03/04/2020
*MPINGO WA NEW JERUSALEM PENTECOST M'MALAWI 🇲🇼
_*Nthenda yoopya ndiso njira Zake zothanira nawo*_
*pemphero*
_Mulungu WA Ana a Israeli, Musaliiwale dziko lapansi, Musaliiwale dziko LA Malawi 🇲🇼. Tithandizeni ndukutichiritsa Tonse. Amen._
*_Uneneri WA yeremia zamthendayi_*
*_Yeremia 16 vs 1-12_*
1Ndiponso mau a Mulungu anadza kwa ine, kuti, 2Usatenge mkazi, usakhale ndi ana amuna ndi akazi m'malo muno. 3Pakuti Yehova atero za ana amuna ndi za ana akazi akubadwa m'malo muno, ndi za amai anawabala iwo, ndi za atate ao anawabala iwo m'dziko muno: 4Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala cakudya ca mbalame za kumlengalenga, ndi zirombo za dziko lapansi. 5Pakuti Yehova atero, Usalowe m'nyumba ya maliro, usanke kukacita maliro ao, kapena kuwalirira; pakuti ndacotsa mtendere wanga pa anthu awa, cifundo ndi nsoni zokoma, ati Yehova. 6Akuru ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzacita maliro ao, sadzadziceka, sadzadziyeseza adazi, cifukwa ca iwo; 7anthu sadzawagawira mkate pamaliro, kuti atonthoze mitima yao cifukwa ca akufa, anthu sadzapatsa iwo cikho ca kutonthoza kuti acimwe cifukwa ca atate ao kapena mai wao. 8Usalowe m'nyumba ya madyerero kukhala nao, ndi kudya ndi kumwa. 9Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli; Taonani, ndidzaletsa pano, pamaso panu masiku anu, mau akukondwerera ndi mau akusangalala, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi. 10Ndipo padzakhala, pamene udzaonetsa anthu awa mau awa onse, ndipo iwo adzati kwa iwe, Cifukwa cace nciani kuti Yehova watinenera ife coipa cacikuru ici? mphulupulu yathu ndi yanji? cimo lathu lanji limene tacimwira Yehova Mulungu wathu? 11Pamenepo uziti kwa iwo, Cifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu yina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga cilamulo canga; 12ndipo mwacita zoipa zopambana makolo anu; pakuti, taonani, muyenda yense potsata kuumirira kwa mtima wace woipa, kuti musandimvere Ine.
*NJIRA ZOTHANIRA NAWO*
*_2Mbiri 7: 14_*
14ndipo anthu anga ochedwa dzina langa akadzicepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera m'Mwamba, ndi kukhululukira coipa cao, ndi kuciritsa dziko lao.
*_Yesaya 43: 4-7_*
4Pokhala iwe wa mtengo wapatari pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako. 5Usaope; pakuti Ine ndiri ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kucokera kum'mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kucokera kumadzulo. 6Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kumwera, Usaletse; bwera nao ana anga amuna kucokera kutari, ndi ana anga akazi kucokera ku malekezero a dziko lapansi; 7yense wochedwa dzina langa, amene ndinamlenga cifukwa ca ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.
_*2Mbiri 30: 18-20*_
18Pakuti, anthu aunyinji, ndiwo ambiri a Efraimu, ndi Manase, Isakara, ndi Zebuloni, sanadziyeretsa, koma anadya Paskha mosati monga munalembedwa. 19Koma Hezekiya anawapempherera, ndi kuti, Yehova wabwino akhululukire yense wakuika mtima wace kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ace, cinkana sanayeretsedwa monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika. 20Ndipo Yehova anamvera Hezekiya, nawaciritsa anthu.
*_Deuteronomy 7:15_*
15Ndipo Yehova adzakucotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa ziri zonse za Aigupto muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu.
*PHUNZIRO*
Nthawi zonse tikhale omvetsera, timvere ndinso Kupempha kwa Mulungu pa China chilichonse. Mulungu ndiothekera..... Kumbukirani kuti muzu wa mavuto ndi nyengo zonse za nsautso ndi kusamvera, kukonda Ndalama ndi dzina.
Tilole Mulungu atithandize ndikupatsa madalitso ndi ulemerelo omwe adalonjeza kukenani. Dziko lino sikwathu, tiyeni tikhale ngati alendo, pakuti posachedwa, tichoka padziko pano kuloza kuchiweruzilo. Tikhale odekha ndi ofatsa muchilichonse, tipemphere chipambano kuzera kwa Yehova. Ndithudi Malawi apulumutsidwa ku mtenda ya Covid 19.
Kuchokera ku banja LA mpingo WA New Jerusalem Pentecost pansi pa ulamuliro WA BP Rev Peter kachulu ndi Senior Pastor Wyson.
Tikufunirani umoyo wathanzi ndikukulimbikitsani kusamila kwa yehova nthawi zonse. Dana nachoni choyipa.
Monga mwa malemba........
*_1samueli 25: 6_*
6ndipo muzitero kwa wodalayo, Mtendere ukhale pa inu, mtendere ukhalenso pa nyumba yanu, ndi mtendere ukhale pa zonse muli nazo.
Amen.