23/08/2026
FAITH TEMPLE OMC YAPEREKA K3 MILLION KU MPINGO
Gulu la amayi Otumikira Mwa Chikondi (OMC) la Kasungu Faith Temple mu mpingo wa Malawi Assemblies of God Ku Kasungu, lapereka ndalama yokwana K3 Miliyoni ku mpingo kuti ithandize pa ntchito yogula Coaster (Basi) ya mpingo.
Wachiwiri kwa mkhalapampando wa amayi pa mpingowu, Rose Nkhoma ndiye wapereka ndalamazi m'malo mwa amayi onse a OMC pomaliza pa mapemphero, lero.
Ndalamazi adazipeza pa mwambo omwe anakhazikitsa chimbale chao sabata ziwiri zapitazo.
A Nkhoma ati polingalira masomphenya omwe mpingo uli nao ogula Basi (Coaster), sangakhale chete koma kutengapo mbali.
M'busa Chikumbutso Msendema wa mpingowu, wayamikira zomwe amayiwa achita.
Iwo ati zonse zokonzekera kugula Coaster zili mchimake ndipo posachedwapa khumbo la mpingowu likwanilitsidwa.
Mpingo wa Kasungu Assemblies -Faith Temple, ukukonza zogula Coaster ya mpingo chaka chino.
(Kasungu Faith Temple Media)