28/05/2026
NGOZI ZA PA LAKE CHILWA
Monga mukudziwa ngozi za pa lake chilwa zimachitikachitika. Mwa zifukwa zina zimene zimachititsa ngozizi ndi monga;
Nyanjayi siyakuya
Lake Chilwa ndi nyanja imodzi imene madzi ake si akuya kuno ku Malawi, izi zimapangitsa kuti ma boat aziyenda movutikila
Mphepo ya ya mwera
Nyanjayi ndi ya flat, ndipo zimapangitsa kuti pazitha kuyamba mafunde mophweka especially ikakhala nthawi ya mvula ndi ya mphepo. Kugwiritsa ntchito ma tima bwato tating'onoting'ono sitichedwa kugudubuzika.
Lake Chilwa ilibe outlet
Izi zimapangitsa kuti mudzadze michenga ndi zomera zimene zimatha kukola mwabwato kuti asamayende bwino kapena kukodwa kumene.
Chifunga
Makamaka usiku kapena mbandakucha,
Chifukwa cha zifukwa izi, Lake Chilwa imatengedwa yoopsa kwambiri kwa anthu ogwiritsa ntchito tima bwato tating'onoting'ono poyerekeza ndi nyanja zina