24/04/2026
Lingaliro la Kadzutsa
24/4/26✍️
Yehova amakhala pamodzi nafe chinkana Iye ndi Wokwezeka ndipo "Kumwamba kwa Kumwamba sikukhoza kumusunga Iye." The heavens of heavens cannot contain Him!
📚 2 Mbiri 6:1-42
18. Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu pa dziko lapansi? Taonani, thambo, inde m'mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?
Yankho: Inde nzoona! Koma zindikirani kuti kwa ife "Yehova amaziphimba ndi mdima wa ndiweyani" ndipo sitingathe kuoona ichi ndi maso athu. (v.1)
Kwa Mose Mulungu akulonjeza, "Ine Ndidzakhala ndi iwe." (Ekso. 3:12)
Lonjezano lomwelo Mulungu akupereka kwa Yakobo. (Gen. 31:3,5; Gen. 48:15)
Kwa Abrahamu Yehova akuti, "Usaope Abramu, Ine Ndine chikopa chako ndi mphoto yako yaikirukuru. (Gen.15:1)
Motsimikizika Davide akuti, "Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa sindidzaopa choipa, pakuti Inu muli pamodzi ndi ine..." (Mas. 23:4)
Yesu Mwini akuti, "Ndiri pamodzi ndi iwe kufikira matsiriziro a nthawi ya pansi pano." (Mat. 28:20)
"Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva Mau Anga nakatsegula pakhomo, Ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine." (Chiv.3:20)
Lero, mloreni Yesu alamulire moyo wanu.
Ambuye akudalitseni. Amen.