06/04/2026
KUKHALA MU PEMPHERO
Pa tsiku lachiwiri la Youth Week of Prayer wa Seventh-day Adventist Church, achinyamata ochokera ku Balaka East, Balaka North komanso Balaka Main asonkhana popitiriza kumva mawu a Mulungu.
Ulaliki unalalikidwa ndi m’busa Orlac Mozalande pa mutu wakuti “Prayer in Action” (Pemphero pa Kuchita).
M’busayu anafotokoza kuti Yesu ndi chitsanzo pa moyo wa pemphero, potengera Marko 1:35 pamene ankadzuka m’mawa kupemphera.
Iye ananenanso kuti pemphero ndi njira yolumikizirana ndi Mulungu, komwe timapereka zosowa ndi nkhawa zathu.
Achinyamata analimbikitsidwa kukhala okonda pemphero chifukwa moyo wopambana umafunikira kulumikizana ndi Mulungu. Zinthu zonse monga sukulu, ntchito, ndi bizinesi ziyenera kuyikidwa mu pemphero kuti zipambane.
M’kulimbikitsa, anatchula zitsanzo za Nehemiya ndi Danieli, omwe anapemphera n’kupeza mayankho kwa Mulungu. Izi zikuwonetsa kuti zimene munthu sangathe, Mulungu amatha, ndipo pemphero limathandiza kukwaniritsa zolinga.
Pomaliza, abusa anatsindika kuti pemphero liyenera kuphatikizidwa ndi zochita. Achinyamata ayenera kugwira ntchito limodzi ndi kupemphera, chifukwa kupambana kwawo kuli mu kudalira Mulungu.
Msonkhanowu ukupitirirabe mpaka Sabata lomwe likubwerali.
Wolemba:
Esau Banda
.