12/04/2019
NDINGATHAWIRE KUTI?
Mkulu wina olemba ndi kutsindikiza mabuku, otchedwa William Shakespeare, analemba buku lina lotchedwa, "Julius Caesar."
Mu bukuli muli nkhani ya mkulu wolamula wakale wa kudziko la Rome otchedwa Julius Caesar amene nthawi ya ulamuliro wace anali wokondedwa.
Koma kamba ka ndale ndi akuluakulu ogwira nao ntchito, guru la ogwira nao ntchito (senators) linapanga upo wofuna kupha mtsogoleriyu ndipo ciwembuci cinapangidwa kuti cikacitikire ku malo a zokambirana monga ikhalira parliament yomwe kwa iwo imatchedwa capitol.
Mkazi wace analota maloto omucenjeza kuti asapite kumalowo, koma Iye monga mtsogoleri anacita makani kuti apita basi potengera kuti iye amati nkokakambirana zokweza dziko.
Mkulu wina wolosera ndi kulota za mtsogolo (Sooth sayer) naye anafuna kupereka uthengau panjira pomwe panali namtindi wa anthu ofuna kumuona pomwe anali kupita ku capitol, koma analephera kutero kamba ka namtindiwu kotero Caesar anakafika ku capitol komwe kunali zokambirana za akuluakulu a boma.
Zokambirana ziri mkati, mkulu otchedwa Cassius anafunsa funso kwa Caesar kotero Caesar poyankha, m'modzi wa mguru la ma senators otchedwa Casca anadzipsetsa mtima mwadala monga mwa cikonzero cao (Conspiracy) kotero anasolola lupanga lace nalankhula mau kuti, "Manja anga, ndilankhulire" (Let my hands speak for me) kotero anagwaza nalo pamtima pa Julius Caesar amene anaferatu pomwepo.
Imfa itacitika, cinawatsalira ndi nzeru yokaliuzira dziko kuti imfa ya mtsogoleri wao yabwera bwanji kotero anamemeza dziko lonse kukakumana malo otchedwa Market Square.
Mu kukambirana kwao, anauzana kuti asakanene bodza koma kunena zoona kuti iwo amupha pofuna kupulumutsa dziko ku nkhanza ndi kudzikonda kwace kotero alole kuti pasankhidwe mtsogoleri wina.
Izi zitakonzeka, ndikulengezedwa, mbiri ya imfa ya Julius Caesar inali ponseponse ndipo mkulu wina otchedwa Mark Antony, anapempha kuti akalankhule pa malirowo.
Mark Antony anali mnzace wa Julius Caesar amene amauzana naye zinsinsi zambiri ngakhale Mark Antony sanali mgulu la olamulira ndipo guru iri la upandu linalamula kuti Mark Antony akalankhule kumapeto koma asakalankhule zowapacika ai.
Pa mwambowu, akuluakulu aboma monga Marcus Brutus, Cassius ndi Caius Ligarius analankhula ndipo anthu anaombera mmanja kuti zoona Caesar anayeneradi kufa ndithu cifukwa mu umboni wao, ananena kuti, Caesar anali Mtsogoleri odzikundikira cuma amene sakhudzidwa ndi kusowa kwa anthu mdziko lace kotero iwo atenga risk yomupha kuti apereke ufulu kwa anthu wamba.
Izi zinawakomera anthu omwe anaimba nthungululu ndi kuombera mmanja uku mtembo wa Caesar usanafike pamalopo.
Mwadzidzidzi, Mark Antony anafika pamalopo ndi mtembo wa Caesar ataukulunga nauika pamsanja pomwe amalankhulira ndi kuyamba kulankhula uku akulu onse aboma ndi aupanduwa akunyamuka.
Mmau ace, Mark Antony anangoti, "Ndabwera kudzaika m'manda Caesar osati kudzamutamandira" (I've come to burry Caesar, not to praise Him).
Komabe ndinayenera kukuuzani za ma plan a mu will ya Caesar.
Caesar anaika cuma capadera cothandizira inu mdzaka za mtsogolomu ndipo mbali ya malo ambiri anapereka kwa anthu inu ovutika.
Pali zabwino zambiri zomwe Caesar amakukonzerani zomwe ngakhale wamwalira, zinthuzi muziona zikukucitikirani.
Mau awa, anautsa mkwiyo wa anthu omwe analingalira kuti, nkutheka guru la akuluakulu a boma lija, lapha Caesar osati pa zifukwa zomwe amanenazo ai, koma kufuna udindo wace kotero anthu a dziko la Rome anapsa mtima nalonjeza kusaka aliyense payekhapayekha wacita nao ciwembuci ndi kumuphanso.
Mguru la akuphali munali mkulu wina wosatchuka otchedwa Pindarus ndipo Iye podziwa kuti kalikonse katha kucitika, anathawira kuphiri komwe ali pamwamba pa phiriri amaona zonse zocikika pa Market Square ndipo mkwiyo wa anthu amatha kuuona kuti anthu akubalalika nasakasaka malo onse omwe angathe kupeza akuluakulu akuphawa.
Mantha atamugwira, anadziwa kuti, nkosathekanso kubwerera kunyumba kwace cifukwa anaona nyumba zina za akuluakuluwa zikuyatsidwa moto ndipo anadziwa kuti kubwerera kwa Iye ndi cionongeko.
Atakhala n'kusowa nzeru, analankhula mau onena kuti;
"FAR FROM THIS COUNTRY, PINDARUS SHALL RUN, WHERE NO ROMAN, BUT, SHALL TAKE NOTE OF HIM."
Iri linali lingaliro lomwe linamufikira kuti, kutali ndi dziko lace la Rome, Iye akuyenera kuthawira kuti pasapezekenso wina ozindikiranso za komwe wapita.
Konsekutu kunali kusowa ndi kuusakasaka mtendere polingalira za kupalamula komwe anapalamula ndipo anaziona kuti palibenso pobisalika mu dziko la Rome angathe kukhala, koma kupita kutali zedi kuti pasapezeke omupeza ndi kumupha.
Ambiri lero tiri mdziko la cilendo osati mwa kufuna ai, koma kamba ka mavuto omwe tinawapalamula kwathu.
Ena tinathawa milandu ya kupha, kuba angakhalenso milandu ya zigololo yomwe mwa njira ina iriyonse ikanaphetsa miyoyo yathu.
Ena tikunema pano tinathawa mavuto a banja, ena ngongole zitafika povuta zomwe manjira ina iriyonse zimapereka citonzo komanso ciopsezo ku moyo wathu.
Koma ngakhale titathawa motani pamaso pa nyengo zimenezi, malo alionse amene timathawirawo sitipezabe mtendere, zonsezi ndi cifukwa cakuti, tathawa pamaso pa Mulungu.
Adamunso atalephera kumvera macenjezo a Mulungu posadya zipatso za mtengo oletsedwawo, tikupeza kuti atangodya cipatso ca pakati pa munda, Adam ndi Hava anadziona kupelewera pamaso pa Mulungu kotero nthawi yomwe Mulungu anali kuwaitana, iwo sanafune kuyankha koma kuthawa ndi kubisala (Gen 3: 8-10).
Koma ngakhale anabisala, Mulungu diso lace limawaonabe.
Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu? Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu? Ndikakwera kunka kumwamba, muli komweko; kapena ndikadziyalira ku Gehena , taonani, muli komweko.
(MASALMO 139:7-8).
Tingathe kuthawira kuli konse, komabe consciece yathu ndi imene imatisaka ndipo timakhalabe anthu ozunzika mumtima.
Tinayenera kudziwa kuti, tonsefe ndi ocimwa ndi operewera pamaso pa Mulungu kotero, kuthawa anthu a dziko lapansi kapenanso nyengo za dziko lapansi sikungatipindulire, koma kuthawira kwa mwini opereka moyoyo.
Ndipo ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musaope iwo akupha thupi, ndipo akatha ichi alibe kanthu kena angathe kuchita. Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya ku Gehena , inde, ndinena ndinu opani ameneyo.
(LUKA 12:4-5)
Ndikufuna ndilankhule ndi moyo wa wina lero amene akusautsidwa mu njira zosiyanasiyana ndipo akulakalaka atangosowa, kufa ndipo sakuonanso cifukwa cokhalira ndi moyo lero kuti, kulibe kwina komwe ungathe kuthawira, koposa kwa Mulungu.
Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.
(MASALMO 46:1)
Anthu athawirapo maiko ocuruka kamba ka zovuta za mdziko lao monga njala, nkhondo ndi zina zocuruka natchulidwa ma refugee kumeneko, koma kumaiko konseko anathawirako, sanakhale mwaufulu cifukwa zovuta sizimati zawapeza liti, koma refugee camp yopambana yomwe inu ndiine tingathawireko mmasautso athu, ndiye kwa Mulungu.
Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.
(MIYAMBO 18:10)
Mulungu akudalitseni pamene mukutsinkhatsinkha zosankha kwa Mulungu yekha monga kothawirako mnyengo zanu zonse.
Evangelistkawalanga@dailystrength2019.