17/03/2026
*ANTHU AKUFA*
Timamva Bwanji tikamva za imfa kapena anthu akufa?
*Chiyambi cha imfa;*
- Munda mwa Eden Mulungu anati Mtengo wapakati akaudya azafa ndithu.
*koma satana Malingana ndi Yohane 8:44 Tate wamaboza onse akuti* 📌[Gen 3:4] Kufa simuzafa ayi,[KUFA MUZAFA INDE KOMA OSATI KUFELATU]
*Munthu akafa amapita kuti?;*
- ena timati ali kumwamba,ena wasanduka mizimu,ena ali panjira yamoyo ndi imfa,
*Baibulo likuti 📌Masalimo 146:4,✔️Mlaliki 12:7 Mzimu umapita kwa Mulungu,Fumbi nkubwerela komwe lachokera*
*Kodi akufa amaziwa kuti afa?;*
- _Masalimo 115:17,Mlaliki 9:5,6 okufa saziwa kanthu Bi!,olo mutazichekacheka pa Maliro sangakumveni_
*Munthu okufa ndi Galu wokufa zonsezi nzofana;*📌_Mlalik 3:19_
*Kodi olungama akafa amapita kumwamba?;*
- _AYI 📌Machitidwe 2:29,34, olo Davide ali mmanda pano sikuti akudyerela kumwamba ayi, ndipo sikuti anakakumana ndi Mulungu,Mzimu okhawo unakasungidwa malo osungilako mizimu ya anthu,kufikila Lipenga losiriza mpamene azaone Mulungu_
*Kodi okufa amatha kuyankhula ndi amoyo?;*
- _AYI_
*_Munthu akafa saziwanso kanthu_*
*Nanga aja amatilotesa kuti tiaphikile sadaka aja ndindani?;*
- ZIWANDA, 📌1Sam 28:13-14 kapena kuti milungu,
*INUYO MUWELUZE KODI MILUNGU NDI CHANI?*
*Langizo kwa Akhristu;* _1 Timo 4:1 Masiku osiriza ena azaphunzisa zosiyana ndi zomwe zili baibulo_
*Kodi okufa angathe kupempheredwa kuti alape?;* _AYI_
_Paja tawerenga masalimo ndi mlaliki kuti_ *okufa salemekeza Mulungu ndipo saziwa kanthu* _ndipo a Heberi 9:27, kwaikika kwa munthu kufa kamodzi,kwinako nkumadikila chiweruzo_
*NB SUMMARY*;
BAIBULO LIKUTI
_THUPI(fumbi) + MPWEYA (mzimu)= *MUNTHU*_
_THUPI (fumbi) - MPWEYA (Mzimu)= *AMALEMU*_
(nkhan ikupitilila ku comment)