26/05/2016
Mwadzuka bwanji abale mwa Ambuye. Tiyeni tikhale ndi mtima wachikondi pa munthu wina ndi mzake posatengera kaonekedwe ka khungu, zikhulupiliro komanso mbali yomwe wina achokera, mwaichi tiyeni tisaphe anzathu awa achi alubino. Mmodzi mwa mkhristu wathu yemwe analinso wachi alubino yemwenso amayimba kwaya ya ulaliki, waphedwa ndi anthu pazifukwa ndi zikhulupiro za kumidima, tiyeni tiwayikize mmapemphero a ku banja kwa malemu Fletcher Masina panyengo yowawitsayi.