Friends of Pastor S.W Dumuka.

Friends of Pastor S.W Dumuka. Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Friends of Pastor S.W Dumuka., Religious organisation, Area 21, Lilongwe.

YOHANE 6:35πŸ“–Yesu anati kwa iwo,  ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupili...
09/09/2022

YOHANE 6:35πŸ“–
Yesu anati kwa iwo, ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupilira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.πŸ™

30/07/2022

COMFESSION

Lord Jesus, I recognize you as my Lord, Master and Ruler, the One to whom I belong and that has the final say in my life. I believe with all my heart and declare with my mouth that you're Lord over everything in heaven and earth.Amen

01/07/2022

PEMPHERO LOPEMBEDZERA.

WODALA ndinu MULUNGU amene munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Ndinu Mulungu amene mumawona paliponse ngakhale pansi pa nthaka, pansi pa nyanja.

Yakwana nthawi yomwe timagona kuti matupi athu apumule, tikupempha chitetezo chanu Ambuye.
Tikupempha Angelo anu akhale nafe ndikutimenyera nkhondo za mumdima ife tili chete.

Asamalireni onse omwe ali paulendo kufikira akafike komwe akupita.
Ena akudwala , asamalireni MULUNGU ndipo awone chikondi chanu, azachitire umboni mawa.

AMBUYE tikuyikanso dziko lathu mmanja mwanu, apatseni nzeru zochuluka atsogoleri anthu, muwapatse Mtima ofewa osati wa mwala, adzimva kupweteka mkati mwa mitima yawo anthu akamavutika. Asadzilemeretse okha popeza chuma ndi chotsala koma asamalire nkhosa zanu m***a mtima.

Alimbikitseni onse omwe akuvutika ndi nkhondo, madzi osefukira, zimomerezi, njala ndi zina zotere. Achitileni chifundo Ambuye.

Ambuye, mutilore ife ana anu kuti mutikondere kufikira mawa mmawa, popeza tidziwa kuti kugona ndi kosavuta koma kudzuka.

Tapemphera zonse mu dzina lamphamvu la YESU KHRISTU.AMEN

01/07/2022

Sekelerani, kondwerani chifukwa Mulungu watifikitsa tsiku lina.
Ulemu ndi matamando zipite kwa Iye.

30/06/2022

Lemekeza MULUNGU ukuwerengawe, dziwa kuti chisomo chake chagwera pa iwe. Ma thousands agona tulo usiku wathawu koma sanadzuke nawo lero.
Ali nawo ndi cholinga moyo wako Ambuye. Ngati nkotheka m***a kugawa uthengawu kwa anzanu.

29/06/2022

GENESIS 45
* Yosefe adziulula kwa abale ache*

3 Ndipo Yesefe anati kwa abale ache, ine ndine Yosefe ; kodi akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ache sanakhoza kumyankha iye ; pakuti anabvutidwa pakumuona iye.

4 Ndipo Yosefe anati kwa abale ache, Muyandikiretu kwa ine; nayandikira. Ndipo Yosefe anati, Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndilowe m' Aigupto.

Abale ake anamuchita chipongwe, kumuponya m'dzenje kenako mkumutulutsamo, kumugulitsa. Zonsezi zinachitika chifukwa cha sanje.

Ankawona ngati athana naye, kwake kwatha, omvera!! chimene MULUNGU anakukonzerani kuti chidzakhala chanu, palibe yemwe angachilepheretse kapena kutembelera.

Anthu omwe amakuyang'anirani pansi lero, tsiku lina adzakugwadirani muli mwini chuma, azafuna nthandizo lanu, koma ndi pemphero langa kuti, musamabwenzere choipa kwa adani anu. Chitani chabwino kwa okuchitilani zoipa kuti ufumu wa MULUNGU uwonekere kwa iwo.

YOSEFE SADABWENZELE CHOIPA, KOMA MMALO MWAKE!! ANAWAPATSA ABALE AKE ZOSOWA ZAWO.

Ambuye akudalitseni.

Address

Area 21
Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Friends of Pastor S.W Dumuka. posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share