15/05/2026
MAU ODZUKIRA
" Sichinakugwereni inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako."
1 AKORINTO 10:13
Okondedwa, kupilira ndi chinthu cha mtengo wapatali, moyowu timadutsa mu zambiri koma Mulungu akuti okhala mwa Iye adzamuthandiza kupilira kuti agonjetse.
Mukhale ndi tsiku lopambana. Amen