19/05/2026
Uthenga Wa Chipulumutso
Ndikudziwa Kuti Inuyo Mukupita Ku Church Mwina Simujombaso Komaso Mawu a Mulungu Mukuwadziwa Kwambiri Ena Amakuitanani A Khristu Mwina Ena Akuitana inuyo Kuti Atsogo Ena Ndinu Abusa Kumene Koma Muli Ndi Vuto La NTCHIMO Ubale Wanu Ndi Mulungu Sulibwino.
Mukudziwa Abale Kuti CHOLINGA Cha Mulungu Sikuti inuyo Mudzipedzeka Malo Opemphereramo Okha Ayi Tiyende Mu Chiyero Molemekedza Mawu Ake Kuti Tikhare Nawo Moyo Osatha Tione Mawuwa
2 Timoteyo 3:1-4
Koma dziwa izi: Mʼmasiku otsiriza kudzafika nthawi zoopsa kwambiri.
Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero.
Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino,
opereka anzawo kwa adani awo, osaopa zoyipa, odzitukumula, okonda zowasangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu.
Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa.
Tikuona Mumawu Awa Akunena Za Matsiku Otsilidza Zonse Akunena Mawuwa Zikuchitika Matsiku ano Anthu Adzakhala Okonda Ndalama So Muone panopa Ena Asanduka ma h**e Chifukwa Cha Ndalama Ena kujoina Satanic Chifukwa Cha Ndalama Muzonse Pali Mawu Awa
2 Timoteyo 3:5
Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa.
Tonse Tichenjere Ndi Mawu Awa Kukhala Ndi maonekedwe Achipembedzo Koma Kuyikana MPHAMVU yake Zoona Akhristu omwa mowa Akhristu Ochita Chigololo MKAZI wake alinaye Koma kumayendaso Ndi Wamwini wake Akhristu opita ku church Atamvala kolekedzera mu Nchafu KODI NDI MTUNDU WANJI WA AKHRISTU ABADO UNO OCHITA ZOIPA?
CHOKANIKO KU NTCHIMO KHALANI AKHRISTU WOONA MTIMA OTI AMBUYE YESU AKAMATIONA ADZIKONDWERA NAFE.
CHOKANIKO KUKHALA AKHRISTU ABODZA.