Chilobwe Assemblies Of God Christ Tabernacle

Chilobwe Assemblies Of God Christ Tabernacle Christ Tabernacle church exists to worship God and serve lives

10/08/2026

*VESI YOTSOGOLERA LERO 10 AUGUST 2026*
CHIVUMBULUTSO 14:13 Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti ntchito zao zitsatana nao pamodzi.

*Kumwalira uli mwa Ambuye ndiko kumwalira Ambuye Yesu ali mpulumutsi wamoyo wako. Ukamwalira uli mwa Ambuye umakapumula ku zolemetsa za moyo uno. Koma ukamwalira usali mwa Ambuye umakakumana ndi Gahena. Kumwalira usali mwa Ambuye ndiko kumwalira usanalape machimo ndi kulandira Yesu kukhala mpulumutsi wamoyo wako. Ndi chinthu choopsa kwambiri kumwalira usali mwa Ambuye. Lapani machimo anu zenizeni, landirani Yesu kukhala mpulumutsi wamoyo wanu. Kuti mutamwalira lero kapena tsiku lina lirironse muzakhale odala kuti mukapumule ku zolemetsa za moyo uno. “Lero ndi kulapa machimo anga onse, Ambuye Yesu ndikhululukireni. Ndipulumutseni Ambuye Yesu. Kuyambira lero mukhale mpulumutsi ndi Ambuye wamoyo wanga. Zikomo Yesu pondipulumutsa, Amen!” Mwapulumuka tsopano! Khalani mwa Yesu masiku onse amoyo wanu.*

Mukhale ndi Loremba Lopambana
*Bishop WJ Ching’amba 0884507838/0999201500 Chilobwe Assemblies Of God*

09/08/2026

*MAVESI OTSOGOLERA LERO 9 AUGUST 2026*
Chivumbulutso 20:12, 15 Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aangʼono omwe atayimirira patsogolo pa Mpando Waufumu ndipo mabuku anatsekulidwa. Buku lina linatsekulidwa limene linali Buku Lamoyo. Akufa anaweruzidwa monga mwa zimene anachita monga mmene zinalembedwera mʼmabuku. Ngati dzina la wina aliyense silinapezeke mʼBuku Lamoyo, anaponyedwa mʼnyanja yamoto.

*Imfa ilibe odi ndipo simaona nkhope, msinkhu, udindo, kapena chuma. Imfa ya munthu wina aliyense ndi yopweteka kwambiri. Koma kodi mutafa lero mukafikira kuti? Kodi dzina lanu munalembetsa m’buku la moyo osatha? Lapani machimo anu lero ndi kulandira Yesu kukhala mpulumutsi wamoyo wanu kuti dzina lanu lirembedwe m’buku la moyo osatha. Kuti mutafa lero kapena tsiku lina lirironse mukakhale ndi Mulungu Kumwamba. _“Ambuye Yesu ndipulumutseni ine ochimwa! Lowani mumtima mwanga, mukhale mpulumutsi ndi Ambuye wamoyo wanga. Chotsani dzina langa m’buku la imfa ndipo mulirembe m’bukhu la moyo osatha. Ndithandizeni kuyenda nanu masiku onse amoyo wanga. Zikomo Ambuye Yesu pondipulumutsa ndi kulemba dzina langa m’buku la moyo osatha. Amen!”_ Ngati mwapemphera kuchokera pansi pa mtima wanu, mwapulumuka ndipo dzina lanu lalembedwa m’buku la moyo. Lekani moyo wauchimo ndipo khalani moyo wachiyero nthawi zonse kuti dzina lanu lasachotsedwe m’buku la moyo.*

Mukhale ndi Lamulungu Lopambana
*Bishop WJ Ching’amba 0884507838/0999201500 Chilobwe Assemblies Of God*

live report from Ablaze TV
27/07/2026

live report from Ablaze TV

27/07/2026

in the last days through prayer

youth day 2026 Ablaze in the last days through prayer🔥
27/07/2026

youth day 2026
Ablaze in the last days through prayer🔥

23/07/2026

*VESI YOTSOGOLERA LERO 23 JULY 2026*
Yohane 14:27 Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.

*Mtendere wa mumtima ndi chinthu chofunika kwambiri chimene ndalama singakwanitse kugula, maphunziro, kutchuka, udindo sizingakwanitse kukupatsa. Ukakhala opanda mtendere wa mumtima china chilichonse m’moyo uno chimakhala chopanda phindu, chakudya sichikukomera, umalephera kugona pa chibedi cha wofuwofu. Mtendere wa mumtima ndi mphatso imene Ambuye Yesu amapereka kwa okhulupirira Iye amene amachita chifuniro chake. Ukakhala ndi mtendere wa mumtima umaganiza bwino, umakhala ndi chiyembekezo posatengera nyengo zimene ukudutsamo. Ukhonza kugona pa mwala ngati Yakobo koma ndi kumalota zakumwamba. Kulibe mtendere kwa yense okhala mu uchimo. Chincho lapani machimo anu zenizeni, landirani Yesu kukhala mpulumutsi wamoyo wanu ndipo yambani kuchita chifuniro chake. Ndipo muzakhala ndi mtendere wa mumtima posatengera nyengo zimene mukudutsamo. “Ambuye Yesu ndipulumutseni ine ochimwa! Mukhale mpulumutsi wamoyo wanga. Ndipatseni mtendere wa mumtima. Amen!” , mwezi wanga olandira chisomo chochuluka chokumana ndi zosowa zanga zonse #*

Mukhale ndi Lachinai Lopambana
*Bishop WJ Ching’amba 0884507838/0999201500 Chilobwe Assemblies Of God*

24/06/2026

*VESI YOTSOGOLERA LERO 24 JUNE 2026*
Masalimo 27:4 Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova, ichi ndi chimene ndidzachifunafuna: kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova, ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.

*Munthu amene nthawi zonse amakhala akuyang’ana ndi kulingalira za kukongola kwa Mulungu ndi kumafunafuna nkhope ya Mulungu amakhala odzala ndi chiyembekezo. Ndipo pang’ono pang’ono moyo wake, makhalidwe, machitidwe ndi mayankhulidwe ake zimayamba kuwonetsera kukongola kwa Mulungu. Chifukwa maso ako akamapenyetsetsa kukongola kwa Mulungu, mtima wako ukamafunafuna Mulungu, chimene Mulungu ali chimayamba kuwumbika mwayiweyo. Kulambira Mulungu zenizeni ndi kufunafuna Mulungu ndi mtima osweka ndi olapadi kumabweretsa kusinthika kwa makhalidwe, machitidwe ndi mayankhulidwe, komanso nyengo zako zimayamba kusintha. Chifukwa ndi zosagwira kumalambira ndi kumafunafuna nkhope ya Mulungu amene ndi okongola muzonse komabe iweyo ndi kumakhala moyo, makhalidwe, machitidwe ndi mayankhulidwe onyansa ofanana ndi Satana. Amene umamulambira, kumufunafuna ndi kumutumikira ndi amene umafanana naye. Inuyo mumalambira, kufunafuna ndi kutumikira ndani?*

Mukhale ndi Lachitatu Lopambana
*Bishop WJ Ching’amba 0999201500/0884507838 Chilobwe Assemblies Of God*

09/06/2026

*TODAY’S KEY VERSES 9 JUNE 2026*
John 14:13-14 And whatever you ask in My name, that I will do, that the Father may be glorified in the Son. If you ask anything in My name, I will do it.

*Don’t undermine the power of prayer. Prayer works because God answers prayer. Prayer permits God to do something for our needs. If you are not praying for your needs it means you are telling God that you don’t need His help. Because praying is to seek help from God. When a believer prays God works. Jacob prayed and God blessed him and changed his name. Jabez prayed and God answered him and by God’s help he became more honourable than his brothers. Daniel prayed and delivered him from hungry lions. The early believers prayed to God that apostle Peter should be released from prison and God answered them. Keep on praying and God is going to answer you. Have you prayed today? Remember to pray is to speak with God and permit Him to work on your needs. “I obtain grace to pray without ceasing. Amen!”*

Have a blessed Tuesday
*Bishop WJ Ching’amba 0884507838/0999201500 Chilobwe Assemblies Of God*

08/06/2026

*MAVESI OTSOGOLERA LERO 8 JUNE 2026*
2 Akorinto 8:1-3 Ndipo tsopano, abale, tikufuna kuti mudziwe za chisomo chimene Mulungu wapereka ku mipingo ya ku Makedoniya. Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri. Motero ndikuchitira umboni kuti anapereka mmene akanathera, ndipo mwinanso kuposera mmene akathera kupereka. Anapereka mosakakamizidwa.

*Kupereka molowamanja ndi khalidwe la Mzimu Woyera. Amapereka kwa okhulupirira zonse zofunika pa moyo wake wa uzimu, utumiki, banja, maphunziro, ntchito, bizinesi ndi tsogolo. Akhristu amene ndi odzadzidwa ndi otsogozedwa ndi Mzimu Woyera amapereka molowamanja monga momwe Mzimu Woyera amachitira. Akhristu amipingo ya ku Makedoniya ngakhale anali osauka koma anapereka molowamanja popanda kukakamizidwa chifukwa adali odzadzidwa ndi otsogozedwa ndi Mzimu Woyera. Khalani odzadzidwa ndi otsogozedwa ndi Mzimu Woyera ndipo simuzavutika kupereka molowamanja ndi kulipira zakhumi mokhulupirika posatengera nyengo zimene mukudutsamo.*

Mukhale ndi Loremba Lopambana
*Bishop WJ Ching’amba 0884507838/0999201500 Chilobwe Assemblies Of God*

Address

Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Chilobwe Assemblies Of God Christ Tabernacle posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share