25/05/2026
Ndalama zokwana 35 million Kwacha ndi zomwe zinapezeka pa Mwambo wa Diner and Dance Gala ndinso fundraising yomwe inakonzedwa ndi gulu la Association of Former Catholic Seminarians mu mzinda wa Blantyre.
Ndalamazi zomwe ntchito yake ndi kulipilira anyamata omwe ali ndi khumbo lodzakhala ansembe ndipo pano ali m'sukulu zikuluzikulu zosulira ansembewa, zikuyembekezeka kukaperekedwa ku likulu la mpingo wa Katolika mdziko muno a Malawi Conference of Catholic Bishops (MCCB).
Mlangizi wa gululi Monsignor Henry Chikanda ati ndi okhutira ndi mmene gululi likugwilira ntchito zake kaamba koti pali kusintha kwakukulu kuchoka pa mmene gululi linayamba ntchitoyi pomwe chaka choyamba linapeza 2 million kwacha, chaka chotsatira chomwe ndi cha 2025 anapeza 10 million kwacha ndipo pano ndalamayi yakwera.
Wapampando wa gululi Dr. Maxon Ngochera wayamikira mamembala a gululi ndi onse akufuna kwabwino omwe anatengapo mbali ndi kuthandizira kuti apeze ndalamazi.