19/08/2026
FAMILY DAY!
Loweruka lapitali pa 15 August 2026 bungwe la mabanja achikhristu la CFM pa St Pius X Parish linali ndi macheza (Mass and Get Together)
Mwambowu unayamba ndi Misa nthawi ya 2 koloko masana kenaka kunali kucheza, kukhwasula nyama ndi kumwelera limodzi mpaka madzulo.
Anatsogolera nsembe ya Misa ndi Bambo Mfumu wapa parish Fr Peter Kantembe. Kunalinso mwambo wa keke (cake) komanso kupereka ma certificate ku mabanja eight omwe akwanisa zaka zochuluka akukhala limodzi motere:
Isaac ndi Martha Nyalugwe analandira certificate ya zaka 10.
Sebastian ndi Rebecca Chinkhandwe 15 years.
Gerald ndi Clara Macheso 20 years.
Joshua ndi Danile Chirwa 20 years.
Emmanuel ndi Maganizo Chizinga 25 years.
Marcel ndi Agnes Lukhere 25 years.
Sebastian ndi Herederitta Chimthiko 40 years.
Denis ndi Mercy Lukhere 45 years.
Mu Mau awo, wachiwiri kwa chair couple wa St Pius CFM Dumisani ndi Emuly Lindani anathokoza Bambo Mfumu ndi mabanja onse potengapo mbali pazochitika zonse za tsikuli.
Mwambo woterewu umene chaka chino unachitikira ku Aula Magna, umachitika chaka ndi chaka pa St Pius Parish.
St Pius X Parish Media Team