15/10/2025
RIP MULUNGU ATITHANDIZILE KUVETSETSA
Zatsimikizika tsopano kuti a-Malawi okwana khumi, asanu ndi atatu (18) ndi omwe afa pa ngozi ya bus yomwe inachitika ku Limpopo, m'dziko la South Africa.
Bus-yi inanyumala anthu opitilira 90 pa nthawi yomwe ngoziyi imachitika lamulungu lapitali.
Malingana ndi kalata yaku ofesi ya mtsogoleri wa dziko lino ndi nduna, nzika za dziko lino zokwana 18 zafa pa ngoziyo.
Kudzera mu kalatayo, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika komanso mai wa fuko la dziko lino Getrude Mutharika, apepesa mawanja ofeledwa.
Pakadali pano, Mutharika wathokoza dziko la South Africa kaamba ka thandizo lomwe lapereka kwa okhudwa pa ngoziyo.
Mukalatayo, yomwe wasayinira ndi Justin Saidi, mlembi wamkulu mu ofesiyo, boma lati ndilodzipereka kupereka thandizo kwa mawanja omwe akhudzidwa ndi ngoziyo.