Blantyre-Chiradzulu Zone Adventist Youth Ministries

Blantyre-Chiradzulu Zone Adventist Youth Ministries This is the official page for Blantyre-Chiradzulu Zone Adventist Youth Ministries of Eastern Malawi Conference Adventist Youth Ministries

๐— ๐—Ÿ๐—˜๐—ก๐——๐—ข ๐—”๐— ๐—˜๐—ก๐—˜ ๐—”๐—ž๐—จ๐—ž๐—”๐—ง๐—จ๐— ๐—œ๐—ž๐—œ๐—ฅ๐—” ๐—ž๐—จ ๐—ฃ๐—”๐—ง๐—›๐—™๐—œ๐—ก๐——๐—˜๐—ฅ ๐—–๐—”๐— ๐—ฃ๐—ข๐—ฅ๐—˜๐—˜ ๐—ช๐—”๐—™๐—œ๐—ž๐—”Mlendo amene akuKatumikira ku Pathfinder Camporee yoyamba ya Eas...
17/08/2026

๐— ๐—Ÿ๐—˜๐—ก๐——๐—ข ๐—”๐— ๐—˜๐—ก๐—˜ ๐—”๐—ž๐—จ๐—ž๐—”๐—ง๐—จ๐— ๐—œ๐—ž๐—œ๐—ฅ๐—” ๐—ž๐—จ ๐—ฃ๐—”๐—ง๐—›๐—™๐—œ๐—ก๐——๐—˜๐—ฅ ๐—–๐—”๐— ๐—ฃ๐—ข๐—ฅ๐—˜๐—˜ ๐—ช๐—”๐—™๐—œ๐—ž๐—”

Mlendo amene akuKatumikira ku Pathfinder Camporee yoyamba ya Eastern Malawi Conference wafika mdziko muno. M'busa Bongani Ndlobvu wochokera ku Zimbabwe West Union Conference amene ndi President wa Conference-yi wafika lero kudzera pa Bakili Muluzi International Airport ku Chileka, mu mzinda wa Blantyre.

Wapampando wa achinyamata mu Malawi Union Conference Master Guide Vitumbiko Chijere Chirwa komanso atsogoleri ena a Pathfinder ndi omwe anakachingamira mlendoyu pa bwalo la ndegeli. M'busa Ndlobvu akhala mlaliki ku Camporee yonse.

Eastern Malawi Conference Pathfinder Camporee yayamba dzulo pa 16 August 2026 ndipo itha pa *22 August 2026 ku Mlangeni Campsite, Mangochi. Achinyamata oposa 500 ochokera m'madera osiyanasiyana asonkhana kuti aphunzire za uzimu, luso, ndi umodzi pansi pa mutu wakuti โ€œSTAND STRONGโ€.

Atsogoleri ati kufika kwa mlendoyu ndi chizindikiro chakuti Mulungu ali ndi dongosolo lalikulu la mibadwo yachinyamata mu Conference ino. Ma Pathfinder akuyembekezeka kupindula kwambiri ndi maulaliki, masewero olimbitsa thupi, ndi maphunziro omwe akonzedwa sabata yonseyi.

Muchithunzomo, Master Guide Ndlobvu ndi omwe avala sumumba omwe komanso buluku la khaki.

Abusa ambiri kuphatikizapo mtsogoleri wa Eastern Malawi Conference m'busa Master Guide Dr Sanned Lubani ali kuno ku Mangochi.

Wolemba : McAllan Mapinda
EMC Media

Adventurers min camp in progress at Maranatha girls Academy ๐Ÿ’ฅ
31/07/2026

Adventurers min camp in progress at Maranatha girls Academy ๐Ÿ’ฅ

Amen
29/07/2026

Amen

29/07/2026

๐— ๐—” ๐—”๐——๐—ฉ๐—˜๐—ก๐—ง๐—จ๐—ฅ๐—˜๐—ฅ 31 ๐—”๐—ก๐—ฌ๐—”๐— ๐—จ๐—ž๐—” ๐—ž๐—จ๐—ฃ๐—œ๐—ง๐—” ๐—ž๐—จ ๐—–๐—”๐— ๐—ฃ ๐—ฌ๐—” ๐—•๐—Ÿ๐—”๐—ก๐—ง๐—ฌ๐—ฅ๐—˜-๐—–๐—›๐—œ๐—ฅ๐—”๐——๐—ญ๐—จ๐—Ÿ๐—จ ๐—ญ๐—ข๐—ก๐—˜

Gulu la achinyamata a zaka za 4 mpaka 9 odziwika kuti Ma Adventurer mu bungwe la Adventist Youth Ministries ochokera pa Lisanjala, okwana 31, lero anyamuka ulendo wopita ku Camp ya Blantyre-Chiradzulu Zone ya ma Adventurer.

Camp-yi ikuchitikira ku Maranatha Girls Academy ku Machinjiri komwe achinyamatawa akaphunzire zinthu zosiyanasiyana kuphatikizapo masewero olimbitsa thupi, maulaliki ndi nyimbo mwazina.

Mโ€™busa amene akukatumikira kumeneko ndi Master Guide Orlac Mozalande wachigawo chathu cha Malabvi.

Ma Adventurer akuwoneka okondwa kwambiri pamene akunyamuka. Ena ali ndi zikwama zawo, ena akuyimba, ndipo onse ali ndi chisangalalo chofuna kuphunzira zinthu zatsopano.

Mโ€™modzi mwa atsogoleri awo Master Guide Dorothy Njunga wati ali ndi chiyembekezo kuti achinyamatawa akapindula mu uzimu komanso maphunziro ena okhudza thanzi lawo.

โ€œCholinga chathu ndi kuwaphunzitsa ana awa kukhala otsatira a Yesu, kukhala athanzi, okondwa, komanso othandiza mโ€™mudzi,โ€ adatero Master Guide Njunga.

Atsogoleri ena ndi Master Guide Mwadaine Mwaziwa, Master Guide Alice Mbendera komanso Master Guide Ernest Jumbe omwe akuperekeza achinyamatawa.

Camp iyi ikuyamba lero pa 29 July ndipo ikuyembekezeka kufika pachimake la Sabata pa 1 August kenaka kutseka pa 2 August 2026.

Wolemba : McAllan Mapinda
Lisanjala Media

Tsiku lotseka kulipira lina ndi lero. Tayesetsani kuti musaphonye zabwinozi.
20/07/2026

Tsiku lotseka kulipira lina ndi lero. Tayesetsani kuti musaphonye zabwinozi.

๐—•๐—Ÿ๐—”๐—ก๐—ง๐—ฌ๐—ฅ๐—˜-๐—–๐—›๐—œ๐—ฅ๐—”๐——๐—ญ๐—จ๐—Ÿ๐—จ ๐—ญ๐—ข๐—ก๐—˜ ๐—ฌ๐—”๐—ž๐—ข๐—ก๐—ญ๐—” ๐—–๐—”๐— ๐—ฃ ๐—ฌ๐—” ๐— ๐—” ๐—”๐——๐—ฉ๐—˜๐—ก๐—ง๐—จ๐—ฅ๐—˜๐—ฅ๐—ฆ ๐—ฌ๐—” ๐Ÿฎ๐Ÿฌ๐Ÿฎ๐ŸฒBungwe la achinyamata la Adventist Youth Ministries mu Bl...
19/07/2026

๐—•๐—Ÿ๐—”๐—ก๐—ง๐—ฌ๐—ฅ๐—˜-๐—–๐—›๐—œ๐—ฅ๐—”๐——๐—ญ๐—จ๐—Ÿ๐—จ ๐—ญ๐—ข๐—ก๐—˜ ๐—ฌ๐—”๐—ž๐—ข๐—ก๐—ญ๐—” ๐—–๐—”๐— ๐—ฃ ๐—ฌ๐—” ๐— ๐—” ๐—”๐——๐—ฉ๐—˜๐—ก๐—ง๐—จ๐—ฅ๐—˜๐—ฅ๐—ฆ ๐—ฌ๐—” ๐Ÿฎ๐Ÿฌ๐Ÿฎ๐Ÿฒ

Bungwe la achinyamata la Adventist Youth Ministries mu Blantyre-Chiradzulu Zone mu Eastern Malawi Conference, yakonza Camp ya ma Adventurer yomwe ikuyembekezeka kukopa ana ambiri ochokera mโ€™mipingo yosiyanasiyana mderali.

Camp iyi idzachitika kuyambira pa 29 July mpaka 2 August 2026 ku Maranatha Girls Academy ku Area 6, Machinjiri, munzinda wa Blantyre.

Pansi pa mutu woti โ€œLittle Hearts, Big Missionโ€ _Mitima Yaingโ€™ono, Utumiki Waikulu_, ana adzaphunzitsidwa kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso mtima wothandiza ena.

Malinga ndi EMC m'busa Master Guide Orlac Mozalande yemwe ndi Patron wa AYM mu Blantyre-Chiradzulu Zone wasankhidwa kukhala m'busa wa camp iyi. Iye azatsogolera maphunziro a mโ€™Baibulo, mapemphero komanso kulimbikitsa ana pa ntchito ya Mulungu.

Ana adzasangalala ndi zochitika zosiyanasiyana monga nyimbo, masewero a mpira ndi basketball, komanso masewero ena.
Kuphatikiza apo padzakhala maphunziro a ma award okhudza ukhondo, zakudya zopatsa thanzi, makhalidwe abwino, komanso thanzi ndi masewero olimbitsa thupi.

Mtengo wolembetsera ndi K20,000.00 ndipo tsiku lomaliza ndi 27 July, 2026.

Ofuna kulipira m***a kuteri pa Mpamba 0889920691 kapena Airtel Money 0997542928 dzina lake _Tionge Kanyimbo_. Angathenso kulipira ku Bank ya FDH, Account Name: _Blantyre Chiradzulo Zone Adventist Youth Ministries_, Account No: 1910100045427.

Kwa mafunso ena, anthu atha kulumikizana ndi 0999397281.

Akuluakulu alimbikitsa makolo kutumiza ana awo ku camp iyi kuti akule mthupi, mโ€™maganizo komanso mu uzimu.

Olemba: McAllan Mapinda
EMC

๐— ๐—Ÿ๐—˜๐—ก๐——๐—ข ๐—ช๐—”๐—ฃ๐—”๐——๐—˜๐—ฅ๐—” ๐—ข๐——๐—ญ๐—”๐—ง๐—จ๐— ๐—œ๐—ž๐—œ๐—ฅ๐—” ๐—ž๐—จ ๐—–๐—”๐— ๐—ฃ๐—ข๐—ฅ๐—˜๐—˜ ๐—ช๐—”๐——๐—ญ๐—œ๐—ช๐—œ๐—ž๐—”Bungwe la achinyamata la Adventist Youth Ministries mu Eastern Malawi ...
07/07/2026

๐— ๐—Ÿ๐—˜๐—ก๐——๐—ข ๐—ช๐—”๐—ฃ๐—”๐——๐—˜๐—ฅ๐—” ๐—ข๐——๐—ญ๐—”๐—ง๐—จ๐— ๐—œ๐—ž๐—œ๐—ฅ๐—” ๐—ž๐—จ ๐—–๐—”๐— ๐—ฃ๐—ข๐—ฅ๐—˜๐—˜ ๐—ช๐—”๐——๐—ญ๐—œ๐—ช๐—œ๐—ž๐—”

Bungwe la achinyamata la Adventist Youth Ministries mu Eastern Malawi Conference ya Mpingo wa Seventh-day Adventist pomwe likupitilira kukonzekera za Camporee yoyamba ya ma Pathfinder yomwe ikhalepo kuyambira pa 16 mpaka pa 22 August 2026 ku Mlangeni Campsite ku Mangochi lalengeza za mlendo wapadera amene azakhale akutumikira.

Msasa wa sabata umodziwu ukuyembekezeka kusonkhanitsa mazana a ma Pathfinder ochokera mโ€™dziko muno ndi mayiko ena kuti adzakule mโ€™chikhulupiriro, aphunzire luso losiyanasiyana, kupembedza pamodzi ndi kukhala pa umodzi. Malinga ndi otsogolera, cholinga cha msonkhanowu ndi kulimbikitsa chikhulupiriro, makhalidwe abwino komanso utsogoleri mwa achinyamata.

M'busa Bongani Ndlobvu ochokera ku Zimbabwe West Union Conference ndi amene wasankhidwa kukhala mlendo wapadera amene azizapereka mauthenga kwa otenga nawo mbali pa sabata yonseyi maka ma Pathfinder ndi atsogoleri awo.

Bungwe la Youth Ministries ku Eastern Malawi Conference lati kulembetsa kukupitilirabe mpaka pa 20 July 2026. Otenga nawo mbali ochokera mโ€™dziko muno akulipira MK120,000.00 pa munthu aliyense, pomwe alendo ochokera kunja akulipira $80.00. Tsiku lomaliza lolembetsa ndi pa 20 July, 2026 ndipo malo aziperekedwa kwa amene wachita changu..

Atsogoleri a Conference ati Camporee iyi ndi mbiri yatsopano kwa EMC ndipo ndi njira imodzi yothandizira ma Pathfinder kuti aime molimba mโ€™chikhulupiriro chawo mโ€™nyengo zovutazi.

Kuti mudziwe zambiri, omwe ali ndi chidwi atha kulumikizana ndi +265 888 750 188 / +265 999 229 151 kapena kuchezera www.emcyouthministries.com.

Olemba : McAllan Mapinda
EMC Media

Tumizani Chipepeso Chanu kwa atsogoleri athu Master Guide Martha Yesaya pa 0881 53 46 96
02/07/2026

Tumizani Chipepeso Chanu kwa atsogoleri athu Master Guide Martha Yesaya pa 0881 53 46 96

Condolence Message
02/07/2026

Condolence Message

๐—ฃ๐—ฅ๐—ข๐—š๐—ฅ๐—”๐—  ๐—ฌ๐—” ๐— ๐—”๐—Ÿ๐—œ๐—ฅ๐—ข ๐—” ๐—ฃ๐—”๐—ฆ๐—ง๐—ข๐—ฅ ๐—ฌ๐—ข๐—Ÿ๐—ข๐—ฆ ๐—ก๐—ž๐—จ๐—ญ๐—œ๐—ข๐—ก๐—”Lero pa 2 July 2026 nthawi ya 10:00am kuchoka ku siwa ku Chileka kupita ku nyum...
02/07/2026

๐—ฃ๐—ฅ๐—ข๐—š๐—ฅ๐—”๐—  ๐—ฌ๐—” ๐— ๐—”๐—Ÿ๐—œ๐—ฅ๐—ข ๐—” ๐—ฃ๐—”๐—ฆ๐—ง๐—ข๐—ฅ ๐—ฌ๐—ข๐—Ÿ๐—ข๐—ฆ ๐—ก๐—ž๐—จ๐—ญ๐—œ๐—ข๐—ก๐—”

Lero pa 2 July 2026 nthawi ya 10:00am kuchoka ku siwa ku Chileka kupita ku nyumba ya chisoni ya Taprama ku green corner komwe kukachitikile mwambo wonse wamaliro kuyambira 11:30am mmawa asananyamuke kupita ku Zalewa.

Malirowa aikidwa mawa Friday pa 03 July 2026 ku Zalewa.

Directions/Mayendedwe aku Zalewa ali motere:

Mukafika pa Zalewa mukatenga nseu opita ku Lilongwe mukafika pa mudzi wa Kandoje ndipafupi ndi school ya Kadasana primary. Tiyeni tonse tikhale nawo shepherdess Nkuziona ndi banja lonse munyengo yovutayi komaso tiwakumbukile mmapemphero.

Pomwe amasitiya dzulo pa 1 July 2026 nkuti ali mtsogoleri wa achinyanata komanso zamaphunziro nchigawo cha South East Malawi Conference.

Iwowa atisiya madzidzi.

Olemba : McAllan Mapinda
EMC Media

Address

Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Blantyre-Chiradzulu Zone Adventist Youth Ministries posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share