08/05/2026
APATSIDWA MAUPHUNGU OSIYANASIYANA
Linali tsiku lamtengo wapatali pa Sector 2 pa 03 May, 2026, limene linali tsiku lamalangizo kwa achinyamata.
Ndandanda wa anthu omwe unayikidwa kuti upereke malangizowa unakonzekera bwino zedi potengera zakuya zomwe zinaphunzitsidwa kwa achinyamatawa. Abusa Dingani Mfune ndi Mayi busa Mfune ndi omwe anali alendo oyitanidwa pa chilinganizochi. Koma iwo sanali okha ayi, anali limodzi ndi Mayi busa Esmie Mulangeni omwe anawalandira m’malo mwa abusa Alfred Mulangeni monga eni khomo komanso mothandizidwa ndi mabanja a Bambo ndi Mayi Labana komanso banja la bambo ndi mayi Mbeya.
Uphunguwu unaperekedwa magawi awiri. Gawo loyamba lomwe linachitika chigawo chakumamawa, linali la gulu lonse. Gawo lachiwiri lakumasana, linali gawo limene achinyamatawa anagawidwa magulu anayi kutengera zaka zawo kuti alandire malangizi ogwirizana ndi msinkhu wawo.
Mwa zina, achinyamata anaphunzitsidwa ndi kulangizidwa zokhudza moyo wawo wauzimu, za malonda, m’mene angadzisamalire, kuwalimbikitsa atsikana komanso udindo wa ana pakhomo. Poyankhulapo Bambo Labana omwenso ndi Patron wa achinyamata (AY) pa Sector 2, anawerenga kuchokora pa Mateyu 6:33 kulimbikitsa kuti ayambe athanga ufumu wa kumwamba ndipo zonse zizatsatira.
Abusa Dingani Mfune amene achinyamata owakonda amangoti Pastor Dingz, anapempha achinyamatawa kuti makolo akawoneretu kusintha pa khalidwe lawo tsiku lomwero
Promise Gracium msungwana yemwe ali mu class ya explorer anayamikira malangizowa kuti sanali omuthandizira moyo wake uzimu okha komanso moyo wake watsiku ndi tsiku monga ku school ndi pakhomo. Iye anapitiliza kulangiza amzake kuti akhale osinthika kutsatira malangizowa.
Naye mtsogoleri wa achinyamata, SYL Kingsley Dzikolo anathokoza anamkungwi onse popanga chilinganizochi kuti chikhale chopambana pakupezeka kwawo osatengera kutanganidwa kwawo. Iwo anapitiliza kuti ndi khumbo lawo kuti ngati mpingo ungalore, mtsogolomu kudzakhale malangizo amasiku awiri pozindikira vuto lomwe linalipo lakuchepa kwa nthawi.
Potsiriza zonse kunali chionetsero ndikuyendera perete omwe achinyamatawa anakonza monga mwa mwambo wawo.
Olemba: Kelvin Chimpokosera
Zithunzi: Novakiwa Perekamoyo