25/07/2026
โ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐
โ
โ"๐จ๐๐ ๐๐๐๐๐, ๐๐๐๐๐ ๐๐
๐ ๐๐๐๐๐๐๐; ๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐, ๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐
๐ ๐๐๐๐; ๐ด๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐ ๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐
๐ ๐'๐๐๐
๐๐ ๐๐ ๐จ๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐. ๐ฒ๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐ ๐ฐ๐๐๐๐๐๐๐..... ๐ป๐๐๐๐๐๐ ๐ฐ๐๐ ๐๐
๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐ฐ๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐; ๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐, ๐๐
๐ ๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐
๐." (Mateyu 10:5-6,16).
โ
โAbale ndi alongo mwa Khristu Yesu, tanthauzo la mau oti '๐บ๐ถ๐บ๐ฏ๐๐น๐' (wolves) mu Chingerezi ndi; gulu la agaru olusa a mtchire, omwe amakhala ndi moyo posaka mwagulu ndi kudya nyama zinzawo. Makhalidwe ndi machitidwe awo a zinthu amayimirira anthu aziwanda ndi oyipa mitima. Tanthauzonso la nkhosa ndi zifyuyo zokhala ndi ubweya wambiri, zowetedwa chifukwa cha nyama ndi ubweya wake. Nzosalusa ndi kuononga nyama zinzawo popeza zimadya udzu. Ndipo khalidwe lawo limaimirira anthu abwino ndi odzichepetsa kapena ana a Mulungu mosiyanitsa ndi mbuzi kapena anthu oyipa mitima.
โ
โMu Baibulo, Ambuye Yesu Khristu amawafanizitsa ana a Mulungu kapena Okhulupirira ake enieni ngati nkhosa; ndi Iye mwini ngati M'busa Wabwino." ๐ฐ๐๐ ๐๐
๐๐๐ ๐ด๐๐๐๐ ๐พ๐๐๐๐๐๐; ๐๐
๐๐๐ ๐๐
๐๐๐๐๐
๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐; ๐๐
๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐
๐๐๐๐๐ ๐๐๐. ๐ด๐๐๐๐ ๐จ๐๐๐๐ ๐๐๐
๐๐
๐๐๐๐ ๐๐๐, ๐๐
๐ ๐ฐ๐๐ ๐๐
๐๐๐
๐๐๐๐ ๐จ๐๐๐๐; ๐๐
๐๐๐ ๐๐
๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐." (Yohane 10:14-15). Ndipo ngati Mlengi wa Kumwamba ndi dziko lapansi, (๐ฌ๐ผ๐ต๐ฎ๐ป๐ฒ 1:10), Yesu ankadziwa bwinobwino zoti nkhosa ndi mimbulu sizikhalira pamodzi ngati mphaka ndi khoswe. Koma mwadaladala adazilola zidzitero.
โ
โMonga tawerengera m'Malemba oyambirira m'mwambamu, Yesu adatuma Ophunzira ake kuti akatumikire Uthenga wake pakatikati pa mimbulu; akudziwa bwino kuopsya kwake kwa nkhosa zosalusa ndi zodzichepetsa kupezeka pakati pa mimbulu yolusa ndi ya njala. Nchifukwa chiyani adachita zimenezi kapena amakonda kuchita zoterezo ndi Akhristu Okhulupirira ake? Nchifukwa ninji amakonda kuyika miyoyo ya nkhosa zake zomwe anazigula modula ndi mwazi wake pa chiswe? Ndi nkhanza kodi? Ayi sichoncho!
โ
โKuyambira ku chiyambi, Iye wakhala akufuna nkhosa zake zidzikhala ndi moyo potambasula ndi kuwonetsera Chikhulupiriro chawo mopanda malire, iliyonse payokhapayokha; ndi kukhalanso ndi chidaliro chathunthu chopanda nacho mtengo wogwira, pa Iye ngati M'busa Wabwino, mu mayendedwe awo onse a Chikhristu padzikoli. Iyi ndi njira imodzi yophunzitsira nkhosa zakezo mwauzimu kuti zidziligonjetsa dziko lapansi monga Iyenso adalilaka ndipo pano akulamulira limodzi ndi Atate ake mu Ufumu Wakumwamba.
โ
โ"๐ด๐๐๐๐๐๐, ๐๐๐๐๐๐ ๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐, ๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐จ๐๐๐๐ ๐๐๐ ๐๐๐๐๐
๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐ผ๐๐๐๐." (Luka 12:32). Dziwani kuti ndi kagulu ka nkhosa ka M'busa Wabwino komwe kamasowekera kumadya msipu wobiriwira mdambo padzikoli pakati pa mimbulu yolusa ndi ya njala komanso yodzazidwa ndi ziwanda zosiyanasiyana, mopanda mantha poika chidaliro chawo kwathunthu pa Mlengiyo yemwenso ndi M'busa wawo Wabwino. Nkhosazitu zilibiretu chodzitetezera ndi mtengo wogwira ku mimbuluyi kupatula kudalira M'busa wawo Wabwinonoyu.
โ
โNzowonadi, Mbusa Wabwinoyu amachita ndi kagulu ka nkhosa zake m'njira yofuna kukhala ndi nkhosa zenizeni zogonjetsa m'mayesero osiyanasiyana a dziko lapansi. "๐ฐ๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐, ๐๐
๐๐
๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐
๐ ๐ฐ๐๐ ๐๐ ๐๐๐๐๐
๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐, ๐๐๐๐๐ ๐ฐ๐๐๐๐๐ ๐๐
๐๐๐๐๐๐๐๐๐, ๐๐
๐๐๐ ๐๐
๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐
๐ ๐จ๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐ ๐๐๐๐๐
๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐." (Chivumbulutso 3:21). Kotero nzosadabwitsa kuti Khristu ankawaphunzitsa Ophunzira ake mokhwima ndi mwa magobo; powatuma kukalalikira Uthenga Wabwino ngati nkhosa pakati pa mimbulu; nkuwaletsa kunyamula kamba aliyense, ndalama kapena chovala chapadera; ngakhalenso kuwayendetsa opanda nsapato kuphazi pa ulendo wopita kunkhondo. ( ๐ ๐ฎ๐๐ฒ๐๐ 10:9-10)
โ
โIye nthawi zambiri amatero akafuna kukhazikitsa makhalidwe aumulungu wofanana ndi a Iye mwini mwa nkhosa yake iliyonse. Safuna kungowalemba chabe makhalidwewo m'mitima yawo koma achite kuwalotchwa kuti asadzafutidwenso ndi china chirichonse ngakhale ndi nthawi imene. Ameneyo ndiye Yesu Khristu weniweni ndimdziwa ndi kumtumikira ine. Ndithudi! Yemwe amawatenga atumiki ake enieni ngati akapolo wopanda phindu, womwe sawalola kumapangira malonda nkupezerapo chuma kuchokera mu kulalikira Uthenga wake Wabwino. (๐๐๐ธ๐ฎ 17:7-10)
โ
โ"๐ต๐
๐๐๐ ๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐
๐๐๐
๐๐, ๐๐
๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐
๐๐๐๐๐; ๐๐
๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐. ๐ท๐๐๐๐๐ ๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐
๐ ๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐ ๐๐ ๐
๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐; ๐๐๐๐ ๐จ๐๐๐๐ ๐๐๐๐ ๐๐
๐๐๐๐ ๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐. ๐ฒ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐-๐๐๐๐๐๐ ๐ผ๐๐๐๐ ๐๐๐๐, ๐๐
๐๐๐ ๐๐๐ ๐๐
๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐." (Luka 12:29-31). Eya! Mukukamba za kukhazikitsa Chikhulupiriro changwiro changati cha ana m'mitima ya nkhosa zake! Iye amakhumba atamasamalira nkhosazo yekha mu china chirichonse osati izozi zidzizisamalira zokha, ayi. Kodi m'mayesa ndi Iye amazitsogolera ku msipu wobiriwira, osati pazokha?
โ
โPopitiriza nkhaniyi, talingalirani kagulu kochepa ka nkhosa kupezeka malo amodzi ndi gulu lochuruka la mimbulu yolusa, izozi nkumazitetezera zokha zikamalumidwa ndi adaniwo! Kodi zingakwaniritse kutero popanda M'busa wawo? Nzosatheka popeza izozi zilibe chitetezero pazokha. Ndipo nzosadabwitsanso kuti Ambuye amafuna kagulu ka nkhosa zawozo kadzikhala ndi makhalidwe aumulungu otsatirawa pakati pa mimbuluyi. " ๐๐๐๐ ๐ฐ๐๐ ๐๐
๐๐๐๐๐ ๐๐๐ ๐๐๐, ๐ฒ๐๐๐
๐๐๐๐๐ ๐๐๐ ๐๐
๐๐๐ ๐๐๐, ๐๐
๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐;" (Mateyu 5:44)
โ
โDziwani kuti Yesu Khristu anawaphunzitsa Ophunzira ake kamenyedwe ka nkhondo kauzimu; pomwe ankawatumiza kukalimbana ndi ziwanda. Anawapatsa Iwo mphamvu yotsutsana ndi mizimu yoyipa osati anthu anzawo ayi. Kutulutsa ziwanda mwa anthuwo; kuchiza matenda ndi madwale onse odzera mu mizimu yoyipa mwa anthuwo. Ndipo monga Iye mwini sadagwiritsepo ntchito Mphamvu yake pa munthu aliyense kupatula pa ziwanda mu Utumiki wake onse nkubwera kwake koyamba padziko, popeza sadabwere kudzaononga koma kudzapulumutsa anthu; adagawiranso uphungu wa kamenyedwe ka nkhondo koteroko kwa Ophunzira akewo. (๐ ๐ฎ๐๐ฒ๐๐ 10:1)
โ
โKotero, kagulu ka nkhosa ka M'busa Yesu Khristu sikaloredwa kugwiritsa ntchito zipolopolo zauzimu zenizeni mu mfuti zawo ndi kuombera adani awo poyesera kuzitetezera kwa mimbulu; koposa kutulutsa ziwanda zomwe zikugwiritsidwa ntchito mwa adaniwo potsutsana nawo. Awa anali ndipo ndi maganizidwe a M'busa Wabwino pa adani ake onse ngakhalenso adani a nkhosa zake.
โ
โKunalembedwa: "๐ซ๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐; ๐
๐๐๐๐๐๐๐๐, ๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐.... ๐ด๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐
๐ ๐๐๐๐๐. ๐ฎ๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐. ๐ต๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐, ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐, ๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐
๐ ๐๐๐๐๐
๐๐๐ ๐๐
๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐. ๐ด๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐, ๐๐๐๐๐
๐๐
๐๐, ๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐; ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐
๐๐, ๐ฒ๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐, ๐ฐ๐๐ ๐๐
๐๐
๐๐๐๐๐๐๐๐๐, ๐๐๐ ๐จ๐๐๐๐๐. ๐ฒ๐๐๐ ๐๐๐๐๐ ๐๐
๐๐๐ ๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐, ๐๐๐
๐๐๐๐๐, ๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐
๐๐, ๐๐๐๐๐๐๐๐; ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐
๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐ ๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐. ๐ด๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐ ๐๐๐๐๐, ๐๐๐๐ ๐๐
๐ ๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐๐๐๐๐๐ ๐๐๐๐๐." (Aroma 12:14,17-21)
โ
โKotero ngati kubwezera ndi kwa Ambuye osati kwa nkhosazo, zikutanthauza kuti nkhosa zomwe Mbusa Wabwino amazitsogolera ku madambo a nsipu wobiriwira komwenso kuli mimbulu yolusa kudzera mu chitsogozo cha Mzimu Woyera, ziribe ulamuliro pazokha wobwezera adani pa zoipa zonse amazichitira. Izi zikutanthauzanso kuti sikhalidwe la Akhristu Okhulupirira enieni kubweza choyipa ku choyipa kwa adani awo; ngakhale awachimwire mwa mtundu wanji.
โ
โNdithudi, ndi kusowa khalidwe la Chikhristu chenicheni kwa Okhulupirira Yesu Khristu, kubwezera choyipa ku choyipanso; kutemberera adani, kupempherera moto wonyeketsa kuti utsikire pa Iwo awonongedwe; (๐๐ช๐ ๐ 9: 51-56); kupempherera adani kuti zida zomwe anakutumizira ziwabwerere ndi kuwaononga eni ake; ngakhalenso kuwalingalira zoipa adaniwo kuti ziwachitikire m'miyoyo yawo; pokhapokha ngati utalamulidwa ndi Mzimu Woyera kuti utero. Dziwani kuti M'busa Wabwinoyutu amapindula koposa muuzimu pomwe kagulu kake ka nkhosa kakukumana ndi mimbulu mdambo; monga momwe Atate Wakumwamba amapindulanso ndi Satana pomulola kumawachitira zoipa ana Ake osankhidwa.
โ
โZikomo.
โ
โ๐ ๐๐๐บ๐๐ถ ๐๐ผ๐ต๐ป ๐ ๐ป๐ฒ๐น๐ฒ๐บ๐ฏ๐ฎ
โ๐ญ๐ผ๐ฒ ๐๐ฎ๐ฟ๐๐ฒ๐๐ ๐ ๐ถ๐ป๐ถ๐๐๐ฟ๐ถ๐ฒ๐
โ+265881199062
โ+265888867202.
โ