16/07/2022
Nanga zomati kayambitse wako mpingo monga muja mabishop ena amachitira akapeza munthu kapena mkhristu walephera ku thupi zimatanthauza chani ? Chifukwa
1. Yesu adabwera kudzasaka chotayikacho ndipo chikhala kuti aliyense sachimwa ndiyetu bwezi kulibeko mpingo, choncho kuchotsatu ochimwa mumpingo ndikusunga okhulupirika ndikuona kuti pakukolatu
2. Munthu sangayambitse mpingo koma Yesu yekha
3. Palibe mwini wa mpingo
4. Kodi alipo mu Bible yemwe adachotsedwako mu mpingo ?
Kodi ndikulakwa kunena kuti mkhristu ndi munthu yemwe ndi wochenjera pa kachitidwe ka zinthu ? Chifukwa munthu timamutenga kukhala ochimwa kapena kuti si mkhristu kamba koti uchimo wake watulutsira poyera. Tinene kuti alipo chibadwire yemwe sachimwa? Komano simudayambe mwakhalako pansi nkulingalira kuti anthu amène mumawakhulupirira aja kuseriku amakukhumudwitsani ? Apa ndikufuna mufufuze kuti nanga angapulumuke ndi ndani ? Angapulumuke bwanji ? Nanga chipulumutso ndi chiyani ?