Showers of Blessings Mountain Ministry

Showers of Blessings Mountain Ministry GOD IS STILL PUT HIS EYES ON US, AND HIS EARS TO HEAR FROM US ,2 CHRONICLES 7:14-15

First message in 20261 thessalonians 5:18-19
06/01/2026

First message in 2026
1 thessalonians 5:18-19

Check out Mtumwi’s video.

05/01/2026

1 Chronicles 4 : 10

And Jabez called on the God of Israel, saying, Oh that thou wouldest bless me indeed, and enlarge my coast, and that thine hand might be with me, and that thou wouldest keep me from evil, that it may not grieve me! And God granted him that which he requested.

1 Mbiri 4:10 Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israyeli, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti coipa cisandibvute. Ndipo Mulungu anafikitsa copempha iye.

# Ngati pempheroli Lili lanunso, type Amen

God bless you and enlarge your boundaries too.... shalom!!!

https://youtu.be/cLNXhtMqxq8?si=FXUazLKu3liVbCiFthank you children of God for the support given me in 2025. I promise to...
01/01/2026

https://youtu.be/cLNXhtMqxq8?si=FXUazLKu3liVbCiF

thank you children of God for the support given me in 2025. I promise to bring the best this year,2026,God will.
tsiku la vote ndi nyimbo yauzimu, yoyimbidwa or muzisankho zampingo, school, union or any other organizations. sizapanga expire.
please keep on like , subscribe,share and comment to my YouTube page.
happy new year to all

Tsiku la vote by Mtumwi Patrick Martin (Official music video Dir by Vj Bornie)

25/12/2025

KUKONDWERERA KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU SIMAFANO:

*Luka 2:9-11 Ndipo mngelo wa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuwala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anaopa ndi mantha akuru. Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa cikondwero cacikuru, cimene cidzakhala kwa anthu onse; pakuti wakubadwirani inu lero, m'mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.*

MALEMBAWA AKUTI YEHOVA ANATUMA ANJELO AKE KUKAWAUZA ABUSA KUTI MMUDZI MWA DAVID MWABADWA MPULUMUSI. NDIPO ANATI UTHENGAWU NGWACHISANGALALO CHACHIKULU KWA ANTHU ONSE KUPHATIKIZIRAPO IFEYO.

ZATSIKU LOMWE YESU ANABADWA NDIZOPANDA NCHITO KUTI TILIDZIWE ZOTI LINALI LOLEMBA, LACHIWIRI, OR LACHITATU KAYA MWEZI UTI KUTI MU JANUARY, FEBRUARY OR MARCH, ZOMWE ZIKUFUNIKA KUKONDWERERA NDIKUBADWA KWA YESU KO, KOMWE KUDABWERETSA CHIPULUMUSO KWA ANTHU ONSE.

MONGA KUMWAMBA KUKONDWERA KUBADWA KWA YESU, INENSO NDIKUKONDWERA NDITHU, INUNSO KONDWERANI PAMODZI NDIANJELO AMULUNGU.
MERRY CHRISTMAS TO ALL OF YOU IN JESUS NAME...AMEN

Mulibwanji okondedwa mwa Ambuye:TILENGEZE ZA CHAKA CHOKOLOLA CHA 202622/12/25MULUNGU ANALENGA ZONSE NDIMAWU AKE NDIPO ZI...
22/12/2025

Mulibwanji okondedwa mwa Ambuye:

TILENGEZE ZA CHAKA CHOKOLOLA CHA 2026

22/12/25

MULUNGU ANALENGA ZONSE NDIMAWU AKE NDIPO ZINAKHALA IYE MONGA ADAFUNIRA. ANAPANGA MUNTHU NCHIFANIZIRO CHAKE, WAMAMUNA NDIWAMKAZI NAWADALITSA. ANAWAPASA MPHAVU YONCHULA MAINA ANYAMA NDIZINTHU MONGA ANAFUNIRA NDIPO MAYINAWO ANAKHALA.

LERO CHIFANIZIRO CHAMULUNGU NDIFE. TIKALENGEZA NDICHIKHULUPILIRO ZIKHALA:

*Miyambi 18:20-21 Mimba ya munthu idzakhuta zipatso za m'kamwa mwace; Iye nadzakhuta phindu la milomo yace. Lilime liri ndi mphamvu pa imfa ndi moyo; Wolikonda adzadya zipatso zace.*

MILOMO YATHU ILENGEZE ZA ZOKOLOLA KUNCHITO YAMANJA ATHU MCHAKA CHIKUBWERACHI. OSAKAYIKIRA POLENGEZA, MUNTHU AMAKHUTA NDIZOLAKHULA ZAMKAMWA MWACHE, ONSE AMENE ADAPAMBANA ANALANKHULIRA NYENGO ZAWO NDIPAKAMWA PAWO. LENGEZANI LERO KUTI ATATE " NDIKUFUNA KUDYA ZIPATSO ZAMANJA ANGA, NDIKUFUNA KUKOLOLA OLO NDITALIMA PADWALE CHIFUKWA CHAULEMELERO WADZINA LANU, NDIYENDERENI MODABWISA MUCHAKA CHIKUBWERACHI, MASOKA NDIMINYAMA, KUBEREDWA NDIKUPONDEREZEDWA ZISALOWE NAWO MUCHAKA CHINA. NDAPEMPHA IZI MUDZINA LA YESU KHRISTU AMBUYE, AMEN".

Ambuye akudalitseni okondedwa, shalom!!!

19/12/2025

*Lingaliro lathu lalero pa 19 December 2025*

*Masalmo 34:1-3 Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; Kumlemekeza kwace kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza. Moyo wanga udzatamanda Yehova; Ofatsa adzakumva nadzakondwera. Bukitsani pamodzi ndine ukuru wa Yehova, Ndipo tikweze dzina lace pamodzi.*

Brethren, kufika lero pa 19/12/25 ndichisomo chachikulu. Ochuluka sanafikire chisomo choterechi ngakhale anali nawo mtima ofuna.

Mulungu walola kuti inu ndine tikhale moyo kuti tibukise dzina la Yehova Mulungu wathu.

Takumbukirani muzowawa zomwe mwadusamo, Mulungu wakupambanisani.
Kumbukiraninso zabwino zochuluka mwapeza muchaka ichi, Mulungu anakupasani. Werengani madalitso onse nkumawatchula limodzilimodzi kuti muone chifundo Cha Yehova pa inu. Zimenezi zitilankhulitse ngati Davidi kuti "ndidzalemekeza Yehova mmoyo mwanga ndipo kumulemekeza kwake kudzakhala konkera mpaka muyaya".

Ngati pali ena omwe akuwona zoti sanaduse bwino muchacha ichi Cha 2025 ndipo kuti alibe ngakhale kaumboni, musadandaule, Tayambani kuyamika Mulungu pazochepa mungakumbuke or zachaka chatha ndipo Mulungu akupasani umboni wachaka chino or kutasala tsiku limodzi kuti chithe chakachi, Mulungu wathu sachedwa komanso safulumira, zamatsiku alibe nazo nchito,koma zamoyo wanu.

Ambuye adalitse tonse, mdzina la khristu Yesu Ambuye wathu, Amen

13/11/2025

Lingaliro lathu lalero

Masalmo 1:1-6

*WODALA munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, Kapena wosaimirira m'njira ya ocimwa, Kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Komatu m'cilamulo ca Yehova muli cikondwerero cace; Ndipo m'cilamulo cace amalingima usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; Wakupatsa cipatso cace pa nyengo yace, Tsamba lace lomwe losafota; Ndipo zonse azicita apindula nazo. Oipa satero ai; Koma akunga mungu wouluka ndi mphepo. Cifukwa cace oipa sadzaimirira pa mlanduwo, Kapena ocimwa mu msonkhano wa olungama. Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama; Koma mayendedwe a oipa adzatayika.*

12/11/2025

Lingaliro lathu lalero:
Buku Lopatulika 1992
1 Akorinto 9:22-24 Kwa ofoka ndinakhala ngati wofoka, kuti ndipindule ofoka, Ndakhala zonse kwa anthu onse, 1 kuti pali ponse ndikapulumutse ena. Koma ndicita zonse zifukwa ca Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nao. Kodi umudziwa kuti iwo akucita makani a Iwiro, athamangadi onse, koma nmodzi alandira mfupo? Motero 2 thamangani, kuti mukalandire.

https://youtu.be/cLNXhtMqxq8?si=v9FR5IaBoNiubvzaa wonderful team of the most high has made it possible to have a 3.5k vi...
11/10/2025

https://youtu.be/cLNXhtMqxq8?si=v9FR5IaBoNiubvza

a wonderful team of the most high has made it possible to have a 3.5k viewers within a month. (thank you team)

Tsiku la vote by Mtumwi Patrick Martin (Official music video Dir by Vj Bornie)

https://youtu.be/cLNXhtMqxq8?si=QkLvAmVltnO8oqKvThis gospel song has an important message for the nation hence 2.3k with...
22/09/2025

https://youtu.be/cLNXhtMqxq8?si=QkLvAmVltnO8oqKv

This gospel song has an important message for the nation hence 2.3k within a 10 days period. Let's continue share the link..
Ambuye Mulungu mutisegule maso, e.t.c

Tsiku la vote by Mtumwi Patrick Martin (Official music video Dir by Vj Bornie)

Children of God, here is a new national anthem you can't miss, down,watch, like, comment and share https://youtu.be/cLNX...
11/09/2025

Children of God, here is a new national anthem you can't miss, down,watch, like, comment and share

https://youtu.be/cLNXhtMqxq8?si=MFqSyoO4-XIJkEbS

This is a hit

Tsiku la vote by Mtumwi Patrick Martin (Official music video Dir by Vj Bornie)

Address

MACHINJIRI
Blantyre
265

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Showers of Blessings Mountain Ministry posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share