloweza, ophunzitsidwa osadziwa kuti akuchokera kwa dziwanda. Timawankha mapemphero ambiri safikira ambiri amene amayeselera limalekeza pa ntambo 9 chifukwa chake ambiri amangopalapata. Pemphero limene sitiwankha ndi la achikulire wa[ILLIMAKHATHUMA] chifukwa pemphero lawo likamabwera ndi ziphaliwali, kudula ma tcheni. Tinene kuti timaopa achikulire ndi mpingo wawo chifukwa upeza kamwana kakang'ono kakapemphera kamafika Ku ntambo 16. Chifukwa pemphero lawo ndi la moyo timaopa pemphero la moyo, pa mpingo pamene pali cha moyo, m'busa, prophet ali ndi chamoyo. Takhala tikuwankha mapemphero ife timakhalira. Munthu nkumati ndamva mkati kuti ndapemphera. Haha pemphero sitimva mkati lokumva nkati ndi la level 1-4, nkumati ine ndinapemphera ndipo malilime anabwera osiyana siyana kuchoka awa kubwera malilime ena. Nkumati ndinamva kudzodza, kudzodza kumakhala kosiyasiyana kumakhala tu kupusitsidwa mpemphero. Alipotu azibusa ena amapemphera 3 hours ife timangoseka. Pemphero timaopa ife ndi losakaniza ndi mau osati kupemphera yankho uli nalo kale. Pemphero lanji lopanda wina kulankhula po. Kupemphera osamva liu la Mulungu. Ambiri tu amapemphera ndi dzimau nkumati koma nde lero kunali pemphero, intercession inabvuta, timangowankha. Unamva liu lake liti kuti "pemphero lako lafika ku mpando Wanga?" Tidawankha la Daniel, timawankha olo ukafikirako ndeno mayankho akamatsika timawankha ngati wasuntha pa line. Timamanga nthenje. Pa Mzinda tu pali pemphero chifukwa mwini wake likamabwera limabwera ndi ziohaliwali nde ana nkosabvuta kudutsa chifukwa amakhala kuti walambula nseu zing'aning'ani zadutsa ena afooka mbalimu okomoka akomoka kuti adzuke pamatenga nthawi. NDE mumati mumapemphera mmipingomu muti aleluya mwapisila mmatumba, kudzodza mulibe, zosakunkhudzani mukuyang'ana kachibwenzi. Convener akuyang'ana nthawi amvekere tilambira kwa 10 minutes. Kumayang'ana nthawi ikangokwana - Amen mukatero mukuyembekeza mayankho akumwamba? Amabwera mayankho ambali inayi. Mumangoti ife timapemphera ma born again. Ati tiyeni kubunda ife timangoti tiyeni ukamakwera bus ife timakhala nawe limodzi. Kupemphera osadutsa ntambo 2 nkumati koma nde kunali pemphero, munthu ali pa bunda tu. Enanu mmapemohera pemphero ochita kulemba, analemba 1820 iwe nkumati to kupemphera. M'busa wokufa ananso akufa. Ndi chifukwa kuli mipingo tambiri chifukwa pemphero kulibe kumpingoko aliyense akangomva nkati. Kupemphera ndi ntchito ndipo amene anapemphera nkufika ndekuti anakonzekera osati lodzidzimuka. Pemphero timalankhula ndi Mulungu wanuyo ngati upempha nsima akuuze kuti ndayankha, ndakupatsa. Tikutitu nkulankhulana ndeno Mulungu wanu yo amalankhula? Anthu tu ali nkusala mwezi wonse kungofa ndi njala. Kulitu ma bandulo bandulo a mapemphero a anthu ofooka nde timawankha. Mapemphero mmipingomu a ma founder akungogona tulo. Nawo ma intercessor Ati apempherere abusa maganizo ali kutali. Abusawo akungogona, akati apemphere koma ali busy. Pemphero likangofika Ku ma 20 chakuti uku umakhala a achikulire. Muti mpingo wa nzimu Woyera koma makulankhulani Nzimu yo? Koma malambiro ali pano moto, mabingu amaphurika. Nde pano po wina akugona wagona 7 koloko nkumati akatumikira. A mulengalenga timakhala pa pemphero ngati pemphero lafikira timawankha mayankho. Ndi chifukwa munthu amayaka 3-4 days abusa sachita chibwana , amakhala mpemphero. Mufunse Mzinda Woyera mmene umapemphera, mmene umalambilira. Ukamayika nthawi kuti tiweruka nthawi zanji pemphero lanu silifika. Ndi chifukwa chake mumakhala ndi ma service atatu. Ndipo zilipo zikhulupiliro zina zongoyeselera , timawankha. Nde ena amapita kupemphera ndi misozi osati ya chikhulupiliro koma kuti mabvuto afikapo, timawankha. Udzaone pemphero la pa Mzinda, mpingo umatimvetsa kuwawa chifukwa amachita chimene Mbuye wawo wawauza sapanga zoloweza. Timawankha, kuli ma mendulo a mapemphero. Kulibe pemphero losalankhulana ndi Mulungu. Mudzafunse kuti Mulungu amalankhula mumatani, mizimu imabwera mumatani, pemphero limakatumphula ku mizimu nkutsika. Simungafikire ngati simupita pa Mzinda. Malambiro muphunzire pa Mzinda Woyera amalambira bwanji Mulungu zazikulu zimachitika ndi pa Mzinda Woyera wokha. Simudziwa kuti timafuna kulambira timatani. Ukanfunse wa living waters, assemblies of God, amene amati a chipente ngati timakapezekamo. [Nthawi zina timamva kuti wa satanik anapita ku ma kachisi a ma pente ndipo watembenuka ntima.] Ngati munthu pemphero lake silifika pa ntambo 17 nkovuta kuti angatembenuze munthu. A sataniki imakhala plan kuti aziti anatembenuka ntima. Ngati anali wa satanic tate wake ku uzimu mndani? Tchalitchi yanuyo muti pali Yesu analankhula ndani? Zizindikiro zinalipo pa kumasulidwapo ndi zotani? Sibwezi pano kutabwera Mzinda Woyera, athamanga sadayambe. Chizindikiro chachikulu akatembenuka ntima amakhala osakhazikika pa malopo, kukayambitsa mpingo wawo ati anandikhumudwitsa. Akukhumudwitsa bwanji ngati anakupulumutsa. Ngati amapemphera bwanji osawauza zimene zikuchitika kudziko li. Tuti pemphero ndi kulankhulana, inu Mulungu amakuzindikiritsani. Awa Mulungu wawo amawauza zochita ndipo akawuza amabwera pamaso pa Mulungu wawo ndipo zimadutsa. Mwazi wa Yesu wopanda phindu pa moyo wa munthu, kutembenuka ntima ulibe ndi masomphenya ndi omwe koma ulibe masomphenya uyenda ndi Yesu. Pa Mzinda munthu akabwera mumamuuza iwe ndiwe m'busa nde amasiya zakezo nkuyamba ubusa. Munthu zaka 20 ukutumikira koma ambiri anangotsala dzina lokha. Born again ati born again anameta seda, ameta mbali ma style akunsi kwa nyanja. Zoti seda ndi njoka sadziwa. Pano tiana kuti adziwike kuti ndi ana a mapwepwete awayika seda komatu ali pa mpingo. Amene ife , timatsikirapo, amene adamva mkulu wa dziwanda a kulankhula amenewo a mapemphera zenizeni. Muli ma pesiya mulengalenga amangoseka. Satana ngochenjera anawona kuti anthu tiwaonetse ngati a mapemphera tiwapatse mlozo, cholinga Nzimu Woyera asagwire ntchito, anthu asakhazikike mpemphero, uthenga kuupeputsa. Mesa ma cyclone ndi anthu a pansi pa nyanjawa, sikusinthanso kwa nyengo Mulungu akufuna achotse zonse zoyipa. Akufuna kubwere mbeu yomvera Nzimu yodzadza ndi mabvumbulutso. Asamazinamize anthu kunjaku ife timapempera bwerani ku crusade", kumangodyetsedwa njoka, adyetsedwa njoka anthu. Makachisi ambiri ubale ndi Mulungu unatha mchifukwa ILLIMAKHATHUMA wabwera kuzabwenzeretsa ubale, kudzabwenzeretsa chimene satana adalanda pa munthu ndi chifukwa kunabwera ILLIMAKHATHUMA!