Namilango Seventh-day Adventist Church

Namilango Seventh-day Adventist Church Namilango Seventh-day Adventist Church is situated in Machinjiri township in the city of Blantyre. Currently with membership of 1300 members. Visit us

29/08/2026

Kupetedwa ndi Kusefedwa Masiku Otsiriza || 29 August 2026

29/08/2026

Sabbath Worship || 26 August 2026
Preacher: Evengelist Biliati

29/08/2026

Sabbath Worship | Come To Jesus | Elder Ganett

29/08/2026
22/08/2026

Gogo Ganiza (Jane Kumbani Ganiza) Funeral | 22 August 2026

22/08/2026

Khalidwe Likalalike | Through it all Music Group

22/08/2026

Hossana kwa Yesu | Mthawira AY

22/08/2026

Sabbath Worship

22/08/2026

*PHUNZIRO #08 LA KOTALE MWACHIDULE KWAMBIRI*

*15th-21st AUGUST, 2026.*

_*"PAMENE YESU ANAUKA KWA AKUFA"*_

*VESI LOLOWEZA: 1 AKORINTO 15:14-17*

_*"Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwa kulalikira kwathu kuli chabe. Chikhulupiriro chanunso chili chabe. Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; chifukwa tinachita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Khristu; amene sanamuukitsa, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa. Pakuti ngati akufa saukitsidwa, Khristunso sanaukitsidwa; ndipo ngati Khristu sanaukitsidwa, chikhulupiriro chathu chili chopanda pake; muli chikhalire m'machimo anu"*_

👉🏽Mu nthawi ya Paulo anthu ena sankakhulupirira za mdzukiro.
👉🏽 Mdzukiro ndi nthawi imene akufa adzaukitsidwa pakubweranso kwachiwiri kwa Yesu Khristu
👉🏽Paulo akufuna timvetsetse choonadi cha mdzukiro
👉🏽Sabata ino tiwunikira _1 Akorinto 15_ ndi Chiphunzitso cha mdzukiro

*SUNDAY - TSIKU LOYAMBA:*

_*"KULENGEZA MDZUKIRO WA YESU"*_

*1 AKORINTO 15:1-4*

👉🏽Paulo akuyamba _1 Akorinto 15_ ndi Uthenga Wabwino
👉🏽Wakuti Yesu amatipulumutsa ku machimo
👉🏽Paulo analalikira uthenga wabwinowu kwa Akorinto
👉🏽Ndipo anthuwo anakhulupirira uthengawo
👉🏽Tsopano anayenera kugwiritsa ntchito uthengawo
👉🏽Zikatero Mulungu adzawapulumutsa _(1 Akorinto 15:1,2)_
👉🏽 Mdzukiro wa Yesu ndi gawo lofunikira kwambiri la Uthenga Wabwino
👉🏽 Paulo akuti Yesu anafera zoipa zathu monga mwa malembo _(1 Akorinto 15:3)_
👉🏽Imfa ndi mdzukiro wa Yesu zimakwaniritsa malonjezo a Mulungu a Chipangano Chakale
👉🏽_1 Akorinto 15:5-8_ akutipatsa umboni wa mu Baibulo wakuti anthu ambiri anamuona Yesu atauka kwa akufa
👉🏽Anthu amenewa Yesu akuwatchula kuti ndi _*"MBONI ZA IZI"*_ _(Luka 24:48)_

*MONDAY - TSIKU LACHIWIRI:*

_*"CHIYEMBEKEZO CHATHU CHOKHACHO"*_

*1 AKORINTO 15:9-19*

👉🏽Mu _1 Akorinto 15:9-19_ Paulo akunena chifukwa chimene sitiyenera kukana mdzukiro wa Yesu
👉🏽Popanda mdzukiro tilibe chiyembekezo
👉🏽 Amitundu ambiri kalelo sankakhulupirira za mdzukiro
👉🏽 Ndipo Paulo sankawamvetsetsa anthu okayikira mdzukirowa
👉🏽Ngati kulibe mdzukiro, Paulo ndiyetu akuti;
🔨Yesu sanauke kwa akufa
🔨 kulalikira kwathu kuli chabe
🔨 Chikhulupiriro chathu ndi chopanda pake/chopanda ntchito
🔨Ndife mboni zonama
🔨Machimo athu sanakhululukidwe
🔨Akufa adakagonabe m'manda ndipo anataika

*TUESDAY - TSIKU LACHITATU:*

_*"KHRISTU ADALI CHIPATSO CHOUNDUKULA"*_

*1 AKORINTO 15:20-23*

👉🏽 Mdzukiro wa Yesu ndi woonadi
👉🏽Choncho tikhonza kutsimikiza kuti aliyense amene anafa ali mwa Yesu.........
👉🏽.......adzaukitsidwa pakubweranso kwachiwiri kwa Yesu Khristu
👉🏽Mu _1 Akorinto 15:20-23_ Yesu akutchulidwa *'Chipatso Choundukula'*
👉🏽Chifukwa chakuti Iye ali umboni kuti akufa mwa Yesu adzaukitsidwa pakubweranso kwake kwachiwiri
👉🏽Yesu adzabwezera Ufumu kwa Mulungu Atate
👉🏽Dziko lapansi lidzayambanso kulamulilidwa ndi Mulungu _(1 Akorinto 15:25-28)_
👉🏽Yesu adzadziyika yekha pansi pa ulamuliro wa Mulungu Atate _(1 Akorinto 15:28)_
👉🏽Kuti timvetsetse izi, yerekezani Yesu ndi Adam
👉🏽Yesu adakhala Adamu wachiwiriyo pofuna kupulumutsa ife ku uchimo
👉🏽Iye adzadzipereka kutumikira Atate zinthu zimene Adamu oyambayo sanachite.

*WEDNESDAY - TSIKU LACHINAYI:*

_*"THUPI LATSOPANO"*_

*1 AKORINTO 15:36-41*

👉🏽Mu ndime iyi👆🏽, Paulo akufotokoza mwachidule za thupi lowukitsidwa
👉🏽Paulo akuyamba uthenga wake waufupi ndi mafunso awiri _(1 Akorinto 15:35):_
🔨1.Akufa aukitsidwa bwanji?
🔨2.Ndipo adza nalo thupi lotani?

👉🏽Mafunsowa akuyankhidwa mu _1 Akorinto 15:36-40_
👉🏽Thupi loukitsidwa ndi limene Yesu adzatipatse tikadzaukitsidwa kwa akufa
👉🏽Paulo wagwiritsa ntchito zitsanzo zitatu pofotokoza zimene zidzachitike pa mdzukiro;

1. Paulo akuyerekeza thupi ndi mbewu
👉🏽Mbewu ikadzalidwa imayenera kufa isanamere
👉🏽 kusintha kumeneku ndi chozizwa cha Mulungu

2. Paulo akufotokoza za mmene Mulungu amaperekera matupi osiyanasiyana kwa anthu ndi nyama

👉🏽Awa ndi matupi amene tikukhala nawo panowa.
👉🏽mu njira yomweyo Mulungu adzatipatsa matupi atsopano kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano

3. Paulo akufotokoza za matupi amene tidzakhale nawo tikadzauka kwa akufa _(1 Akorinto 15:40-42)_

👉🏽Paulo akuti tidzakhala ndi matupi a ulemerero

*THURSDAY - TSIKU LACHISANU:*

_*"CHIGONJETSO CHATHU CHOTSIRIZA KUGONJETSA IMFA"*_

*1 AKORINTO 15:54-57*

👉🏽Mu _1 Akorinto 15:50_ Paulo akubwera ndi Chiphunzitso chachilendo
👉🏽 _*"koma ndinena ichi abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu........"*_
👉🏽Akhristu ambiri amaganiza kuti Paulo akuti kumwamba tidzakhala anthu opanda matupi
👉🏽Komatu Paulo sakuphunzitsa choncho
👉🏽Mu _1 Akorinto 15:42-49_ Paulo akuyerekeza matupi omwe tili nawowa
👉🏽Ndi matupi amene adzaukitsidwe
👉🏽Matupi omwe tili nawowa anaonongedwa ndi uchimo komanso amafa
👉🏽Koma thupi loukitsidwa lidzakhala lopanda uchimo
👉🏽Komanso lidzakhala lamuyaya _(1 Akorinto 15:50)_
👉🏽Paulo wagwiritsa ntchito mawu oti, _*"thupi ndi mwazi"*_
👉🏽kutanthauza matupi amene tili nawo panowa
👉🏽Ndi chifukwa chake ayenera kusinthidwa mkamphindi pakubweranso kwachiwiri kwa Yesu Khristu

*FRIDAY - TSIKU LA CHISANU NDI CHIMODZI:*

_*"KUOMBA NKOTA"*_

🔨Ambiri mwa anthu a Mulungu anamwalira pamene matupi awo anali odwala
🔨Koma pa nthawi ya mdzukiro adzaukitsidwa Ndi matupi a thanzi Ndi a mphamvu zamuyaya.

*A M E N 🙏*

_Tikukufunirani nonse Sabata lopambana lodzadza ndi madalitso ochokera kwa Yehova Mulungu wakumwamba._

_Ndife abale anu ndi mlongo wanu mwa Khristu Yesu Ambuye wathu;_

*SSLS TEAM:*

*Jimmy HB Njiragoma Phiri*
_+265 888 611 266_

*Hudson Nkumbira Gama*
_+265 888 481 718_

*Mrs Edina Kholowa*
_+258 841 102 715_

*Donald Katete*
_+265 888 598 149_

Address

Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Namilango Seventh-day Adventist Church posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share