09/01/2026
KUFUNIKIRA KWA MAPEPHERO A UTSIKU
Mateyu 25:1-10 (bukhu lopatulika)
Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, natuluka kukakomana ndi mkwati. 2Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera. 3Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengeranso mafuta; 4koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao. 5Ndipo pamene mkwati anachedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo. 6Koma pakati pa usiku panali kufuula, Onani, mkwati! Tulukani kukakomana naye. 7Pomwepo anauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zao. 8Ndipo opusa anati kwa ochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu zilikuzima. 9Koma ochenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha. 10Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.
-Apapa tikuona kuti mkwati anafika pakati pa usiku, pakati pa usiku ndi pamene pamachitika zithu zambiri, Paulo ndi Sila ali mu ndende anapephera ndipo pakati pa usiku ndi pamene zitseko zinaseguka, ndipo maunyolo a mmanja ndi mmapazi anaduka.
Pakati pa usiku maunyolo amaduka, pakati pa usiku zitseko zimatha kutseguka kapena kukhala zotsekeka.
-Mu Mateyu 25:10 tikuona kuti anamwali khumi opusa aja ali kogula mafuta, chitseko chinasekeka ndipo sanakwanitse kulowa, chitseko choboleza chanu chitha kusekeka kapena kuseguka pakati pa usiku, anamwali khumi opusa chinasekeka, pomwe Paulo ndi Sila ali mu ndende pakati pa usiku chiseko chinaseguka,,, osati chinangoseguka chokha ai, koma anapephera ndi kuimba nyimbo zoyamika Mulungu.
-Inuyo pamene muli otanganidwa ndi kugona, otanganidwa ndikupita kogula mafuta ngati anamwali asanu opusa aja, chitseko chanu chimakhala chikusekedwa. Pomwe pamene mukhala mukupephera ndi kuimba nyimbo zoyamika Mulungu, chitseko chanu chimakhala chikuseguka....
-Anthu ambiri saziwa kufunika kodzuka utsika ndikupephera,, makamaka kumayambiriro a chaka, izizi zimathandiza kuti chiseko choboleza chanu chikhale chosegulidwa chaka chonse, mwezi uno wa Januwale ndi ofunika kwambiri chifukwa ndi mwezi oyamba,, ndi mwezi omwe timayenera kupatulira pamaso pa Mulungu...ndi kupephera ndi kutsala kudya. Ndi mwezi omwe timapuputha thupi lathu pamaso pa Mulungu.
-Ndi pephero ndi pembezero langa kuti chitseko chanu cha madalitso ndi kuboleza chikhale chotsegula chaka chonse chino cha 2026, zomwe mwakhala mukulephera kukwaniritsa mu 2025, mukwaniritsa mopweka kwambiri mu chaka chino cha 2026, chaka cha kudzoza kwatsopano, chaka chimene mulandire zithu zimene simunaganizepo...
-Chaka chimene mukalilira kwa Ambuye Yesu, azikuyankhani.
Ambuye Yesu akudalitseni nonse.
Amen